Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 29


Gawo 29

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith, Mneneri, pamaso pa akulu asanu ndi m’modzi, ku Fayette, New York, Seputembera 1830. Vumbulutso ili lidaperekedwa masiku angapo msonkhano waukulu usadachitike, kuyambira pa Seputembara 26, 1830.

1–8, Khristu amasonkhanitsa osankhidwa Ake; 9–11, Kubwera Kwake kudzabweletsa Zakachikwi; 12–13, Khumi ndi Awiri adzaweruza Israeli yense; 14–21, Zizindikiro, miliri, ndi zipululu zidzatsogolera Kudza Kwachiwiri; 22–28, Chiwukitso chotsiriza ndi chiweruzo chotsiriza zidzatsatira Zakachikwi; 29–35, Zinthu zonse ndi zauzimu kwa Ambuye; 36–39, Mdyerekezi ndi makamu ake adaponyedwa kuchokera kumwamba kuti adzayese munthu; 40–45, Kugwa ndi Chitetezero kumabweretsa chipulumutso; 46–50, Ana aang’ono ndi owomboledwa kudzera mu Chitetezero.

1 Mvetserani ku mawu a Yesu Khristu, Muwomboli wanu, Wamkulu Ine Ndine, amene mkono wake wachifundo udatetezera machimo anu;

2 Amene adzasonkhanitsa anthu ake ngakhale monga thadzi amasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, ngakhale onse amene ati adzamvere mawu anga ndi kudzichepetsa okha pamaso panga, ndi kuitanira pa ine mu pemphero lamphamvu.

3 Taonani, indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti pa nthawi ino machimo anu akhululukidwa kwa inu, kotero mulandira zinthu izi; koma kumbukirani kuti musachimwenso, kuopa kuti zowopsa zingabwere pa inu.

4 Indetu, ndinena kwa inu kuti mudasankhidwa kuchokera m’dziko lapansi kuti mulalikire uthenga wabwino wanga ndi mawu achisangalalo, ngati ndi mawu a lipenga.

5 Kwezani mitima yanu ndipo kondwerani, pakuti ine ndili pakati panu, ndipo ndine nkhoswe yanu ndi Atate; ndipo ndi chifuniro chake kuti akakupatseni ufumuwo.

6 Ndipo, monga kwalembedwa—Chilichonse chimene mudzapempha ndi chikhulupiliro, pokhala ogwirizana mupemphero molingana ndi lamulo langa, inu mudzalandira.

7 Ndipo inu mwayitanidwa kuchititsa kusonkhanitsa kwa osankhidwa anga; pakuti osankhidwa anga amamva mawu anga ndipo sawumitsa mitima yawo;

8 Kotero chilamulo chidapita kuchokera kwa Atate kuti iwo adzasonkhanitsidwa m’malo amodzi pamaso pa dziko lino, kukonza mitima yawo ndi kukonzekera m’zinthu zonse motsutsana ndi tsiku limene chisautso ndi chipasuko zidzatumizidwa pa oipa.

9 Pakuti ola layandikira, ndipo tsiku layandikira pamene dziko lacha; ndipo onse odzikuza ndi iwo akuchita zoipa adzakhala ngati chiputu; ndipo ndidzawatentha, atero Ambuye wa makamu; kuti kuipa sikudzakhala pa dziko lapansi;

10 Pakuti ola ili pafupi, ndipo chimene chidanenedwa ndi atumwi anga chikuyenera kukwaniritsidwa; pakuti monga iwo adanena chomwecho chidzachitidwa;

11 Pakuti ndidzadziulula ndekha kuchokera kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu, pamodzi ndi makamu onse, ndipo ndidzakhala muchilungamo pamodzi ndi anthu pa dziko lapansi kwa zaka chikwi, ndipo oipa sadzaima.

12 Ndiponso, indetu, indetu, ine ndinena kwa inu, ndipo ichi chapita mu lamulo lokhazikika, mwa chifuniro cha Atate, kuti atumwi anga, Khumi ndi Awiri amene adali ndi ine mu utumiki wanga ku Yerusalemu, adzaima pa dzanja langa lamanja pa tsiku la kudza kwanga mu lawi la moto, atavekedwa ndi miinjiro ya chilungamo, ndi nduwira pamitu yawo, mu ulemelero ngakhale ngatinso ine, kudzaweruza nyumba yonse ya Israeli, ngakhale onse amene adandikonda ine ndipo adasunga malamulo anga, ndipo palibe wina.

13 Pakuti lipenga lidzawomba onse utali ndi phokoso, inde monga pa Phiri la Sinai, ndipo dziko lonse lapansi lidzagwedezeka, ndipo iwo adzatulukira—inde, ngakhale akufa amene adafa mwa ine, kuti akalandire korona wa chilungamo, ndi kuti akavekedwe, ngakhale monga inenso, kukakhala ndi ine, kuti tikathe kukhala amodzi.

