Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 121


Mutu 121

Pemphero ndi mauneneri otengedwa kuchokera pa zikalata ziwiri ku Mpingo zolembedwa ndi Joseph Smith Mneneri pamene iye adali mkaidi mu ndende ya Liberty, Missiouri, yoyamba idalembedwa pa Malitchi 20, 1839, ndipo yachiwiriyi idalembedwa cha pakatikati pa Malitchi 22. Mneneri ndi abwenzi ake angapo adali atakhala mndende kwa miyezi. Mapempho awo ndi madandaulo awo kwa adindo aboma osiyanasiyana adalephera kuwabweretsera iwo chithandizo.

1–6, Mneneri achondelera Ambuye chifukwa cha Oyera mtima ozunzika; 7–10, Ambuye ayankhula mtendere kwa iye; 11–17, Otembeleledwa ndi iwo onse amene amakweza mfuu wabodza wa zolakwa motsutsana ndi anthu a Ambuye; 18–25, Iwo sadzakhala ndi ufulu wa unsembe ndipo adzalangidwa; 26–32, Mavumbulutso a ulemelero alonjezedwa kwa iwo amene amapilira molimba mtima; 33–40, Chifukwa chimene ambiri ndi oitanidwa koma ochepa ndi osankhidwa; 41–46, Unsembe ukuyenera kugwiritsidwa ntchito pa chilungamo chokha.

1 O Mulungu, Kodi mulikuti? Nanga lilikuti hema lomwe limaphimba pobisalira panu?

2 Kodi dzanja lanu lidzaletsedwa mpaka liti, ndipo diso lanu, inde diso lanu loyera, kuyang’anira kuchokera kumwamba kwamuyaya zolakwa za anthu anu ndi za atumiki anu, ndi khutu lanu kupyozedwa ndi kulira kwawo?

3 Inde, O Ambuye, mpaka liti iwo adzazunzika zolakwa izi ndi kupondelezedwa kosavomelezeka, mtima wanu usadafewetsedwe kwa iwo, ndipo zipyso zanu zisunthidwe ndi kuwachitira chifundo iwo?

4 O Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, wolenga kumwamba, dziko lapansi ndi nyanja, ndi zinthu zonse zili m’menemo, ndi amene mumalamulira ndi kugonjetsa mdyelekezi, ndi mdima ndi usiku ulamuliro wa Sheoli—tambasulani dzanja lanu; diso lanu lipyoze; hema lanu livundukulidwe; pobisala panu pasaphimbidwenso; khutu lanu limvere; mtima wanu ufewetsedwe; ndipo zimpsyo zanu zisunthidwe ndi kutichitira chifundo ife.

5 Mkwiyo wanu uyake motsutsana ndi adani athu; ndipo, mu ukali wa mtima wanu, ndi lupanga lanu tibwenzereni ife zolakwa zathu.

6 Kumbukurani kuzunzika kwa oyera mtima, O Mulungu wathu; ndipo atumiki anu adzakondwera mu dzina lanu kwamuyaya.

7 Mwana wanga, mtendere ukhale pa moyo wako; mazunzo ako ndi masautso ako adzakhala koma kwa kamphindi kochepa;

8 Ndipo kenako, ngati iwe udzawapilira bwino, Mulungu adzakukweza iwe pamwamba; udzapambana pa adani ako onse.

9 Abwenzi ako akuima nawe, ndipo iwo adzakunyadiranso iwe ndi mitima yofunda ndi manja aubwenzi.

10 Iwe siudafike ngati Yobu; abwenzi ako sakutsutsana nawe, kapena kukunenera iwe cholakwa, monga momwe adachitira Yobu.

11 Ndipo iwo amene akukuzenga iwe ndi zolakwa, chiyembekezo chawo chidzatenthedwa, ndipo zofuna zawo zidzasungunuka ngati mame ouma amasungunukira pamaso pa malawi a kuwala kwa dzuwa;

12 Ndiponso kuti Mulungu waika dzanja lake ndi chisindikizo chosintha nthawi ndi nyengo, ndi kuchititsa khungu malingaliro awo, kuti iwo asakathe kumvetsa machitidwe ake ozizwitsa; kuti iye akathe kutsimikizira iwonso ndi kuwagwira iwo mu chinyengo chawo;

