Gawo 111
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Salem, Massachusetts, Ogasiti 6, 1836. Pa nthawi imeneyi, Mpingo ndi atsogoleri ake adali ndi ngongole yaikulu chifukwa cha kumanga kwa Kachisi ya Kirtland ndi mazunzo mu Missouri. Pomva kuti ndalama zochuluka zingathe kupezeka kwa iwo mu Salem, Mneneri, Sidney Rigdon, Hyrum Smith, ndi Oliver Cowdery adapita kumeneko kuchokera ku Kirtland, Ohio, kuti akafufuze zonenedwazi, kuphatikizirapo kulalikira uthenga wabwino. Abalewo adachitapo zinthu zingapo za Mpingo komanso kulalikira. Pamene chidakhala chachidziwikire kuti palibe ndalama zomwe zikuyenera kubwera, adabwelera ku Kirtland.
1–5, Ambuye amayang’ana ku zosowa zakuthupi za atumiki Ake; 6–11, Adzachita mwachifundo ndi Ziyoni ndi kukonza zinthu zonse mu ubwino wa atumiki Ake.
1Â Ine, Ambuye Mulungu wanu, sindili wokondwa ndi kubwera kwanu ulendo uno, posatengela zopusa zanu.
2Â Ndili ndi chuma chambiri mu mzinda muno cha inu, chopindulira Ziyoni, ndi anthu ambiri a mumzinda uno, amene ndidzawasonkhanitsa mu nthawi yake pa kupindula kwa Ziyoni, kudzera mu chida chanu.
3Â Kotero, ndikofunikira kuti mudziwane ndi anthu a mumzinda uno, monga mudzatsogozedwa, ndi monga chidzapatsidwa kwa inu.
4 Ndipo zidzachitika mu nthawi yake kuti ndidzapereka mzinda uwu m’manja mwanu, kuti mudzakhala ndi mphamvu pa iwo, kotero kuti iwo sadzapeza magawo obisika anu; ndipo chuma chake cha golide ndi siliva chidzakhala chanu.
5Â Musadere nkhawa za ngongole zanu, pakuti ndidzakupatsani inu mphamvu yakubweza.
6Â Musadere nkhawa zokhudza Ziyoni, pakuti ndidzamuchitira chifundo.
7 Khalanibe m’malo ano, ndi m’madera ozungulira;
8Â Ndipo malo amene kuli chifuniro changa kuti inu mukhale, makamaka, adzasonyezedwa kwa inu mwa mtendere ndi mphamvu ya Mzimu wanga, umene udzasefukira kwa inu.
9Â Malo awa mutha kuwapeza mobwereka. Ndipo funsani mosamala zokhudzana ndi anthu akale kwambiri ndi oyambitsa mzinda uwu;
10Â Pakuti pali chuma chochuluka kuposa chimodzi cha inu mumzinda uno.
11Â Kotero, khalani ochenjera monga njoka, koma opanda tchimo; ndipo ndidzakonza zinthu zonse pa ubwino wanu, mofulumira monga mungathe kuzilandira. Ameni.