Gawo 17
Vumbulutso loperekedwa kudzera kwa Joseph Smith Mneneri kwa Oliver Cowdery, David Whitmer, ndi Martin Harris, ku Fayette, New York, Juni 1829, asadaone mapale ozokotedwa amene adali ndi zolemba za Buku la Mormoni. Joseph ndi mlembi wake, Oliver Cowdery, adali ataphunzira kuchokera mu kumasulira kwa mapale a Buku la Mormoni kuti mboni zitatu zapadera zidzasankhidwa (onani Eteri 5:2–4;2 Nefi 11:3;27:12). Oliver Cowdery, David Whitmer, ndi Martin Harris adasunthika mwa chikhumbo chouziridwa kuti akhale mboni zapadera. Mneneri adafunsa kwa Ambuye, ndipo vumbulutso ili lidaperekedwa mu yankho kudzera mu Urimu ndi Tumimu.
1–4, Mwa chikhulupiliro Mboni Zitatu zidzaona mapale ndi zinthu zina zopatulika; 5–9, Khristu achitira umboni wa umulungu wa Buku la Mormoni.
1 Taonani, ndinena kwa inu, kuti mukuyenera kudalira pa mawu anga, amene ngati mutatero ndi mtima wonse, mudzaonetsedwa mapale, ndiponso chapachifuwa, lupanga la Labani, Urimu ndi Tumimu, zimene zidaperekedwa kwa m’bale wa Yaredi pa phiri, pamene iye adayankhula ndi Ambuye maso ndi maso, ndi zosonyezera zozizwitsa zimene zidaperekedwa kwa Lehi pamene iye adali m’chipululu, ku malire a Nyanja Yofiira.
2 Ndipo ndi mwa chikhulupiliro chanu kuti mudzaziona izo, ngakhale mwa icho chikhulupiliro chimene adali nacho aneneri akale.
3 Ndipo mutatha kulandira chikhulupiliro, ndi kuziona ndi maso anu, mudzachitira umboni wa izo, mwa mphamvu ya Mulungu;
4 Ndipo izi mudzachita kuti mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., asathe kuwonongedwa, kuti ndithe kubweretsa cholinga cha chilungamo changa kwa ana a anthu mu ntchitoyi.
5 Ndipo inu mudzachitira umboni kuti mwaziona, ngakhale monga mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., wazionera izo; pakuti ndi mwa mphamvu yanga kuti iye waziona izo, ndipo ndi chifukwa iye adali ndi chikhulupiliro.
6 Ndipo iye wamasulira bukuli, ngakhale gawo limene ine ndamulamula iye, ndipo monga Ambuye wanu ndi Mulungu wanu alimoyo ndi zoona.
7 Chotero, inu mwalandira mphamvu yomweyo, ndi chikhulupiliro chomwecho, ndi mphatso yomweyo monga kwa iye;
8 Ndipo ngati muchita malamulo anga omalizawa, amene ine ndakupatsani, zipata za gahena sizidzapambana motsutsana nanu; pakuti chisomo changa ndi chokwanira kwa inu, ndipo inu mudzakwezedwa pa tsiku lomaliza.
9 Ndipo ine, Yesu Khristu, Ambuye wanu ndi Mulungu wanu, ndayankhula kwa inu, kuti ndithe kubweretsa zolinga za chilungamo changa kwa ana a anthu. Ameni.