Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 117


Gawo 117

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Mneneri, ku Far West, Missouri, Julaye 8, 1838, lokhudzana ndi maudindo anthawi yomweyo a William Marks, Newel K, Whitney ndi Oliver Granger.

1–9, Atumiki a Ambuye sakuyenera kusilira zinthu zakuthupi, pakuti “Kodi katundu ndi chiyani kwa Ambuye?”; 10–16, Iwo akuyenera kusiya chibwana cha moyo, ndipo nsembe zawo zidzakhala zopatulika kwa Ambuye.

Indetu akutero Ambuye kwa mtumiki wanga William Marks, ndiponso kwa mtumiki wanga Newel K. Whitney, aloleni iwo alongosole malonda awo mwachangu ndi kuyenda kuchokera ku dziko la Kirtland, ine Ambuye ndisadatumizenso chisanu pa dziko lapansi.

Aloleni adzuke, ndi kuima, ndi kubwera patsogolo, ndipo asachedwe, pakuti ine, Ambuye, ndalamula ichi.

Kotero, ngati iwo achedwa sizidzakhala bwino ndi iwo.

Aloleni iwo alape machimo awo onse, ndi zilakolalo zawo zonse zosilira, pamaso panga, atero Ambuye; pakuti kodi katundu ndi chiyani kwa ine? atero Ambuye.

Lolani katundu wa Kirtland abwenzedwe ku ngongole, atero Ambuye. Aloleni apite, atero Ambuye, ndi zinazonse zotsala, lolani zikhale mu manja anu, atero Ambuye.

Pakuti kodi ine ndilibe mbalame za mlengangalenga, ndiponso nsomba za mnyanja, ndi zilombo za m’mapiri? Kodi ine sindidapange dziko lapansi? Kodi ine sindisunga tsogolo la ankhondo onse a maiko a dziko lapansi?

Kotero, kodi ine sindidzapangitsa malo achipululu kuphukira masamba ndi kutulutsa maluwa, ndi kubala zochuluka? Atero Ambuye.

Kodi kulibe malo okwanira pa mapiri a Adamu-ondi-Ahmani, ndi mu zigwa za Olaha Shineha, kapena malo amene Adamu adakhalako, kuti inu muzisilira icho chimene chili koma kachidutswa, ndi kunyalanyaza zinthu zofunikira kwambiri?

Kotero, bwerani kuno ku dziko la anthu anga, ngakhale Ziyoni.

10 Mloleni mtumiki wanga William Marks akhale okhulupirika pa zinthu zochepa, ndipo iye adzakhala olamulira pa zambiri. Mloleni iye atsogolere pakati pa anthu anga mu mzinda wa Far West, ndipo mloleni iye adalitsidwe ndi madalitso a anthu anga.

11 Mlolemi mtumiki wanga Newel K. Whitney achite manyazi ndi gulu la Nicolai ndi zonyansa zawo zonse zachinsinsi, ndi zilakolako zake zonse za moyo pamaso panga, atero Ambuye, ndi kubwera ku dziko la Adamu-ondi-Ahmani, ndi kukhala bishopu kwa anthu anga, atero Ambuye, osati mu dzina koma mu ntchito, atero Ambuye.

12 Ndiponso, ndinena kwa inu, ndikukumbukira mtumiki wanga Oliver Granger; taoani, indetu ndinena kwa iye kuti dzina lake lidzakumbukiridwa mopatulika kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo, kunthawi ndi nthawi, atero Ambuye.

13 Kotero, mloleni iye alimbane moona mtima ku chiwombolo cha Utsogoleri oyamba wa Mpingo wanga, atero Ambuye; ndipo pamene iye adzagwa iye adzadzukanso, pakuti nsembe yake idzakhala yopatulika kwambiri kwa ine kuposa kukula kwake, atero Ambuye.

14 Kotero, mloleni iye abwere kuno mwachangu, ku dziko la Ziyoni; ndipo mu nthawi yoikika iye adzapangidwa wamalonda ku dzina langa, atero Ambuye, ku phindu la anthu anga.

15 Kotero musalore munthu aliyense anyoze mtumiki wanga Oliver Granger, koma lolani madalitso a anthu anga akhale pa iye kunthawi za nthawi.

16 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, lolani atumiki anga onse mu dziko la Kirtland akumbukire Ambuye Mulungu wawo, ndi nyumba yanganso, kuisunga ndi kuiteteza iyo yoyera, ndi kuthamangitsa osintha ndalama mu nthawi yanga yoikika, atero Ambuye. Ngakhale choncho. Ameni.