Gawo 73
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Sidney Rigdon, ku Hiram, Ohio, Januwale 10, 1832. Kuyambira kumayambiliro kwa mwezi wa Disembala wapitawo, Mneneri ndi Sidney adali akugwira ntchito yolalikira, ndipo mwa njira imeneyi zambiri zidakwaniritsidwa mu kuchepetsa malingaliro osakhala bwino amene adabuka motsutsana ndi Mpingo (onani mutu wa gawo 71).
1–2, Akulu akuyenera kupitiriza kulalikira; 3–6, Joseph Smith ndi Sidney Rigdon akuyenera kupitiriza kumasulira Baibulo mpaka litatha.
1 Pakuti indetu, akutero Ambuye, kuli koyenera mwa ine kuti iwo apitirize kulalikira uthenga wabwino, ndi mu chilimbikitso kwa mipingo mu madera ozungulira, kufikira msonkhano;
2 Ndipo kenako, taonani, zidzadziwika kwa iwo, ndi liwu la msonkhano, mautumiki awo angapo.
3 Tsopano, indetu ndinena kwa inu atumiki anga, Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon, atero Ambuye, kuli koyenera kumasuliranso;
4 Ndipo, pamene kuli kothekera, kukalalikira m’madera ozungulira kufikira msonkhano; ndipo pambuyo pake kuli koyenera kupitiriza ntchito yomasulira kufikira itatha.
5 Ndipo lolani ichi chikhale chitsanzo kwa akulu kufikira chidziwitso chowonjezera, ngakhale monga kwalembedwa.
6 Tsopano sindiperekanso zina kwa inu pa nthawi ino. Mangani m’chuuno mwanu ndipo mukhale odziletsa. Ngakhale zili choncho. Ameni.