Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 34


Gawo 34

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Orson Pratt, ku Fayette, New York, Novembara 4, 1830. M’bale Pratt adali ndi zaka khumi ndi zisanu ndi zinayi zakubadwa panthawiyo. Iye adali atatembenuzidwa ndi kubatizidwa pamene adayamba kumva kulalikidwa kwa uthenga wabwino wobwenzeretsedwa ndi mkulu wake, Parley P. Pratt, milungu isanu ndi umodzi yapitayo. Vumbulutso ili lidalandiridwa mnyumba ya Peter Whitmer Sr’.

1–4, Okhulupirika amakhala ana a Mulungu kudzera mu Chitetezero; 5–9, Kulalikira kwa uthenga wabwino kumakonzekeretsa njira ya Kudza Kwachiwiri; 10–12, Ulosi umadza ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.

1 Mwana wanga Orson, mvetsera ndi kumva ndi kuona chimene ine, Ambuye Mulungu, ndi dzanena kwa iwe, ngakhale Yesu Khristu Muwomboli wako;

2 Kuunika ndi moyo wa dziko lapansi, kuunika kumene kumawalira mumdima, ndipo mdima sumakuzindikira;

3 Amene adakonda dziko lapansi kotero kuti adapereka moyo wake wa iye yekha, kuti onse amene adzakhulupilire akathe kukhala ana a Mulungu. Kotero ndiwe mwana wanga;

4 Ndipo odala ndiwe chifukwa wakhulupilira;

5 Ndipo ndiwe odala kwambiri chifukwa waitanidwa ndi ine kuti ukalalikire uthenga wanga—

6 Kuti ukakweze mawu ako ngati ndi phokoso la lipenga, monse motalika ndi mofuula, ndi kufuula kulapa kwa m’badwo wopotoka ndi wokhota, kukonzekera njira ya Ambuye kwa kudza kwake kwachiwiri.

7 Pakuti taona, indetu, indetu, ndinena kwa iwe, nthawi ili pafupi pomwe ine ndidzabwera mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.

8 Ndipo lidzakhala tsiku lalikulu pa nthawi ya kudza kwanga, pakuti mitundu yonse idzanjenjemera.

9 Koma lisadadze tsiku lalikululo, dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi udzasanduka mwazi; ndipo nyenyezi zidzakana kuwala kwawo, ndipo zina zidzagwa, ndipo ziwonongeko zazikulu zikuyembekezera oipa.

10 Kotero, kweza mawu ako ndipo usalekelere, pakuti Ambuye Mulungu wanena; kotero nenera, ndipo chidzapatsidwa ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.

11 Ndipo ngati uli wokhulupirika, taona, ine ndili ndi iwe kufikira ndidzabwera—

12 Ndipo indetu, indetu, ndinena kwa iwe, ndidza msanga. Ine ndine Mbuye wako ndi Muwomboli wako. Ngakhale zili choncho. Ameni.