14 Koma, taonani, ndinena kwa inu, kuti lisadadze tsiku lalikulu ili, dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi udzasanduka mwazi, ndipo nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo padzakhala zizindikiro zazikulu m’mwamba ndi pa dziko lapansi;

15 Ndipo padzakhala kulira ndi kubuula pakati pa makamu a anthu;

16 Ndipo padzakhala mkuntho waukulu wa matalala wotumizidwa kukawononga mbewu za dziko lapansi.

17 Ndipo zidzachitika kuti, chifukwa cha kuipa kwa dziko, kuti ndidzabwezera chilango kwa oipa, pakuti sadzalapa; pakuti chikho cha ukali wanga chadzaza; pakuti taonani,mwazi wanga sudzawayeretsa ngati iwo sadzandimvera.

18 Kotero, ine Ambuye Mulungu ndidzatumiza ntchentche pa dziko lapansi, zimene zidzatera pa okhalamo, ndipo zidzadya mnofu wawo, ndipo zidzachititsa mphutsi pa iwo;

19 Ndipo malilime awo adzayimitsidwa kuti iwo asayankhule motsutsa ine; ndipo mnofu wawo udzagwa kuchoka m’mafupa awo, ndi maso awo kuchoka m’malo mwawo;

20 Ndipo zidzachitika kuti zilombo za kuthengo ndi mbalame za m’mlengalenga zidzawadya iwo.

21 Ndipo mpingo waukulu ndi wonyansa, umene uli wadama wa dziko lonse lapansi, udzagwetsedwa pansi ndi moto wonyeketsa, monga kudanenedwa m’kamwa mwa Ezekieli mneneri, amene adayankhula za zinthu izi, zimene sizidachitike, ndithu zikuyenera, pamene ine ndilipo, pakuti zonyansa sizidzalamulira.

22 Ndiponso, indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti pamene zaka chikwi zidzatha, ndipo anthu adzayambanso kukana Mulungu wawo, pamenepo ine ndidzalilekelera dziko lapansi koma kwa kanthawi kochepa;

23 Ndipo mapeto adzafika, ndipo kumwamba ndi dziko lapansi zidzapsa ndipo zidzapita, ndipo padzakhala kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.

24 Pakuti zinthu zonse zakale zidzapita, ndipo zinthu zonse zidzakhala zatsopano, ngakhale kumwamba ndi dziko lapansi, ndi chidzalo chake chonse, anthu ndi nyama, mbalame za mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja;

25 Ndipo tsitsi olo limodzi, kapena kachitsotso, sizidzatayika, pakuti ndi ntchito ya dzanja langa.

26 Koma, taonani, indetu ndinena kwa inu, dziko lapansi lisadapitilire, Mikaeli, mngelo wanga wamkulu, adzawomba lipenga lake, ndipo kenako akufa onse adzauka, pakuti manda awo adzatsegulidwa, ndipo adzatuluka—inde, ngakhale onse.

27 Ndipo olungama adzasonkhanitsidwa pa dzanja langa lamanja ku moyo wosatha; ndipo oipa pa dzanja langa lamanzere ndidzachita manyazi kukhala nawo pamaso pa Atate;

28 Kotero ndidzanena kwa iwo—Chokani kwa ine, otembeleredwa inu, pitani kumoto wosatha, wokolezedwera mdyerekezi ndi angelo ake.

29 Ndipo tsopano, taonani, ine ndinena kwa inu, pa nthawi iliyonse ine sindidalengeze konse kuchokera mkamwa mwanga kuti iwo akuyenera kubwelera, pakuti kumene ine ndili iwo sangathe kubwera, pakuti iwo alibe mphamvu.

30 Koma kumbukirani kuti ziweruzo zanga zonse sizidaperekedwe kwa anthu; ndipo monga mawu adapita kuchokera mkamwa mwanga ngakhale motero iwo adzakwaniritsidwa, kuti oyamba adzakhala otsiriza, ndi kuti otsiriza adzakhala oyamba m’zinthu zonse zimene ndalenga ndi mawu a mphamvu yanga, imene ili mphamvu ya Mzimu wanga.

31 Pakuti ndi mphamvu ya Mzimu wanga ndidawalenga iwo; inde, zinthu zonse zauzimu ndi zakuthupi—

32 Choyamba chauzimu, chachiwiri chakuthupi, chomwe chili chiyambi cha ntchito yanga; ndiponso, choyamba chakuthupi, ndipo chachiwiri chauzimu, chomwe chili chomaliza cha ntchito yanga—

33 Ndikuyankhula ndi inu kuti mukamvetsetse mwachibadwa; koma kwa ine ndekha ntchito zanga zilibe chimaliziro, ngakhale chiyambi; koma kwapatsidwa kwa inu kuti mukathe kumvetsa, chifukwa mudapempha kwa ine, ndipo mwavomeredwa.