13 Ndiponso chifukwa mitima yawo ndiyachinyengo, ndipo zinthu zimene iwo akufuna kubweretsa pa ena, ndi kukonda kupangitsa anzawo kuvutika, zidzawabwelera pa iwo eni moposera kwambiri;

14 Kuti iwo akathe kukhumudwitsidwanso, ndipo ziyembekezo zawo zikathe kudulidwa;

15 Ndipo osati zaka zambiri kuchokera pano, zomwe iwo ndi ana awo adzasesedwa kuchokera pansi pa thambo, atero Mulungu, kuti palibe mmodzi wa iwo amene adzasiyidwe kuima pa khomalo.

16 Otembeleredwa ndi iwo onse amene adzakweza chidendene chawo motsutsana ndi odzodzedwa anga, atero Ambuye, ndi kulira kuti achimwa pamene iwo sadachimwe pamaso panga, atero Ambuye, koma achita icho chomwe chili choyenera pamaso panga, ndi chomwe ine ndalamula iwo.

17 Koma iwo amene amalira zolakwa amachita izi chifukwa iwo ali atumiki a tchimo, ndipo ndi ana a kusamvera iwo eni.

18 Ndipo iwo amene alumbira bodza motsutsana ndi atumiki anga, kuti iwo akathe kuwabweretsa iwo mu ukapolo ndi imfa—

19 Tsoka kwa iwo; chifukwa iwo alakwira tiana tanga iwo adzadulidwa kuchokera ku miyambo ya nyumba yanga.

20 Nsengwa zawo sizidzadzadza, nyumba zawo ndi nkhokwe zawo zidzawonongeka, ndipo iwo eni adzanyozedwa ndi iwo amene ankawatamandira.

21 Iwo sadzakhala ndi ufulu wa unsembe, ngakhale ana awo pambuyo pawo kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

22 kukadakhala kwabwino kwa iwo kuti mwala wamphero ukolowekedwe m’khosi mwawo ndi kumizidwa mu kuya kwa nyanja.

23 Tsoka kwa iwo onse amene amavutitsa anthu anga, ndi kuwathamangitsa, ndi kuwapha, ndi kuchitira umboni otsutsana nawo, atero Ambuye Wamakamu; m’badwo wa njoka sudzathawa chilango cha gahena.

24 Taonani, maso anga amaona ndi kudziwa ntchito zawo zonse, ndipo ndasungira iwo chiweruzo chachangu mu nyengo yako, kwa iwo onse;

25 Pakuti pali nthawi yoikidwa kwa munthu aliyense, molingana ndi ntchito zake zidzakhalire.

26 Mulungu adzapereka kwa inu chidziwitso mwa Mzimu Woyera wake, inde, mwa mphatso yosaneneka ya Mzimu Woyera, imene sidavumbulutsidwe chiyambire dziko lapansi kufikira tsopano;

27 Imene makolo athu adayembekezera mwa chidwi chachiyembekezo kuti idzavumbulutsidwa mu nthawi zomaliza, imene malingaliro awo adalozedwerako ndi angelo, monga zidasungidwira pa chidzalo cha ulemelero wawo;

28 Nthawi ikudza imene palibe chimene chidzabisidwe, kaya kuli Mulungu m’modzi kapena milungu yambiri, zidzaonetseredwa.

29 Mipando ya chifumu ndi mautsogoleri onse, maulamuliro ndi mphamvu, zidzavumbulutsidwa ndi kuikidwa pa onse amene apilira molimba mtima chifukwa cha uthenga wabwino wa Yesu Khristu.

30 Ndiponso, ngati pali malire oyikidwa kumwamba kapena kunyanja, kapena ku nthaka yowuma, kapena ku dzuwa, mwezi, kapena nyenyezi—

31 Nthawi zonse za kuyenda kwawo, masiku awo onse oikidwa, miyezi, ndi zaka, ndi masiku onse a masiku awo, miyezi, ndi zaka, ndi maulemelero awo onse, malamulo, ndi nthawi zoikika, zidzavumbulutsidwa mu masiku a nyengo ya chidzalo cha nthawi—

32 Molingana ndi icho chimene chidzadzodzedwa pakati pa Bwalo la Mulungu Wamuyaya wa milungu ina yonse dziko lino lapansi lisadakhale, kuti zikuyenera kusungidwa kufikira chimaliziro ndi mathero ake, pamene munthu aliyense adzalowa mpumulo wake wamuyaya.

