Gawo 59
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, mu Ziyoni, Jackson County, Missouri, Ogasiti 7, 1831. Vumbulutsoli lisadachitike, malowo adapatulidwa, monga m’mene Ambuye adalamulira, komanso malo a kachisi wamtsogolo adapatulidwa. Pa tsiku limene vumbulutso ili lidalandiridwa, Polly Knight, mkazi wa Joseph Knight Sr., adamwalira, membala woyamba wa Mpingo kufa mu Ziyoni. Mamembala oyambilira adatchula vumbulutso ili ngati “kulangiza Oyera Mtima kusunga sabata ndi momwe angasalire ndi kupemphera.”
1–4, Oyera Mtima okhulupirika mu Ziyoni adzadalitsidwa; 5–8, Iwo akuyenera kukonda ndi kutumikira Ambuye ndi kusunga malamulo Ake; 9–19, Pa kusunga tsiku la Ambuye kukhala loyera, Oyera Mtima amadalitsidwa kuthupi ndi kuuzimu; 20–24, Olungama alonjezedwa mtendere m’dziko lino ndi moyo wosatha m’dziko lilinkudza.
1 Taonani, odala, atero Ambuye, ali iwo amene abwera ku dziko lino ndi diso lolunjika ku ulemelero wanga, molingana ndi malamulo anga.
2 Pakuti iwo amene ali ndi moyo adzalandira dziko lapansi, ndipo iwo akufa adzapumula ku ntchito zawo zonse, ndipo ntchito zawo zidzawatsatira iwo; ndipo adzalandira korona m’ nyumba za Atate anga, zomwe ndidawakonzera iwo.
3 Inde, odala ali awo amene mapazi awo amaima pa dziko la Ziyoni, amene amvera uthenga wanga wabwino; pakuti adzalandira mphotho yawo zinthu zabwino za dziko lapansi, ndipo idzatulutsa mphamvu zake.
4 Ndipo iwo adzavekedwanso korona wa madalitso ochokera kumwamba, inde, ndi malamulo osawerengeka, ndi mavumbulutso mu nthawi yawo—iwo amene ali okhulupirika ndi akhama pamaso panga.
5 Kotero, ndikupereka kwa iwo lamulo, kunena motere: Udzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, nzeru zako zonse, ndi nyonga zako zonse; ndipo m’dzina la Yesu Khristu udzamtumikira iye.
6 Udzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. Usabe; kapena kuchita chigololo, kapena kupha, kapena kuchita china chonga icho.
7 Udziyamika Ambuye Mulungu wako mu zinthu zonse.
8 Udzipereka nsembe kwa Ambuye Mulungu wako mu chilungamo, ngakhale ya mtima wosweka ndi mzimu wolapa.
9 Ndipo kuti udzisungire wekha kwathunthu wosadetsedwa ndi dziko lapansi, udzapita ku nyumba ya pemphero ndi kupereka masakramenti ako pa tsiku langa loyera;
10 Pakuti indetu ili ndi tsiku loikidwiratu kwa inu kuti mupumule ku ntchito zanu, ndi kupereka mapemphero anu kwa Wam’mwambamwamba;
11 Komabe zowinda zako zidzaperekedwa m’chilungamo masiku onse ndi nthawi zonse;
12 Koma kumbukirani kuti pa ili, tsiku la Ambuye, mudzapereka zopereka zanu ndi masakramenti anu kwa Wam’mwambamwamba, ndi kuulula machimo anu kwa abale anu, ndi pamaso pa Ambuye.
13 Ndipo pa tsiku ili inu musachite chinthu china, koma lolani chakudya chanu chikonzekeredwe ndi mtima umodzi kuti kusala kudya kwanu kukhale kwangwiro, kapena, m’mawu ena, kuti chisangalalo chanu chikhale chodzadza.
14 Indetu, uku ndi kusala ndi kupemphera, kapena m’mawu ena, chisangalalo ndi pemphero.
15 Ndipo pamene mukuchita zinthu izi ndi chiyamiko, ndi mitima ndi nkhope zokondwera, osati ndi kuseka kwambiri, pakuti ichi ndi tchimo, koma ndi mtima wokondwera ndi nkhope yokondwera—
16 Indetu ndinena, kuti pamene mukuchita ichi, chidzalo cha dziko lapansi ndi chanu, zilombo za m’thengo ndi mbalame za m’mlengalenga, ndi zimene zimakwera pamitengo ndi kuyenda pa dziko lapansi;
17 Inde, ndi zitsamba, ndi zabwino zochokera m’nthaka, kapena za chakudya, kapena zobvala, kapena za nyumba, kapena za nkhokwe, kapena za minda ya zipatso, kapena za m’mdimba, kapena za minda ya mpesa;
18 Inde, zinthu zonse zimene zimachokera ku nthaka, m’nyengo yake, zapangidwa kuti zipindule ndi kugwiritsidwa ntchito kwa munthu, kuti zikondweretse diso ndi kusangalatsa mtima;
19 Inde, za chakudya ndi chovala, za kukoma ndi kununkhira, kuti zilimbikitse thupi ndi kupulumutsa moyo.
20 Ndipo zimakondweretsa Mulungu kuti wapereka zinthu zonsezi kwa munthu; pakuti chifukwa cha ichi zidapangidwa kuti zigwiritsidwe ntchito, ndi chiweruzo, osati mochulutsa, kapena molanda.
21 Ndipo mu kanthu kalikonse munthu sakhumudwitsa Mulungu, kapena mkwiyo wake suyaka pa wina aliyense, kupatula iwo amene savomereza dzanja lake mu zinthu zonse, ndipo samvera malamulo ake.
22 Taonani, izi zili molingana ndi chilamulo ndi aneneri; kotero, musandivutitsenso ine zokhudzana ndi nkhaniyi.
23 Koma phunzirani kuti iye amene amachita ntchito za chilungamo adzalandira mphotho yake, ngakhale mtendere m’dziko lino lapansi, ndi moyo wosatha m’dziko lilinkudza.
24 Ine, Ambuye, ndayankhula izi, ndipo Mzimu ukuchitira umboni. Ameni.