34 Kotero, indetu ndinena kwa inu kuti zinthu zonse kwa ine ndi zauzimu, ndipo palibe pa nthawi iliyonse ine ndidakupatsani inu lamulo limene lidali lakuthupi; kapena munthu aliyense, kapena ana a anthu; kapena Adamu, atate wanu, amene ndidamulenga.

35 Taonani, ndidampatsa iye kuti akuyenera kukhala wodzithandizira kwa iyemwini; ndipo ndidapereka kwa iye lamulo; koma palibe lamulo lakuthupi lomwe ndidapereka kwa iye, pakuti malamulo anga ndi auzimu; iwo si achibadwidwe kapena akuthupi, kapena achithupithupi kapena athupi.

36 Ndipo zidachitika kuti Adamu, poyesedwa ndi mdyerekezi—pakuti, taonani, Mdyerekezi adalipo asadabwere Adamu, pakuti adandipandukira, kuti, Ndipatseni ulemelero wanu, umene ndi mphamvu yanga; komanso gawo limodzi mwa magawo atatu a makamu akumwamba adandichotsera kwa ine chifukwa cha ufulu wosankha wawo;

37 Ndipo adaponyedwa pansi, ndipo kotero adadza mdyerekezi ndi angelo ake;

38 Ndipo taonani, pali malo okonzedwera iwo kuyambira pachiyambi, amene malowo ndi gahena.

39 Ndipo kukuyenera kukhala kuti mdyerekezi ayese ana a anthu, kapena sakadatha kukhala odzithandizira kwa iwo okha; pakuti ngati sakadakhala ndi zowawa sakadatha kudziwa zokomazo—

40 Kotero, zidachitika kuti mdyerekezi adayesa Adamu, ndipo adadya chipatso choletsedwacho ndipo adaswa lamulo, momwe adakhala wogonjera ku chifuniro cha mdyerekezi, chifukwa adadzipereka ku yesero.

41 Kotero, ine, Ambuye Mulungu, ndidapangitsa kuti aponyedwe kunja kwa Munda wa Edeni, kuchoka pamaso panga, chifukwa cha kulakwa kwake, kumene adakhala wakufa kuuzimu, yomwe ili imfa yoyamba, ngakhale imfa yomweyo imene ili yotsiriza, yomwe ili yauzimu, imene idzanenedwa pa oipa pamene ndidzati: Chokani, otembeleredwa inu.

42 Koma, taonani, ndinena kwa inu kuti ine, Ambuye Mulungu, ndidapereka kwa Adamu ndi kwa mbewu yake, kuti sadzafa monga ku imfa yathupi, mpaka ine, Ambuye Mulungu, nditatumiza angelo kuti alengeze kwa iwo kulapa ndi chiwombolo, kudzera muchikhulupiliro pa dzina la Mwana wanga Wobadwa Yekha.

43 Ndipo motero ine, Ambuye Mulungu, ndidaika kwa munthu masiku a kuyesedwa kwake—kuti ndi imfa yachibadwidwe iye akathe kuwukitsidwam’kusafa kwa moyo wosatha, inde ambiri amene akakhulupilire;

44 Ndipo iwo amene sakakhulupilira ku chiwonongeko chosatha; pakuti sangawomboledwe mu kugwa kwawo kwauzimu, chifukwa iwo sadalape;

45 Pakuti iwo amakonda mdima koposa kuunika, ndipo ntchito zawo ndi zoipa, ndipo amalandira malipiro awo kwa amene afuna kumumvera.

46 Koma taonani, ndinena kwa inu, kuti ana aang’ono ndi owomboledwa kuchokera ku maziko a dziko kudzera mwa wanga Wobadwa Yekha;

47 Kotero, sangathe kuchimwa, pakuti mphamvu sidapatsidwe kwa Satana kuti akayese ana; mpaka akayambe kudziwa kuyankha mlandu pamaso panga;

48 Pakuti kwapatsidwa kwa iwo monga momwe ine ndikufunira, monga mwa kukonda kwanga, kuti padzatha kufunidwa zinthu zazikulu pa dzanja la makolo awo.

49 Ndipo, kachiwiri, ine ndinena kwa inu, kuti amene ali ndi chidziwitso, ine sindidamulamule kuti alape?

50 Ndipo iye amene alibe kumvetsetsa, zitsala mwa ine kuchita monga kwalembedwa. Ndipo tsopano sindikulengezanso kwa inu pa nthawi ino. Ameni.