Gawo 27
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Harmony, Pennsylvania, Ogasiti 1830. Pokonzekera mwambo wachipembedzo umene pamayenera kuperekedwa m’gonero wa mkate ndi vinyo, Joseph adanyamuka kukagula vinyo. Iye adakumana ndi mthenga wakumwamba ndipo adalandira vumbulutso ili, gawo lomwe lidalembedwa pa nthawiyo ndipo lina lidalembedwa mu Seputembera wotsatira. Madzi tsopano amagwiritsidwa ntchito m’malo mwa vinyo mu mapemphero a m’gonero wa Mpingo.
1–4, Zizindikiro zogwiritsiridwa ntchito pokudya m’gonero zakhazikitsidwa; 5–14, Khristu ndi atumiki Ake kuchokera m’nyengo zonse akuyenera kudya m’gonero; 15–18, Valani zida zonse za Mulungu.
1 Mvetsera ku mawu a Yesu Khristu, Ambuye wako, Mulungu wako, ndi Muwomboli wako, amene mawu ake ali achangu ndi amphamvu.
2 Pakuti, taona, ndinena kwa iwe, kuti zilibe kanthu chimene mudzadya kapena chimene mudzamwa pamene mukudya m’gonero, ngati zingakhale kuti mukuchita ndi diso lolunjika ku ulemelero wanga—kukumbukira kwa Atate thupi langa limene lidaikidwa pansi chifukwa cha inu, ndi mwazi wanga womwe udakhetsedwa ku chikhululukiro cha machimo anu.
3 Kotero, lamulo ine ndikupereka kwa iwe, kuti iwe usagule vinyo kapena chakumwa choledzeretsa cha adani ako;
4 Kotero, simudzadya chilichonse kupatula icho chopangidwa chatsopano pakati panu; inde, mu ufumu wa Atate anga uno umene udzamangidwa pa dziko lapansi.
5 Taona, iyi ndi nzeru mwa ine; kotero, usadabwe;pakuti ola likudza limene ndidzamwa chipatso cha mpesa pamodzi ndi iwe padziko lapansi, ndi Moroni, amene ndamutuma kwa iwe kuti ndivumbulutse Bukhu la Mormoni, lokhala ndi chidzalo cha uthenga wabwino wamuyaya, kwa amene ndapereka mafungulo a cholembedwa cha ndodo ya Efraimu;
6 Ndiponso ndi Eliya, kwa iye amene ndapereka mafungulo a kubweretsa chibwenzeretso cha zinthu zonse zoyankhulidwa ndi pakamwa pa aneneri onse oyera chiyambire dziko lapansi, zokhudza masiku otsiriza;
7 Ndiponso Yohane mwana wa Zakariya, amene Zakariya iye (Eliya) adamuyendera ndikupereka lonjezo kuti adzakhala ndi mwana wamwamuna, ndipo dzina lake lidzakhala Yohane, ndipo iye adzadzadzidwa ndi mzimu wa Eliya;
8 Amene Yohane ndamutuma kwa inu, atumiki anga, Joseph Smith, Jun., ndi Oliver Cowdery, kuti akudzodzeni ku unsembe woyamba umene mudalandira, kuti mukathe kuyitanidwa ndi kudzodzedwa ngakhale monga Aroni;
9 Ndiponso Eliya, amene ndidamupatsa mafungulo a mphamvu yakutembenuzira mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate, kuti dziko lonse lapansi lisathe kukanthidwa ndi thembelero;
10 Ndiponso ndi Joseph ndi Yakobo, ndi Isaki, ndi Abrahamu, makolo ako, amene malonjezano akhala mwa iwo;
11 Ndiponso ndi Mikaeli, kapena Adamu, atate wa onse, kalonga wa onse, makedzana wa masiku;
12 Ndiponso pamodzi ndi Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, amene ndidawatuma kwa inu, mwa amene ndidakudzodzani inu, ndi kukutsimikizirani inu kuti mukhale atumwi, ndi mboni zapadera za dzina langa, ndi kutenga mafungulo a utumiki wanu, ndi a zinthu zomwezo zimene ine ndavumbulutsa kwa iwo;
13 Kwa amene ndapereka mafungulo a ufumu wanga, ndi nyengo ya uthenga wabwino kwa nthawi zotsiriza; ndi chidzalo cha nthawi, m’mene ndidzasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse, za m’mwamba, ndi za pa dziko lapansi;
14 Ndiponso ndi onse amene Atate adandipatsa ine kuchokera ku dziko lapansi.
15 Kotero, kwezani mitima yanu ndi kusangalala, ndipo mangani lamba wa m’chuuno mwanu, ndipo valani pa inu zida zanga zonse, kuti mukathe kupilira tsiku loipa, mutachita zonse, kuti mudzathe kuima.
16 Kotero, imani, mutadzimangilira m’chuuno mwanu ndi choonadi, mutavala chapachifuwa cha chilungamo, ndi mapazi anu mutavala chikonzekero cha Uthenga Wabwino wa mtendere, umene ndidatuma angelo anga kuti aupereke kwa inu;
17 Mutengenso chishango cha chikhulupiliro chimene mudzatha kuzimitsa nacho mivi yonse yoyaka moto ya oipayo;
18 Ndipo tenganinso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la mzimu wanga, limene ndidzatsanulira pa inu, ndi mawu anga amene ine ndivumbulutsa kwa inu, ndipo adzagwirizana pa zinthu zonse zimene mupempha kwa ine, ndipo khalani okhulupirika kufikira ine nditabwera, ndipo mudzakwatulidwa, kuti kumene kuli ine, inunso mudzakhaleko. Ameni.