Gawo 68
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, Novembala 1, 1831, poyankha pemphero kuti malingaliro a Ambuye adziwike zokhudzana ndi Orson Hyde, Luke S. Johnson, Lyman E. Johnson, ndi William E. McLellin. Ngakhale kuti gawo lina la vumbulutsoli lidalunjika kwa amuna anayiwa, zambiri za nkhanizi zikukhudza mpingo wonse. Vumbulutso ili lidakulitsidwa pansi pa chitsogozo cha Joseph Smith pamene lidasindikizidwa mu kope la 1835 la Chiphunzitso ndi Mapangano.
1–5Mawu a akulu akasunthidwa ndi Mzimu Woyera ndi malembo; 6–12, Akulu akuyenera kulalikira ndi kubatiza, ndipo zizindikiro zidzatsatira okhulupilira oona; 13–24, Woyamba kubadwa pakati pa ana aamuna a Aroni akhonza kutumikira ngati Bishopu Wotsogolera (ndiko kuti, kunyamula mafungulo a utsogoleri ngati bishopu) pansi pa chitsogozo cha Utsogoleri Woyamba; 25–28, Makolo akulamulidwa kuphunzitsa uthenga wabwino kwa ana awo; 29–35, Oyera mtima akuyenera kusunga Sabata, kugwira ntchito mwakhama, ndi kupemphera.
1 Mtumiki wanga, Orson Hyde, adaitanidwa ndi kudzodzedwa kwake kuti alengeze uthenga wabwino wosatha, mwa Mzimu wa Mulungu wamoyo, kuchokera kwa anthu kupita kwa anthu, ndi kuchokera ku dziko kupita ku dziko, m’misonkhano ya oipa, m’masunagoge mwawo, kukambirana ndi kufotokoza malemba onse kwa iwo.
2 Ndipo, taonani, ndipo onani, ichi ndi chitsanzo kwa onse amene adadzodzedwa ku unsembe uwu, amene ntchito yawo yaikidwa kwa iwo kupita patsogolo—
3 Ndipo ichi ndi chitsanzo kwa iwo, kuti iwo adzayankhula pamene iwo asunthidwa ndi Mzimu Woyera.
4 Ndipo chilichonse chimene iwo adzayankhula pamene asunthidwa ndi Mzimu Woyera chidzakhala malemba,woyera chidzakhala chifuniro cha Ambuye, chidzakhala maganizo a Ambuye, chidzakhala mawu a Ambuye, adzakhala mawu a Ambuye, ndi mphamvu ya Mulungu ya ku chipulumutso.
5 Taonani, ili ndi lonjezo la Ambuye kwa inu, O inu atumiki anga.
6 Kotero, sangalalani, ndipo musachite mantha, pakuti ine Ambuye ndili nanu, ndipo ndidzaima nanu; ndipo mudzachitira umboni za ine, ngakhale Yesu Khristu, kuti ndine Mwana wa Mulungu wamoyo, kuti ndidali, kuti ine ndili, ndi kuti ine ndili wakudzayo.
7 Awa ndi mawu a Ambuye kwa iwe, mtumiki wanga Orson Hyde, komanso kwa mtumiki wanga Luke Johnson, ndi kwa mtumiki wanga Lyman Johnson, ndi kwa mtumiki wanga William E. McLellin, ndi kwa akulu onse okhulupirika a mpingo wanga—
8 Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni uthenga wabwino kwa zolengedwa zonse, ndikuchita mu ulamuliro umene ndakupatsani, ndikukabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.
9 Ndipo iye amene akakhulupilire ndi kukabatizidwa adzapulumuka, ndipo iye amene sadzakhulupilira adzaweruzidwa.
10 Ndipo iye amene akhulupilira adzadalitsidwa ndi zizindikiro zakutsatira, ngakhale monga kwalembedwa.
11 Ndipo kwa inu kudzapatsidwa kuzindikira zizindikiro za nthawi, ndi zizindikiro za kudza kwa Mwana wa munthu;
12 Ndipo kwa onse amene Atate adzachitira umboni, kwa inu mudzapatsidwa mphamvu ya kuwasindikizira iwo ku moyo wosatha. Ameni.
