Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 11


Gawo 11

Vumbulutso loperekedwa kudzera kwa Mneneri Joseph Smith kwa mchimwene wake Hyrum Smith, ku Harmony, Pennsylvania, Meyi 1829. Vumbulutsoli lidaperekedwa kudzera mu Urimu ndi Tumimu mu yankho ku pemphero ndi funso la Joseph. Mbiri ya Joseph Smith imanena kuti vumbulutsoli lidalandiridwa pambuyo pa kubwenzeretsedwa kwa Unsembe wa Aroni.

1–6, Ogwira ntchito mu munda wampesa adzapeza chipulumutso; 7–14, Funafunani nzeru, fuulirani kulapa, khulupilirani mwa Mzimu; 15–22, Sungani malamulo, ndi kuwerenga Mawu a Ambuye; 23–27, Musakane mzimu wa vumbulutso ndi wa uneneri; 28–30, Iwo amene alandira Khristu amakhala ana a Mulungu.

1 Ntchito yaikulu ndi yodabwitsa ili pafupi kutulukira kwa ana a anthu.

2 Taona, ndine Mulungu; mvetsera mawu anga, amene ali achangu ndi amphamvu, akuthwa kuposa lupanga lakuthwa konsekonse, mpaka kugawanitsa pakati pa zonse fupa ndi mafuta am’mafupa; kotero mvetsera mawu anga.

3 Taona, munda wacha kale kuti mukololedwe; kotero, amene akhumbira kukolora, mlekeni aponye chikwakwa chake mwa mphamvu, kuti akolore pamene tsiku lidakalipo, kuti akadzisungire ku moyo wake chipulumutso chosatha mu ufumu wa Mulungu.

4 Inde, aliyense amene adzaponya chikwakwa chake ndi kukolora, yemweyo waitanidwa ndi Mulungu.

5 Kotero, ngati udzapempha kwa ine udzalandira; ngati udzagogoda chidzatsekulidwa kwa iwe.

6 Tsopano, monga wapempha, taona, ndinena kwa iwe, sunga malamulo anga, ndi kufunafuna kubweretsa ndi kukhazikitsa cholinga cha Ziyoni.

7 Usafunefune chuma koma nzeru, ndipo, taona, zinsinsi za Mulungu zidzatambasulidwa kwa iwe, ndipo kenako udzapangidwa wachuma. Taona, iye amene ali nawo moyo wosatha ali ndi chuma.

8 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngakhale chomwe ukhumba kwa ine chomwecho chidzachitika kwa iwe; ndipo ngati ukhumba, udzakhala njira ya kuchita zabwino zambiri mu m’badwo uno.

9 Usanene kanthu koma kulapa kwa m’badwo uwu. Sunga malamulo anga, ndi kuthandizira kubweretsa ntchito yanga, molingana ndi malamulo anga, ndipo iwe udzadalitsidwa.

10 Taona, iwe uli ndi mphatso, kapena udzakhala ndi mphatso ngati udzafuna kwa ine mwa chikhulupiliro, ndi mtima oona, kukhulupilira mu mphamvu ya Yesu Khristu, kapena mu mphamvu imene ikuyankhula kwa iwe;

11 Pakuti, taona, ndi ine amene ndikuyankhula; taona, ndine kuunika kumene kumawala mumdima, ndipo ndi mphamvu yanga ndikupereka mawu awa kwa iwe.

12 Ndipo tsopano, indetu, indetu, ndinena kwa iwe, ika chikhulupiliro chako mu Mzimu umene umakutsogolera iwe kuchita zabwino—inde, kuchita chilungamo, kuyenda modzichipetsa, kuweruza mwachilungamo; ndipo uwu ndi mzimu wanga.

13 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ndidzapereka kwa iwe Mzimu wanga, umene udzaunikira malingaliro ako, umene udzadzala moyo wako ndi chisangalalo;

14 Ndipo kenako iwe udzadziwa, kapena mwa ichi udzadziwa, zinthu zonse zomwe iwe ufuna kwa ine, zimene zili zokhudzana ndi zinthu za chilungamo, mwa chikhulupiliro kukhulupira mwa ine chimenecho iwe udzalandira.

15 Taona, Ndikukulamula iwe kuti usaganize kuti waitanidwa kuti ulalike kufikira utainidwa.

16 Yembekeza ka nthawi pang’ono, kufikira utadzakhala ndi mawu anga, thanthwe langa, mpingo wanga ndi uthenga wanga wabwino, kuti ukathe kudziwa motsimikizika za chiphunzitso changa.

17 Ndipo kenako, taona, molingana ndi zofuna zako, inde, ngakhale molingana ndi chikhulupiliro chako zidzachitidwa kwa iwe.

18 Sunga malamulo anga; sunga mtendere wako; pempha Mzimu wanga;

19 Inde, kangamira kwa ine ndi mtima wako onse, kuti ukathandizire mu kubweretsa m’kuwala zinthu zimene zayankhulidwazo—inde, kumasulira kwa ntchito yanga; pilira kufikira utaikwaniritsa.

20 Taona, iyi ndiyo ntchito yako, kusunga malamulo anga, inde, ndi mphamvu, malingaliro ndi nyonga zako zonse.

21 Usafune kulengeza mawu anga, koma choyamba funafuna kulandira mawu anga, ndipo pamenepo lilime lako lidzamasulidwa; kenako, ngati ukufuna, udzakhala ndi Mzimu wanga ndi mawu anga, inde, mphamvu ya Mulungu yakutsimikizira anthu.

22 Koma tsopano sunga mtendere wako; werenga mawu anga amene afika pakati pa ana a anthu, ndiponso werenga mawu amene adzabwere pakati pa ana a anthu, kapena amene tsopano akumasuliridwa, inde, kufikira iwe utalandira zonse zimene ine ndidzapereke kwa ana a anthu a m’badwo uno, ndipo kenako zinthu zonse zidzaonjeredwa pamenepo.

23 Taona iwe ndiwe Hyrum, mwana wanga; funafuna ufumu wa Mulungu, ndipo zinthu zonse zidzaonjezeredwa molingana ndi chimene chili cholungama.

24 Manga pa thanthwe langa, limene ndi uthenga wanga wabwino.

25 Usakane Mzimu wa vumbulutso, kapena mzimu wa uneneri, pakuti tsoka kwa iye amene akana zinthu izi.

26 Kotero, zisunge mu mtima mwako kufikira nthawi imene ili mu nzeru zanga kuti iwe udzapite.

27 Taona, ndikuyankhula kwa onse amene ali ndi zikhumbo zabwino, ndipo aponya chikwakwa chawo kuti akolore.

28 Taonani, ine ndine Yesu Khristu Mwana wa Mulungu. Ndine moyo ndi kuunika kwa dziko lapansi.

29 Ndine yemweyo amene ndidabwera kwa anga ndipo angawo sadandilandire;

30 Koma indetu, indetu, ndinena kwa iwe, kuti pamene ambiri andilandira ine, kwa iwo ndidzawapatsa mphamvu zokhala ana a Mulungu, ngakhale kwa iwo amene akhulupilira pa dzina langa. Ameni.