Gawo 8
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Oliver Cowdery, ku Harmony, Pennsylvania, Epulo 1829. M’kati mwa kumasulira kwa Buku la Mormoni, Oliver, yemwe adapitiliza kutumikira monga mlembi, akulemba pa mawu a Mneneri, adafuna kupatsidwa mphatso ya kumasulira. Ambuye adayankha pempho lake popereka vumbulutsoli.
1–5, Vumbulutso limadza ndi mphamvu ya Mzimu Woyera; 6–12, Chidziwitso cha zinsinsi za Mulungu ndi mphamvu ya kumasulira zolemba zakale zimadza mwa chikhulupiliro.
1 Oliver Cowdery, indetu, indetu, ndinena kwa iwe, kuti ndithu monga Ambuye ali wamoyo, amene ali Mulungu wako ndi Muwomboli wako, ngakhale kotero ndithudi udzalandira chidziwitso cha zinthu zilizonse zimene udzapempha mu chikhulupiliro, ndi mtima woona, pokhulupilira kuti udzalandira chidziwitso chokhudza zozokota za zolemba zamakedzana, zomwe zili zakale, zomwe zili ndi zigawo izo za malemba anga omwe ayankhulidwa ndi kuwonetseredwa kwa Mzimu wanga.
2 Inde, taona, ndidzakuuza iwe m’malingaliro ako ndi mu mtima mwako, mwa Mzimu Woyera, umene udzafika pa iwe, umene udzakhala mu mtima mwako.
3 Tsopano, taona, uwu ndi mzimu wa vumbulutso; taona, uwu ndi mzimu umene Mose adatsogolera ana a Israeli kudusa pa Nyanja Yofiira panthaka youma.
4 Kotero iyi ndi mphatso yako; igwiritse ntchito iyo, ndipo ndiwe wodala, pakuti idzakupulumutsa iwe kuchokera m’manja mwa adani ako, pamene, ngati sikudali kotero, iwo akadakupha iwe ndi kubweretsa moyo wako ku chiwonongeko.
5 O, kumbukira mawu awa, ndipo sunga malamulo anga. Kumbukira, iyi ndi mphatso yako.
6 Tsopano iyi si mphatso yako yokha; pakuti uli nayo mphatso ina, imene ndi mphatso ya Aroni; taona, yakuuza iwe zinthu zambiri;
7 Taona, palibe mphamvu ina, kupatula mphamvu ya Mulungu, imene ingapangitse mphatso ya Aroniyi kukhala ndi iwe.
8 Kotero, usakayikire, pakuti ndi mphatso ya Mulungu; ndipo udzayigwira m’manja mwako, ndi kuchita ntchito zodabwitsa; ndipo palibe mphamvu ingadzakwanitse kuyichotsa m’manja mwako, pakuti ndi ntchito ya Mulungu.
9 Ndipo, kotero, chilichonse chimene udzandifunsa kuti ndikuuze mwanjira imeneyoyo, ndidzakupatsa iwe, ndipo udzakhala ndi chidziwitso chokhudza chimenechocho.
10 Kumbukira kuti popanda chikhulupiliro sungathe kuchita kanthu; kotero pempha mwa chikhulupiliro. Osasewera ndi zinthu izi; usapemphe icho chimene sukuyenera.
11 Pempha kuti ukathe kudziwa zinsinsi za Mulungu, ndipo kuti iwe ukathe kumasulira ndi kulandira chidziwitso kuchokera mu zolemba zakale zonsezo zimene zabisidwa, zimene zili zopatulika; ndipo molingana ndi chikhulupiliro chako, zidzachitidwa kwa iwe.
12 Taona, ndi ine amene ndayankhula ichi; ndipo ndine yemweyo amene ndidayankhula kwa iwe kuchokera pachiyambi. Ameni.