Gawo 22
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Mneneri Joseph Smith, ku Manchester, New York, April 16, 1830. Vumbulutso limeneli lidaperekedwa ku Mpingo chifukwa cha ena amene adali atabatizidwa kale kufuna kugwirizana ndi Mpingo popanda kubatizidwanso.
1, Ubatizo ndi pangano latsopano ndi losatha; 2–4, Ubatizo wovomerezeka ndi wofunika.
1 Taonani, ndikunena kwa inu kuti mapangano akale onse ndawachititsa kuti athetsedwe mu chinthu ichi; ndipo ili ndi pangano latsopano ndi losatha, ngakhale ilo lomwe lidali kuyambira pachiyambi.
2 Kotero, angakhale munthu abatizidwe kakhumi sikumuthandiza kanthu; pakuti simungathe kulowa pa chipata chopapatiza ndi chilamulo cha Mose, kapena ndi ntchito zanu zakufa.
3 Pakuti ndi chifukwa cha ntchito zanu zakufa kuti ndapanga pangano lotsiriza ili ndi mpingo uwu kuti umangidwe kwa ine, monga m’masiku akale.
4 Kotero, lowani inu pa chipata, monga ndalamulira, ndipo musafunefune kulangiza Mulungu wanu. Ameni.