33 Kodi madzi oyendayenda angakhale odetsedwa kwa nthawi yayitali bwanji? Ndi mphamvu yanji imene idzaletsa kumwamba? Momwemonso munthu angathe kutambasula nkono wake waung’ono kuti aimitse mtsinje wa Missouri kuyenda munjira yake yoyikidwiratu, kapena kuwutembenuzira kumtunda, ngati kusokoneza Wamphamvu zonse kuti atsanulire chidziwitso kuchokera kumwamba pa mitu ya Oyera Mtima M’masiku Otsiriza.

34 Taonani, alipo ambiri oitanidwa, koma ochepa ndiwo osankhidwa. Nanga n’chifukwa chiyani iwo sadasankhidwe?

35 Chifukwa mitima yawo yakhazikika kwambiri pa zinthu za dziko lapansili, ndipo amafuna maulemu a anthu, mpaka iwo saphunzirapo phunziro limodzi ili—

36 Kuti maufulu a unsembe ndi olumikizidwa mosasiyanitsika ndi mphamvu zakumwamba, ndipo kuti mphamvu zakumwamba sizingalamulidwe kapena kugwiridwa kokha pa mfundo za chilungamo.

37 Kuti izo ziperekedwe kwa ife, ndi zoona; koma pamene tiyamba kubisa machimo athu, kapena kusangalatsa kunyada kwathu, zilakolako zathu zachabe, kapena kulamulira kapena kukakamiza pa miyoyo ya ana a anthu, mu mulingo uliwonse wa kusalungama, taonani, kumwamba kudzadzichotsa kokha; Mzimu wa Ambuye udzakwiya; ndipo pamene iwo wachoka, Ameni ku unsembe kapena ulamuliro wa munthu ameneyo.

38 Taonani, iye asadadziwe, wasiyidwa kwa iye yekha, kukantha dzisonga, kuzunza oyera mtima, ndi kulimbana ndi Mulungu.

39 Ife taphunzira mwa zokumana nazo zachisoni kuti ndi chilengedwe ndi chikhalidwe cha pafupifupi anthu onse, akangolandira ka ulamuliro kochepa, monga momwe amaganizira, nthawi yomweyo iwo amayamba kuchita ulamuliro osalungama.

40 N’chifukwa chake ambiri ndiwoitanidwa, koma ochepa ndi osankhidwa.

41 Palibe mphamvu kapena chikoka chomwe chingasungidwe kapena kuyenera kusungidwa mwa mphamvu ya unsembe, kukopa kokha, mwa kupilira, mwa kudekha ndi chifatso, ndi mwa chikondi chosanamizira;

42 Mwa kukoma mtima, ndi chidziwitso choyera, chimene chidzakulitsa kwakukulu moyo popanda chinyengo, ndipo popanda kunyenga—

43 Chidzudzulo chokudza munthawi yake champhamvu, pamene wasunthidwa ndi Mzimu Woyera; ndipo kenako kuonetsa pambuyo pake kukula kwa chikondi kwa iye amene wamudzudzulayo, kuopa kuti angakutenge iwe ngati mdani wake;

44 Kuti iye akathe kudziwa kuti kukhulupirika kwako ndi kolimba kuposa zingwe za imfa.

45 Zimpsyo zanu zidzadze ndi chikondi kwa anthu onse, ndi abale achikhulupiliro, ndipo ukoma ukometse malingaliro anu mosalekeza, kenako chikhulupiliro chanu chidzakula mphamvu pamaso pa Mulungu; ndipo chiphunzitso cha unsembe chidzafulura pa moyo wanu ngati mame ochokera kumwamba.

46 Mzimu Woyera udzakhala bwenzi lanu lokhazikika, ndipo ndodo yanu yachifumu ndodo yosasintha ya chilungamo ndi choonadi; ndipo ulamuliro wanu udzakhala ulamuliro wosatha, ndipo popanda njira zokakamiza udzasefukira mwa inu ku nthawi za nthawi zosatha.