Gawo 106
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Novembala 25, 1834. Vumbulutso ili likupita kwa Warren A. Cowdery, mchimwene wake wamkulu wa Oliver Cowdery.
1–3Warren A. Cowdery aitanidwa ngati mdindo wotsogolera m’deralo; 4–5, Kudza Kwachiwiri sikudzawapeza ana a kuunika ngati mbala; 6–8, Madalitso aakulu amatsatira utumiki wokhulupirika mu Mpingo.
1 Ndi chifuniro changa kuti mtumiki wanga Warren A. Cowdery akuyenera kusankhidwa ndi kudzodzedwa wansembe wamkulu wotsogolera mpingo wanga, m’dziko la Ufulu ndi zigawo zozungulira;
2 Ndipo akuyenera kulalikira uthenga wabwino wanga wamuyaya, ndi kukweza mawu ake ndi kuchenjeza anthu, osati m’malo ake okha, koma m’madera oyandikana nawo;
3 Ndi kupereka nthawi yake yonse ku maitanidwe a pamwamba ndi oyera awa, amene tsopano ndikupereka kwa iye, kufunafuna mwakhama ufumu wa kumwamba ndi chilungamo chake, ndipo zinthu zonse zofunika zidzawonjezedwa m’menemo; pakuti wantchito akuyenera kulandira malipiro ake.
4 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, kudza kwa Ambuye kwayandikira, ndipo kudzafikira dziko lapansi monga mbala usiku—
5 Kotero, mangani malamba m’chuuno mwanu, kuti mukathe kukhala ana a kuunika, ndipo tsikulo silidzakupezani ngati mbala.
6Â Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, kudali chimwemwe kumwamba pamene mtumiki wanga Warren adagwada ku ndodo yanga yachifumu, ndipo adadzipatula yekha kuchoka ku ntchito za anthu;
7Â Kotero, wodala ndi mtumiki wanga Warren, chifukwa ndidzamuchitira chifundo; ndipo, posatengela zachabechabe za mumtima mwake, ine ndidzamukweza iye pamene iye adzadzichepetsa pamaso panga.
8 Ndipo ndidzampatsa chisomo ndi chitsimikizo chimene angathe kuima nacho; ndipo ngati apitiriza kukhala mboni yokhulupirika ndi kuunika kwa mpingo ndamukonzera iye korona m’nyumba zokhalamo za Atate anga. Ngakhale choncho. Ameni.