Gawo 65
Vumbulutso la pemphero loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, Okotobala 30, 1831.
1–2, Mafungulo a ufumu wa Mulungu aperekedwa kwa munthu pa dziko lapansi, ndipo cholinga cha uthenga wabwino chidzapambana; 3–6, Ufumu wa zaka chikwi wa kumwamba udzabwera ndi kuphatikizana ndi ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi.
1 Mvetserani, ndipo onani, liwu langati m’modzi otumidwa kuchokera kumwamba, amene ali wamphamvu, amene kupita kwake ndi kwa malekezero a dziko lapansi, inde. Amene mawu ake ndi a kwa anthu—Konzerani njira ya Ambuye, pangani njira zake zowongoka.
2 Mafungulo a ufumu wa Mulungu aperekedwa kwa munthu pa dziko lapansi, ndipo kuchokera kumeneko uthenga wabwino udzafala mpaka ku malekezero a dziko lapansi, monga mwala umene wasemedwa kuchokera ku phiri osati ndi manja udzagubudukira, kufikira utadzadza dziko lonse lapansi.
3 Inde, liwu lofuula—Konzekerani njira ya Ambuye, konzekerani mgonero wa Mwana wa Nkhosa, ndikukhonzekera Mkwati.
4 Pempherani kwa Ambuye, itanirani pa dzina lake loyera, dziwitsani ntchito zake zodabwitsa pakati pa anthu.
5 Itanirani pa Ambuye, kuti ufumu wake ukapite pa dziko lapansi, kuti okhala m’menemo akaulandire, ndipo khonzekerani ku masiku alinkudza, mumene Mwana wa Munthu adzatsika kumwamba, atavekedwa mu kuwala kwa ulemelero wake, kukakumana ndi ufumu wa Mulungu umene wakhazikitsidwa pa dziko lapansi.
6 Kotero, ufumu wa Mulungu ukathe kupita patsogolo, kuti ufumu wa kumwamba ukathe kubwera, kuti inu, O Mulungu, mukathe kulemekezedwa kumwamba choncho pansi pano, kuti adani anu akathe kugonjetsedwa; pakuti wanu ndi ulemu, mphamvu ndi ulemelero, kwanthawi zosatha. Ameni.