Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 48


Gawo 48

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Malichi 10, 1831. Mneneri adafunsa kwa Ambuye za njira yopezera malo okhazikikamo a Oyera mtima. Imeneyi idali nkhani yofunika polingalira kusamuka kwa mamembala a Mpingo kuchokera kum’mawa kwa United States, mu kumvera lamulo la Ambuye lakuti akuyenera kusonkhana mu Ohio (onani zigawo 37:1–3; 45:64).

1–3, Oyera mtima mu Ohio akuyenera kugawana malo awo ndi abale awo; 4–6, Oyera mtima akuyenera kugula malo, kumanga mzinda, ndi kutsatira uphungu wa atsogoleri awo.

1 Ndikofunikira kuti mukhalebe pakadali pano m’malo anu okhalamo, monga momwe zidzakhalire pamakhalidwe anu.

2 Ndipo pamene monga muli ndi minda, inu mugawire abale a kum’mawa;

3 Ndipo pamene mulibe minda, mulole iwo agule pakali pano m’madera ozungulira, monga momwe akondera;pakuti pakuyenera kukhala kofunikira kuti akhale ndi malo okhalamo pa nthawi ino.

4 Kukuyenera kukhala kofunikira kuti musunge ndalama zonse zomwe mungathe, ndi kuti mulandire zonse zomwe mungathe muchilungamo, kuti mukupita kwa nthawi muthe kuloledwa kugula malo kukhala cholowa, ngakhale mzinda.

5 Malowo sadaululidwebe; koma akafika abale anu kuchokera kum’mawa padzakhala amuna ena osankhidwa, ndipo kudzapatsidwa kwa iwo kudziwa malowo, kapena kwa iwo kudzaululidwa.

6 Ndipo adzasankhidwa kuti agule malo, ndi kuyamba kuyala maziko a mzinda; Ndipo kenako mudzayamba kusonkhana pamodzi ndi mabanja anu, munthu aliyense molingana ndi banja lake, molingana ndi makhalidwe ake, ndi monga kusankhidwa kwa iye ndi utsogoleri ndi bishopu wa mpingo, molingana ndi zilamulo ndi malamulo omwe mwalandira, ndi amene mudzawalandira pambuyo pake. Ngakhale zili choncho. Ameni.