Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 32


Gawo 32

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Parley P. Pratt ndi Ziba Peterson, ku Manchetser, New York, kumayambiliro kwa Okotobala 1830. Chidwi chachikulu ndi zikhumbo zidamveka mwa akulu kulemekeza Alamani, amene madalitso awo oloseledwa mpingo udadziwa kuchokera mu Buku la Mormoni. Zotsatira zake, pembedzero lidachitidwa kuti Ambuye akathe kuonetsa chifuniro Chake kuti kaya akulu atumizidwe panthawiyo kwa mafuko a Chimwenye ya Kumadzulo. Vumbulutsoli lidatsatira.

1–3, Parley P. Pratt ndi Ziba Peterson akuitanidwa kukalalika kwa Alamani ndi kupelekeza Oliver Cowdery ndi Peter Whitmer Jr.; 4–5, Iwo akuyenera kupemphelera kumvetsetsa malembo oyera.

1 Ndipo tsopano zokhudzana ndi mtumiki wanga Parley P. Pratt, taona, ndikunena kwa iye kuti monga ndili moyo ndikufuna kuti iye adzalengeze uthenga wanga wabwino ndi kuphunzira za ine, ndi kukhala wofatsa ndi wodzichepetsa mumtima.

2 Ndipo icho chimene ndachikhazikitsa mwa iye ndi chakuti iye adzapite ndi atumiki anga, Oliver Cowdery ndi Peter Whitmer, Jun., m’chipululu pakati pa Alamani.

3 Ndiponso Ziba Peterson adzapita nawo; ndipo Ine mwini ndidzapita nawo ndi kukhala pakati pawo; ndipo ndine nkhoswe yawo kwa Atate, ndipo palibe chidzapambane motsutsana nawo.

4 Ndipo iwo adzamvera ku chimene chalembedwa, ndi kusanamizira ku vumbulutso lina lililonse; ndipo iwo adzapemphera nthawi zonse kuti ndidzatambasule zomwezo m’kumvetsetsa kwawo.

5 Ndipo iwo adzamvera kwa mawu awa ndi kusawapeputsa, ndipo ine ndidza wadalitsa iwo. Ameni.