Gawo 33
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Ezra Thayre ndi Northrop Sweet, ku Fayette, New York, Okotobara 1830. Mu malonje a vumbulutso ili, mbiri ya Joseph Smith imatsimikizira kuti “Ambuye… Ndi okonzeka konse kuphunzitsa amene amafunafuna mwakhama mu chikhulupiliro.”
1–4, Ogwira ntchito akuitanidwa kukalengeza uthenga wabwino mu ola la khumi ndi limodzi; 5–6, Mpingo wakhazikitsidwa, ndipo osankhidwa akuyenera kusonkhanitsidwa; 7–10, Lapani, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira; 11–15, Mpingo wamangidwa pa thanthwe la uthenga wabwino; 16–18, Konzekerani pa kubwera kwa Mkwati.
1 Taonani, ndikunena kwa inu atumiki anga Ezra ndi Northrop, tsegulani makutu ndi kumvetsera ku mawu a Ambuye Mulungu wanu, amene mawu ake ndi akuthwa ndi amphamvu, okuthwa kuposa lumo lakuthwa konsekonse, lakugawanitsa pakati pa zonse fupa ndi mafuta a m’mafupa, moyo ndi mzimu; ndipo ndi wozindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.
2 Pakuti, indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti mudaitanidwa kuti mukweze mawu anu monga ndi phokoso la lipenga, kulengeza uthenga wanga wabwino kwa m’badwo wokhota ndi wopotoka.
3 Pakuti taonani, munda wacha kale kuti mukololedwe; ndipo ndi ola la khumi ndi limodzi, ndi nthawi yomaliza imene ndidzaitana ogwira ntchito mu munda wampesa wanga.
4 Ndipo munda wampesa wanga wakhala wovunda mbali zonse; ndipo palibe amene akuchita bwino kupatula ochepa; ndipo iwo akulakwitsa mu njira zambiri chifukwa cha zaunsembe zolakwika, onse okhala ndi malingaliro woipa.
5 Ndipo indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti mpingo uwu ndaukhazikitsa ndipo ndidawuitana kuchokera m’chipululu.
6 Ndipo momwemonso ndidzasonkhanitsa osankhidwa anga kuchokera ku ngodya zinayi za dziko lapansi, ngakhale ambiri amene adzakhulupilira mwa ine, ndi kumvera ku mawu anga.
7 Inde, indetu, indetu, ndikunena kwa inu, kuti munda wacha kale kuti mukololedwe; kotero, ponyani zikwakwa zanu, ndi kukolora ndi mphamvu, malingaliro ndi nyonga zanu zonse.
8 Tsegulani pakamwa panu ndipo padzakhutira, ndipo inu mudzakhala monga ngati Nefi wakale, amene adayenda kuchokera ku Yerusalemu m’chipululu.
9 Inde, tsegulani pakamwa panu, ndipo musasiye, ndipo mudzalemedwa ndi mitolo pamsana panu, pakuti onani, ndili nanu,
10 Inde, tsegulani pakamwa panu, ndipo padzakhutira, nati: Lapani, lapani, ndipo konzani njira ya Ambuye, ndi kukhonza njira zake zolunjika; pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira;
11 Inde, lapani ndi kubatizidwa, aliyense wa inu, ku chikhululukiro cha machimo anu; inde, batizidwani ngakhale ndi madzi, ndipo kenako kudzabwera ubatizo wa moto ndi wa Mzimu Woyera.
12 Taonani, indetu indetu, ndinena kwa inu, uwu ndi uthenga wanga wabwino; ndipo kumbukirani kuti iwo adzakhala ndi chikhulupiliro mwa ine kapena sangathe mwa njira ina kupulumutsidwa;
13 Ndipo pa thanthwe ili ndidzamanga mpingo wanga; inde, pa thanthwe ili inu mwamangidwapo, ndipo ngati inu mupitiriza, zipata za gahena sizidzapambana motsutsana nanu.
14 Ndipo inu mudzakumbukira mfundo ndi mapangano a mpingo kuzisunga.
15 Ndipo aliyense okhala ndi chikhulupiliro mudza mutsimikizira mu mpingo wanga, posanjikiza manja, ndipo ndidzapereka mphatso ya Mzimu Woyera pa iwo.
16 Ndipo Buku la Mormoni ndi malembo oyera aperekedwa ndi ine kuti akuphunzitseni; ndipo mphamvu ya Mzimu wanga imafulumizitsa zinthu zonse.
17 Kotero, khalani okhulupirika, kupemphera nthawi zonse, kukhala ndi nyali zanu zokonzeka ndi kuyaka, ndi mafuta anu, kuti mukakhale okonzeka pa kubwera kwa Mkwati—
18 Pakuti taonani, indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ndikubwera msanga. Ngakhale zili choncho. Ameni.