Gawo 115
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Far West, Missouri, Epulo 26, 1838, kuzindikiritsa dzina la Mpingo monga Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Vumbulutsoli lidavomerezanso Far West ngati malo atsopano osonkhanirana mu dziko la Ziyoni.
1–4, Ambuye atchula mpingo Wake Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza; 5–6, Ziyoni ndi masiteki ake ndi malo a chitetezo ndi kothawira kwa Oyera mtima; 7–16, Oyera mtima kulamulidwa kumanga nyumba ya Ambuye ku Far West; 17–19, Joseph Smith ali ndi mafungulo a ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi.
1Â Indetu akutero Ambuye kwa iwe, mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndiponso mtumiki wanga Sidney Rigdon, ndiponso mtumiki wanga Hyrum Smith, ndi aphungu anu amene ali ndipo adzasankhidwa kuyambira pano;
2Â Ndiponso kwa iwe, mtumiki wanga Edward Partridge, ndi aphungu ake;
3 Ndiponso kwa atumiki anga okhulupirika amene ali alangizi aakulu a mpingo wanga mu Ziyoni, pakuti momwemo udzatchedwa, ndipo kwa akulu ndi anthu onse a mpingo wanga wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza, obalalitsidwa ponseponse pa dziko lonse lapansi;
4 Pakuti motero mpingo wanga udzatchedwa mu masiku otsiriza, ngakhale Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza.
5Â Indetu, ndikunena kwa inu nonse: Dzukani ndi kuwalitsa, kuti kuwala kwanu kuthe kukhala mbendera kwa maiko;
6Â Ndipo kuti kusonkhana pamodzi pa dziko la Ziyoni, ndi pa masiteki ake, kukathe kukhala pa chitetezero, ndi kothawira ku namondwe, ndi ku mkwiyo pamene udzatsanulidwa kopanda kusakaniza pa dziko lapansi.
7Â Lolani mzinda wa Far West, ukhale malo woyera ndi wopatulika kwa ine; ndipo udzatchedwa oyera kwambiri, pakuti pamalo pomwe inu mwaima ndi poyera.
8Â Kotero, ndikukulamulani inu kuti mumange nyumba kwa ine, yakusonkhanirana pamodzi kwa oyera mtima anga, kuti iwo akathe kundilambira ine.
9Â Ndipo lolani kukhale chiyambi cha ntchito imeneyi, ndi maziko, ndi ntchito yokonzekera, chilimwe chikudzachi;
10Â Ndipo lolani chiyambi chichitike pa tsiku lachinayi la Julayi akubwerayu; ndipo kuyambira pa nthawi imeneyi kupita chitsogolo lolani anthu anga agwire ntchito mwakhama kumanga nyumba ku dzina langa;
11Â Ndipo mu chaka chimodzi kuchokera pa tsiku ili lolani iwo ayambirenso kuika maziko a nyumba yanga.
12Â Motero aloleni iwo kuchokera pa nthawi imeneyo kupita mtsogolo agwire ntchito molimbika kufikira itamalizidwa, kuchokera pa mwala wapangodya yake kufikira pamwamba pake, kufikira sikudzatsalira kanthu kamene sikadamalizidwe.
13Â Indetu ndinena kwa inu, musalore mtumiki wanga Joseph, kapena mtumiki wanga Sidney, kapena mtumiki wanga Hyrum, alowe mu ngongole zina zomangira nyumba ku dzina langa;
14Â Koma lolani nyumba imangidwe ku dzina langa molingana ndi chitsanzo chimene ine ndidzaonetsera kwa iwo.
15Â Ndipo ngati anthu anga saimanga iyo molingana ndi chitsanzo chimene ine ndidzaonetsere kwa atsogoleri awo, sindidzaivomereza iyo pa manja awo.
16Â Koma ngati anthu angaimange iyo molingana ndi machitidwe amene ine ndidzaonetsera kwa atsogoleri awo, ngakhale mtumiki wanga Joseph ndi aphungu ake, pamenepo ndidzaivomereza iyo pa manja a anthu anga.
17Â Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, ndi chifuniro changa kuti mzinda wa Far West umangidwe mwachangu mwa kosonkhana kwa oyera mtima anga;
18Â Ndiponso kuti malo ena asankhidwe a masiteki mu madera ozungulira, monga adzaonetseredwa kwa mtumiki wanga Joseph, ku nthawi ndi nthawi.
19Â Pakuti taonani, ndidzakhala naye, ndipo ndidzamupatula iye pamaso pa anthu; pakuti kwa iye ndapereka mafungulo a ufumu ndi utumiki. Ngakhale choncho. Ameni.