Gawo 80
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Stephen Burnett, ku Hiram, Ohio, Malitchi 7, 1832.
1–5, Stephen Burnett ndi Eden Smith aitanidwa kukalalikira malo ena aliwonse omwe angasankhe.
1Â Indetu, akutero Ambuye kwa iwe mtumiki wanga Stephen Burnett: Pita, pita kudziko ndi kukalalikira uthenga wabwino kwa cholengedwa chilichonse chimene chidzagonja pansi pa kumveka kwa mawu ako.
2Â Ndipo pamene iwe wakhumba mzako, ndidzapereka kwa iwe mtumiki wanga Eden Smith.
3 Kotero, pita ndi kukalalikira uthenga wanga wabwino, kaya ku mpoto kapena kum’mwera, kum’mawa kapena kumadzulo, zilibe kanthu, pakuti sungapite pachabe.
4Â Potero, lengeza zinthu zimene iwe wazimva, ndi kuzikhulupilira ndithu, komanso kudziwa kuti ndi zoona.
5Â Taona, ichi ndi chifuniro cha iye amene wakuitana iwe, Muwomboli wako, ngakhale Yesu Khristu. Ameni.