Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 52


Mutu 52

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa akulu a Mpingo, ku Kirtland, Ohio, Juni 6, 1831. Msonkhano udali utachitika ku Kirtland, kuyambira pa 3 ndipo kutsekera pa 6 Juni. Pa msonkhano madzodzedwe apadera ku udindo wa ansembe aakulu adachitika, ndipo maonetseredwe ena a bodza ndi mizimu yonana adadziwika ndi kudzudzulidwa.

1–2, Msonkhano wotsatira wakonzedwa kuti uchitikire ku Missouri; 3–8, Kusankhidwa kwa akulu ena kuti ayendere limodzi kuchitika; 9–11, Akulu akuyenera kukaphunzitsa zimene atumwi ndi aneneri alemba; 12–21, Iwo amene aunikiridwa ndi Mzimu amabweretsa zipatso za matamando ndi nzeru; 22–44, Akulu osiyanasiyana asankhidwa kuti apite kukalalikira uthenga wabwino pamene akuyenda kupita ku Missouri ku msokhano.

1 Taonani, akutero Ambuye kwa akulu amene iye waitana ndi kuwasankha m’masiku ano otsiriza, ndi mawu a Mzimu wake—

2 Nati: Ine, Ambuye, ndidzadziwitsa kwa inu zimene ndidzafuna kuti inu muchite kuchokera pa nthawi ino kufikira msonkhano wina, umene udzachitikire ku Missouri, pa malo omwe ine ndidzawapatule kwa anthu anga, amene ali otsalira a Yakobo, ndipo iwo amene ali acholowa molingana ndi pangano.

3 Kotero, indetu ndikunena kwa inu, lolani mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon ayambe ulendo mwamsanga pomwe zokonsekera zingapangidwe kuchoka m’makomo mwawo, ndi kupita ku dziko la Missouri,

4 Ndipo pamene iwo ali okhulupirika kwa ine, zidzadziwitsidwa kwa iwo chimene iwo adzachite;

5 Ndiponso, pemene iwo ali okhulupirika, zidzadziwitsidwa kwa iwo dziko la cholowa chanu.

6 Ndipo pamene iwo sali okhulupirika, adzadulidwa, ngakhale monga ndifunira, monga ndaonera bwino.

7 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, lolani mtumiki wanga Lyman Wight ndi mtumiki wanga John Corrill ayambe ulendo mwachangu;

8 Ndiponso mtumiki wanga John Murdock, ndi mtumiki wanga Hyrum Smith, ayambe ulendo wawo ku malo omwewo kudzera ku njira ya Detroit.

9 Ndipo aloleni iwo ayende kuchokera kumeneko kulalikira mawu mu njira, kunena osati zinthu zina kuposa zimene aneneri ndi atumwi azilemba, ndi zimene zaphunzitsidwa iwo ndi Mtonthozi kudzera mu pemphero la chikhulupiliro.

10 Aloleni iwo apite awiri awiri, ndipo motero aloleni alalikire mu njira mu mpingo uliwonse, kubatiza m’madzi, ndi kusanjika manja mphepete mwa madziwo.

11 Pakuti atero Ambuye, ndidzafupikitsa ntchito yanga mu chilungamo, pakuti masiku akudza amene ndidzatumiza chiweruzo ku chipambano.

12 Ndipo lolani mtumiki wanga Lyman Wight achenjere, pakuti Satana akufuna kumupetsa iye ngati mankhusu.

13 Ndipo taonani, iye amene ali wokhulupirika adzapangidwa wolamulira pa zinthu zambiri.

14 Ndiponso, ndidzakupatsani chitsanzo mu zinthu zonse, kuti inu musanyengedwe; pakuti Satana ali kunja kwa dziko, ndipo akupita akunyengeza maiko—

15 Kotero iye amene amapemphera, amene mzimu wake ndi wolapa, yemweyo ali olandilidwa kwa ine ngati iye amvera miyambo yanga.

16 Iye amene akuyankhula, amene mzimu wake uli wolapa, amene mayankhulidwe ake ali wofatsa ndi wolimbitsa, yemweyo ndi wa Mulungu ngati iye amvera miyambo yanga.

