Gawo 60
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Independence, Jackson County, Missouri, Ogasiti 8, 1831. Pa chochitika chimenechi akulu amene adapita ku Dera la Jackson ndipo adatengatenga nawo mbali pa kupatulira dziko ndi malo a kachisi adafuna kudziwa chimene amayenera kuchita.
1–9, Akulu akuyenera kulalika uthenga wabwino ku misonkhano ya oipa; 10–14, Iwo sakuyenera kutaya nthawi yawo, kapena kukwilira luso lawo; 15–17, Iwo angathe kutsuka mapazi awo ngati umboni otsutsa iwo amene akana uthenga wabwino.
1 Taonani, akutero Ambuye kwa akulu a mpingo wake, amene akuyenera kubwelera mofulumira ku dziko limene adachokera: Taonani, zandikondweretsa ine kuti mwabwera kuno;
2 Koma mwa ena sindidakondwere, pakuti iwo satsekula pakamwa pawo, koma akubisa luso lawo limene ine ndalipereka kwa iwo, chifukwa cha kuopa munthu. Tsoka kwa otero, pakuti mkwiyo wanga wayaka motsutsana nawo.
3 Ndipo zidzachitika, ngati iwo sakhala wokhulupirika kwambiri kwa ine, chidzatengedwa, ngakhale chimene iwo ali nacho.
4 Pakuti ine, Ambuye, Ndimalamulira kuthambo lam’mwamba, ndi pakati pa ankhondo a dziko lapansi; ndipo pa tsiku limene ine ndidzapanga miyala yanga yamtengo wapatali, anthu onse adzadziwa chiti chimene chimayankhula za mphamvu ya Mulungu.
5 Koma, indetu, ndidzayankhula kwa inu zokhudzana ndi ulendo wanu kupita ku dziko lomwe inu mudachokera. Lolani bwato lisemedwe, kapena kugulidwa, monga mutaonele bwino, zilibe kanthu kwa ine, ndipo muyambe ulendo wanu mwachangu ku malo amene akutchedwa St. Louis.
6 Ndipo kuchokera kumeneko lolani atumiki anga, Sidney Rigdon, Joseph Smith, Jun., ndi Oliver Cowdery ayambe ulendo wawo waku Cincinnati;
7 Ndipo mu malo amenewa aloleni iwo akweze mawu awo ndi kulengeza mawu anga ndi liwu lokuwa, opanda mkwiyo kapena chikaiko, kukwezera m’mwamba manja oyera pa iwo. Pakuti ine ndili okutha kukupanga inu oyera, ndipo machimo anu akhululukidwa.
8 Ndipo lolani otsalawo ayambe ulendo wawo kuchokera ku St. Louis, awiri awiri, ndi kulalika mawu, osati mwamachawi, pakati pa misonkhano ya oipa, kufikira iwo atabwelera ku mipingo imene iwo adachokera
9 Ndipo zonsezi chifukwa cha ubwino wa mipingo; pa cholinga chimenechi ine ndawatuma iwo.
10 Ndipo lolani mtumiki wanga Edward Partridge agawe ndalama zimene ine ndamupatsa iye, gawo limodzi kwa akulu anga amene alamulidwa kuti abwelere;
11 Ndipo iye amene angathe, muloleni azibwenze kudzera mu njira ya mtumiki; ndipo iye amene sangathe, kwa iyeyo sizikufunidwa.
12 Ndipo tsopano ndiyankhula za otsala amene akuyenera kubwera ku malo ano.
13 Taonani, iwo atumizidwa kukalalika uthenga wanga wabwino pakati pa misonkhano ya oipa; kotero, ndikupereka kwa iwo lamulo, kuti: Musataye nthawi yanu, kapena kukwilira luso lanu kuti lisadziwike.
14 Ndipo inu mukatha kubwera ku dziko la Ziyoni, ndipo mwalengeza mawu anga, mudzabwelera mwachangu, kulengeza mawu anga pakati pa misonkhano ya oipa, osati mwamachawi, ngakhale mwa mkwiyo kapena ndi ndewu.
15 Ndipo sasani fumbi la kumapazi anu motsutsa iwo amene sadakulandireni, osati pamaso pawo, kuopa mungawakwiyitse iwo, koma mwa chinsinsi; ndipo tsukani mapazi anu, ngati umbonu otsutsana nawo mu tsiku la chiweruzo.
16 Taonani, izi ndi zokwanira kwa inu, ndi chifuniro cha iye amene wakutumani inu.
17 Ndipo ndi pakamwa pa mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., chidzadziwitsidwa chokhudzana ndi Sidney Rigdon ndi Oliver Cowdery. Otsalawo pambuyo pake. Ngakhale choncho. Ameni.