Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 14


Gawo 14

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa David Whitmer, ku Fayette, New York, Juni 1829. Banja la a Whitmer lidakhala ndi chidwi kwambiri mu kumasulira kwa Buku la Mormoni. Mneneri adakhazikitsa kokhala kwake ku nyumba ya Peter Whitner Sr,. Kumene adakhalako kufikira ntchito yomasulira idafika kumapeto ndipo ufulu wokopera buku lokudzali udapezeka. Ana atatu a Whitmer, aliyense atalandira umboni wa zoona za ntchitoyi, adakhala okhudzidwa kwambiri pa nkhani ya maudindo awo. Vumbulutso ili ndi awiri otsatira (magawoĀ 15ndi16) adaperekedwa mu yankho ku funso kudzera mu Urimu ndi Tumimu. David Whitmer pambuyo pake adakhala m’modzi mwa Mboni Zitatu za Buku la Mormoni.

1–6, Ogwira ntchito m’munda wa mpesa adzapeza chipulumutso; 7–8, Moyo wamuyaya ndi mphatso yaikulu mwa mphatso za Mulungu; 9–11, Khristu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

1 Ntchito yaikulu ndi yodabwitsa yatsala pang’ono kubwera kwa ana a anthu.

2 Taona, ndine Mulungu; tchera khutu ku mawu anga, amene ali achangu ndi amphamvu, akuthwa kuposa lupanga lakuthwa konsekonse, mpaka kugawanitsa pakati pa zonse fupa ndi mafuta am’mafupa; kotero mvetsera mawu anga.

3 Taona, munda wacha kale kuti mukololedwe; kotero, amene akhumbira kukolora, mlekeni aponye chikwakwa chake mwa mphamvu, kuti akolore pamene tsiku lidakalipo, kuti akadzisungire ku moyo wake chipulumutso chosatha mu ufumu wa Mulungu.

4 Inde, aliyense amene adzaponya chikwakwa chake ndi kukolora, yemweyo waitanidwa ndi Mulungu.

5 Kotero, ngati udzapempha kwa ine udzalandira; ngati udzagogoda chidzatsekulidwa kwa iwe.

6 Funafuna kubweretsa ndi kukhazikitsa Ziyoni wanga. Sunga malamulo anga mu zinthu zonse.

7 Ndipo, ngati udzasunga malamulo anga ndi kupilira kufikira kumapeto udzakhala ndi moyo wamuyaya, umene ndi mphatso yaikulu mwa mphatso zonse za Mulungu.

8 Ndipo zidzachitika, kuti ngati iwe udzapempha Atate mu dzina langa, mu chikhulupiliro kukhulupilira, udzalandira Mzimu Woyera, umene umapereka mawu, kuti ukathe kuima ngati mboni ya zinthu zimene iwe udzazimva ndi kuziona, ndiponso kuti ukathe kulalikira kulapa ku m’badwo uno.

9 Taona, ndine Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo, amene ndidalenga kumwamba ndi dziko lapansi, kuunika kumene sikungabisidwe mu mdima.

10 Kotero, ndikuyenera kubweretsa chidzalo cha uthenga wanga wabwino kuchokera kwa Amitundu kupita ku nyumba ya Israeli.

11 Ndipo taona, ndiwe David, ndipo iwe waitanidwa kuti uthandizire; chimene ngati ungachite, ndipo ndi kukhulupirika, udzadalitsidwa zonse muuzimu ndi kuthupi, ndipo yaikulu idzakhala mphotho yako. Ameni.