17 Ndiponso, iye amene anjenjemera pansi pa mphamvu yanga adzapangidwa kukhala wamphamvu, ndipo adzabala zipatso za matamando ndi nzeru, molingana ndi mavumbulutso ndi choonadi chimene ine ndakupatsani inu,

18 Ndiponso, iye amene wagonjetsedwa ndipo sabeleka zipatso, ngakhale molingana ndi chitsanzo ichi, siwanga.

19 Kotero, mwa chitsanzo ichi mudzadziwa mizimu mu chinachilichonse pansi pa thambo la kumwamba.

20 Ndipo masiku afika; molingana ndi chikhulupiliro cha anthu zidzachitika kwa iwo.

21 Taonani, lamulo ili likuperekedwa kwa akulu onse amene ine ndawasankha.

22 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, lolani mtumiki wanga Thomas B. Marsh ndi mtumiki wanga Ezra Thayre ayambe ulendo wawonso, kulalikira mawu mu njira kwa dziko lomweli.

23 Ndiponso, lolani mtumiki wanga Isaac Morley ndi mtumiki wanga Ezra Booth ayambe ulendo wawo, kulalikiranso mawu mu njira kwa dziko lomweli.

24 Ndiponso, lolani mtumiki wanga Edward Partridge ndi Martin Harris ayambe ulendo wawo ndi mtumiki wanga Sidney Rigdon ndi Joseph Smith, Jun.

25 Lolani atumiki anga David Whitmer ndi Harvey Whitlock nawo ayambenso ulendo wawo, ndi kulalika mu njira kwa dziko lomweli.

26 Ndipo lolani mtumiki wanga Parley P. Pratt ndi Orson Pratt ayambe ulendo wawo, ndi kulalikira mu njira, ngakhale kwa dziko lomweli.

27 Ndipo lolani mtumiki wanga Solomon Hancock ndi Simeon Carter nawo ayambenso ulendo wawo kwa dziko lomweli, ndi kulalikira mu njira.

28 Lolani atumiki anga Edson Fuller ndi Jacob Scott nawo ayambenso ulendo wawo.

29 Lolani atumiki anga Levi W. Hancock ndi Zebedee Coltrin nawo ayambenso ulendo wawo.

30 Lolani atumiki anga Reynolds Cahoon ndi Samuel H. Smith nawo ayambenso ulendo wawo.

31 Lolani atumiki anga Wheeler Baldwin ndi William Carter nawo ayambenso ulendo wawo.

32 Ndipo lolani atumiki anga Newel Knight ndi Selah J. Griffin onse adzodzedwe, ndiponso ayambe ulendo wawo

33 Inde, indetu ndikunena, lolani onsewa ayambe ulendo wawo ku malo amodzi, mu njira zawo zosiyansiyana, ndipo munthu m’modzi sadzamangira pa maziko a wina, ngakhale kuyenda mu njira ya wina.

34 Iye amene ali wokhulupirika, yemweyo adzasungidwa ndi kudalitsidwa ndi zipatso zochuluka.

35 Ndiponso, ndikunena kwa inu, lolani atumiki anga Joseph Wakefield ndi Solomon Humphrey ayambe ulendo wawo ku maiko akum’mawa;

36 Aloleni iwo agwire ntchito ndi mabanja awo, osalengeza zinthu zina koma aneneri ndi atumwi, zomwe adaziona ndi kuzimva ndipo akukhulupilira ndithu, kuti mauneneri akathe kukwanilitsidwa.

37 Potsatira kulakwitsa, lolani icho chimene chidaperekedwa pa Heman Basset chilandidwe kwa iye, ndi kuikidwa pa mutu wa Simon Ryder.

38 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, lolani Jared Carter adzodzedwe wansembe, ndiponso George James adzodzedwe wansembe.

39 Lolani otsala mwa akuluwo ayang’anire pa mipingo, ndi kulengeza mawu mu madera owazungulira iwo; ndipo aloleni agwire ntchito ndi manja awo kuti kusakhale kuchita zopembedza mafano ndi zoipa.

40 Ndipo kumbukirani mu zinthu zonse osauka ndi osowa, odwala ndi opsyinjika, pakuti iye amene sachita zinthu zinthu, yemweyo si wophunzira wanga.

41 Ndiponso, lolani atumiki anga Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon ndi Edward Partridge atenge nawo chitsimikizo kuchokera ku mpingo. Ndipo lolaninso pakhale china chotengedwa cha mtumiki wanga Oliver Cowdery.

42 Ndipo motero, monga momwe ndanena, ngati inu mukhala wokhulupirika mudzadzisonkhanitsa nokha pamodzi kusangalala pa dziko la Missouri, limene lili dziko la cholowa chanu, limene tsopano lino ndi dziko la adani anu.

43 Koma, taonani, ine, Ambuye, ndidzafulumizitsa mzindawo mu nthawi yake, ndipo ndidzawaveka okhulupirika ndi chisangalalo ndi kukondwera.

44 Taonani, ine ndine Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, ndipo ndidzawakweza iwo pa tsiku lomaliza. Ngakhale choncho. Ameni.