Gawo 87
Vumbulutso ndi uneneri wa nkhondo, woperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Disembala 25, 1832. Panthawiyi mikangano ku United States yokhudzana ndi ukapolo ndi kuchotsedwa kwa msonkho wa federal South Carolina idali itafala. Mbiri ya Joseph Smith imanena kuti “maonekedwe a mavuto pakati pa mafuko” adali kukhala “owonekera” kwa Mneneri “kuposa momwe adalili poyamba pamene Mpingo udayamba ulendo wake wochoka m’chipululu.”
1–4, Nkhondo idaneneledweratu pakati pa Northern States ndi Southern States; 5–8, Matsoka aakulu adzagwera onse okhala padziko lapansi.
1 Indetu, akutero Ambuye zokhudzana ndi nkhondo zimene zidzachitika posachedwa, kuyambira pa kupanduka kwa South Carolina, kumene kudzathera mu imfa ndi kuzunzika kwa miyoyo yambiri;
2 Ndipo idzafika nthawi imene nkhondo idzatsanuliridwa pa mitundu yonse, kuyambira pamalo ano.
3 Pakuti taonani, a ku Southern States adzagawanika motsutsana ndi a ku Northern States, ndipo Maiko a ku Southern States adzaitana pa mitundu ina, ngakhale mtundu wa Great Britain, monga umatchedwa, ndipo iwo adzaitananso pa mitundu ina, kuti adziteteze ku mitundu ina; ndipo pamenepo nkhondo idzatsanuliridwa pa maiko onse.
4 Ndipo zidzachitika kuti, pakadzapita masiku ambiri, akapolo adzaukira ambuye awo, amene adzasonkhanitsidwa ndi kulangidwira kunkhondo.
5 Ndipo zidzachitikanso kuti otsalira amene atsala a m’dzikolo adzadzisonkhanitsa okha, ndipo adzakwiya kopambana, ndipo adzasautsa Amitundu ndi kusautsidwa kowawa.
6 Ndipo motero, ndi lupanga ndi kukhetsa mwazi okhala pa dziko lapansi adzalira; ndi njala, ndi mliri, ndi chibvomelezi, ndi bingu la kumwamba, ndi mphezi yoopsa ndi yothwanima, iwo okhala padziko lapansi adzamva mkwiyo, ndi ukali, ndi kulanga kwa dzanja la Mulungu Wamphamvu zonse, kufikira chiwonongeko chitatha maiko onse;
7 Kuti kulira kwa oyera mtima, ndi mwazi wa oyera mtima, kudzaleka kukwela m’makutu a Ambuye wa Makamu, kuchokera ku dziko lapansi, kubwenzera chilango adani awo.
8 Kotero, imani inu m’malo opatulika, ndipo musagwedezeke, kufikira tsiku la Ambuye lifike; pakuti taonani, likudza msanga, atero Ambuye. Ameni.