Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 100


Gawo 100

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Sidney Rigdon, ku Perrysburg, New York, Okotobala 12, 1833. Abale awiriwo, pokhala atachoka kwa mabanja awo kwa masiku angapo, adali ndi nkhawa ina yowakhudza iwo.

1–4, Joseph ndi Sidney akalalikire uthenga wa chipulumutso cha miyoyo; 5–8, Chidzapatsidwa kwa iwo mu ola lomwelo chimene akuyenera kunena; 9–12, Sidney akuyenera kukhala woyankhulira ndipo Joseph akuyenera kukhala wovumbulutsa ndi wamphamvu mu umboni; 13–17, Ambuye adzadzutsa anthu oyera, ndipo omvera adzapulumutsidwa.

1 Indetu, akutero Ambuye kwa inu, abwenzi anga Sidney ndi Joseph, mabanja anu ali bwino; iwo ali m’manja mwanga, ndipo ine ndidzachita nawo iwo monga ine ndakondera; pakuti mwa ine muli mphamvu zonse.

2 Kotero, nditsatireni, ndipo mverani uphungu umene ndidzakupatsani.

3 Taonani, ndipo onani, ndili ndi anthu ambiri m’malo ano, m’madera ozungulira; ndipo khomo logwira ntchito lidzatsegulidwa m’madera ozungulira dziko lino lakum’mawa.

4 Kotero, ine, Ambuye, ndakulolani inu kuti mubwere ku malo awa; pakuti kotero kudali koyenera mwa ine ku chipulumutso cha miyoyo.

5 Kotero, indetu ndinena kwa inu, kwezani mawu anu kwa anthu awa; yankhulani maganizo amene ndidzaika m’mitima yanu, ndipo simudzasokonezedwa pamaso pa anthu;

6 Pakuti chidzapatsidwa kwa inu mu ola lomwelo, inde, mu kamphindi komweko, chimene mudzayankhule.

7 Koma lamulo ndikupereka kwa inu, kuti mulengeze chinthu chilichonse chimene mungalengeze mu dzina langa, mu kulemekeza kwa mtima, mu mzimu wa chifatso, mu zinthu zonse.

8 Ndipo ine ndikupereka kwa inu lonjezo ili, kuti pamene mukuchita ichi Mzimu Woyera udzatsanuliridwa mu kuchitira umboni kwa zinthu zonse zomwe mutadzanene.

9 Ndipo ndi koyenera mwa ine kuti iwe, mtumiki wanga Sidney, ukuyenera kukhala woyankhulira kwa anthu awa; inde, ngakhale, ine ndidzakudzodza iwe ku maitanidwe awa, ngakhale kukhala woyankhulira kwa mtumiki wanga Joseph.

10 Ndipo ndidzampatsa iye mphamvu yakukhala wamphamvu mu umboni.

11 Ndipo ndidzakupatsa mphamvu kuti ukhale wamphamvu mu kufotokoza malemba onse, kuti ukhale woyankhulira kwa iye, ndipo iye adzakhala wovumbulutsa kwa iwe, kuti ukathe kudziwa chitsimikizo cha zinthu zonse zokhudzana ndi ufumu wanga padziko lapansi.

12 Kotero, pitirizani ulendo wanu ndipo mitima yanu isangalale; pakuti taonani, ndipo onani, ine ndili ndi inu mpaka ku mapeto.

13 Ndipo tsopano ndikupereka kwa inu mawu okhudzana ndi Ziyoni. Ziyoni adzawomboledwa, ngakhale akulangidwa kwa kanyengo kochepa.

14 Abale anu, atumiki anga Orson Hyde ndi John Gould, ali m’manja mwanga; ndipo pamene iwo asunga malamulo anga adzapulumutsidwa.

15 Kotero, mitima yanu itonthozedwe; pakuti zinthu zonse zidzagwilira ntchito pamodzi kwa ubwino kwa iwo akuyenda mowongoka, ndi ku chiyeretso cha Mpingo.

16 Pakuti ndidzadzidzutsira anthu oyera, amene adzanditumikira mu chilungamo;

17 Ndipo onse amene amaitanira pa dzina la Ambuye, ndikusunga malamulo ake, adzapulumutsidwa. Ngakhale choncho. Ameni.