Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 79


Gawo 79

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, Malitchi 12, 1832.

1–4, Jared Carter aitanidwa kukalalikira uthenga wabwino ndi Mtonthozi.

1 Indetu ndinena kwa iwe, kuti ndi chifuniro changa kuti mtumiki wanga Jared Carter apitenso ku maiko a kum’mawa, kuchokera malo ndi malo, ndi kuchokera mzinda ndi mzinda, mu mphamvu ya kudzodza kumene iye wadzodzedwera, kulengeza uthenga wabwino wa chisangalalo chachikulu, ngakhale uthenga wabwino wosatha,

2 Ndipo ndidzatumiza pa iye Mtonthozi, amene adzamuphunzitsa iye choonadi ndi njira imene iye adzapite;

3 Ndipo pamene iye ali wokhulupirika, ndidzamuvekanso iye korona ndi mitolo.

4 Kotero, mtima wako ukhale okondwera, mtumiki wanga Jared Carter, ndipo usaope, atero Ambuye, ngakhale Yesu Khristu. Ameni.