Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 85


Gawo 85

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Novembala 27, 1832. Gawoli ndi lochokera mu kalata ya Mneneri yopita kwa William W. Phelps, yemwe adali kukhala ku Independence, Missouri. Likuyankha mafunso okhudza Oyera Mtima awo amene adasamukira ku Ziyoni koma amene sadatsatire lamulo la kupatulira katundu wawo ndipo motero sadalandire cholowa chawo molingana ndi dongosolo lokhazikitsidwa mu Mpingo.

1–5, Zolowa mu Ziyoni zikuyenera kulandiridwa kudzera mwa kudzipatulira; 6–12, M’modzi wamphamvu ndi wanyonga adzapereka kwa Oyera mtima cholowa chawo mu Ziyoni.

1 Ndi ntchito ya mlembi wa Ambuye, amene iye wamusankha, kusunga mbiri yakale, ndi mbiri ya mpingo wonse wa zinthu zonse zimene zikuchitika mu Ziyoni, ndi za onse amene amapatulira katundu, ndi kulandira cholowa mwalamulo kuchokera kwa bishopu;

2 Ndiponso makhalidwe awo a moyo, chikhulupiliro chawo, ndi ntchito; ndiponso ampatuko omwe apatuka atatha kulandira cholowa chawo.

3 Ndi zosemphana ndi chifuniro ndi lamulo la Mulungu kuti iwo amene salandira cholowa chawo mwa kudzipatulira, mogwirizana ndi lamulo lake, limene iye wapereka, kuti akathe kupereka chakhumi kwa anthu ake, kuwakonzekeretsa iwo pa tsiku la kubwenzera ndi kuwotcha, mayina awo akuyenera kulembedwa pamodzi ndi anthu a Mulungu.

4 Ngakhalenso mndandanda wa mibadwo yawo sukuyenera kusungidwa, kapena kukhala nawo pomwe ungathe kupezeka pa zolembedwa zilizonse kapena mbiri ya mpingo.

5 Mayina awo sadzapezeka, kapena mayina a makolo, kapena mayina a ana olembedwa m’buku la chilamulo cha Mulungu, akutero Ambuye wa makamu.

6 Inde, atero mawu ofatsa onong’ona; amene amanong’oneza ndi kupyoza zinthu zonse, ndipo nthawi zambiri amapangitsa mafupa anga kunjenjemera pamene akuwonekera, nati:

7 Ndipo zidzachitika kuti ine, Ambuye Mulungu, ndidzatumiza m’modzi wamphamvu ndi wanyonga, wonyamula ndodo yamphamvu m’dzanja lake, wovekedwa ndi kuwala kophimba, amene mkamwa mwake mudzayankhula mawu, mawu amuyaya; pamene matumbo ake adzakhala kasupe wa choonadi, kukonza nyumba ya Mulungu, ndi kukonza mwa maere cholowa cha oyera mtima amene mayina awo apezeka, ndi mayina a makolo awo, ndi ana awo, olembedwa m’buku la chilamulo cha Mulungu;

8 Pamene munthu ameneyo, amene adaitanidwa ndi Mulungu ndi kusankhidwa, amene amatambasula dzanja lake kuti alimbitse chombo cha Mulungu, adzagwa ndi tsinde la imfa, monga mtengo umene wakanthidwa ndi tsinde lowala la mphezi.

9 Ndipo onse amene sadapezeke atalembedwa mu Buku la chikumbutso sadzapeza cholowa pa tsiku limenelo, koma adzadulidwa pakati, ndipo gawo lawo lidzawaika pamodzi ndi osakhulupilira, kumene kuli kulira ndi kukukuta mano.

10 Zinthu izi sindikunena mwa ine ndekha; kotero, monga ayankhula Ambuye, iwo adzakwaniritsanso.

11 Ndipo iwo amene ali a Unsembe Waukulu, amene maina awo sadapezeke olembedwa mu buku la chilamulo, kapena amene apezedwa kukhala ampatuko, kapena kuti adadulidwa kuchoka mu mpingo, pamodzi ndi ansembe aang’ono, kapena mamembala, mu tsiku limenelo sadzapeza cholowa pakati pa oyera mtima a Wamkulukulu;

12 Kotero, zidzachitidwa kwa iwo monga kwa ana a wansembe, monga zidzapezeka zolembedwa m’mutu wachiwiri ndi ndime za makumi asanu ndi limodzi mphambu imodzi ndi yachiwiri ya Ezara.