13 Ndipo tsopano, zokhudzana ndi zinthu zowonjezera pa mapangano ndi malamulo, izo ndiye izi—
14 Patsala pambuyo pake, mu nthawi yoikika ya Ambuye, mabishopu ena akapatulidwe ku mpingo, kukatumikira ngakhale monga oyamba;
15 Kotero adzakhala akulu ansembe oyenera, ndipo adzakhala osankhidwa ndi a Utsogoleri Woyamba wa Unsembe wa Melkizedeki, kupatula ngati ali mbadwa zenizeni za Aroni.
16 Ndipo ngati ali mbadwa zenizeni za Aroni ali ndi kuyenera kwalamulo kwa ubishopu, ngati ali oyamba kubadwa mwa ana a Aroni;
17 Pakuti woyamba kubadwa ali ndi ufulu wa utsogoleri pa unsembe uwu, ndi mafungulo kapena ulamuliro omwewo.
18 Palibe munthu amene ali ndi ufulu mwalamulo ku udindo umenewu, kukhala ndi mafungulo a unsembe umenewu, kupatula ngati ali mbadwa yeniyeni komanso mwana woyamba kubadwa wa Aroni.
19 Koma, monga wamkulu wansembe wa Unsembe wa Melkizedeki ali ndi ulamulilo ogwira ntchito mu maudindo onse aang’ono akhonza kugwira ntchito mu udindo wa bishopu pamene palibe mbadwa yeniyeni ya Aroni ingapezeke, malinga ngati iye waitanidwa ndi kupatulidwa ndi kudzozedwa ku mphamvu imeneyi, pansi pa manja a Utsogoleri Woyamba wa Unsembe wa Melkizedeki.
20 Ndipo mbadwa yeniyeni ya Aroni, nayonso, ikuyenera kusankhidwa ndi Utsogoleri uwu, ndi kupezedwa oyenera, ndi kudzozedwa, komanso kudzozedwa pansi pa manja a Utsogoleri uwu, kupanda apo saloledwa mwalamulo kugwira ntchito mu unsembe wawo.
21 Koma, mwa mphamvu ya lamulo lokhudzana ndi ufulu wawo wa unsembe kutsika kuchokera kwa atate kupita kwa mwana wamwamuna, iwo atha kutenga kudzodzedwa kwawo ngati pa nthawi iliyonse angathe kutsimikizira m’ndandanda wa m’badwo wawo, kapena kuutsimikizira mwa vumbulutso lochokera kwa Ambuye pansi pa manja a Utsogoleri watchulidwa pamwambapa.
22 Ndiponso, palibe bishopu kapena wamkulu wansembe amene adzapatulidwa ku utumiki uwu amene adzazengedwa mlandu kapena kuweruzidwa pa mlandu uliwonse, kupatulapo pamaso pa Utsogoleri Woyamba wa mpingo;
23 Ndipo pamene iye wapezedwa wolakwa pamaso pa Utsogoleri uwu, mwa umboni umene sungathe kutsutsidwa, iye adzaweruzidwa;
24 Ndipo ngati iye alapa iye adzakhululukidwa, molingana ndi mapangano ndi malamulo a mpingo.
25 Ndiponso, pamene makolo ali ndi ana mu Ziyoni, kapena m’masiteki ake aliwonse amene akonzedwa, amene amawaphunzitsa iwo kuti asamvetse chiphunzitso cha kulapa, chikhulupiliro mwa Khristu Mwana wa Mulungu wamoyo, ndi ubatizo ndi mphatso ya Mzimu Woyera mwa kusanjika kwa manja, pamene zaka zisanu ndi zitatu zakubadwa, tchimolo lidzakhala pa mitu ya makolo.
26 Pakuti ili lidzakhala lamulo kwa okhalamo a Ziyoni, kapena m’masiteki ake aliwonse amene akonzedwa.
27 Ndipo ana awo adzabatizidwa ku chikhululukiro cha machimo awo akafika zaka zisanu ndi zitatu, ndi kulandira kusanjika kwa manja.
28 Ndipo adzaphunzitsanso ana awo kupemphera, ndi kuyenda mowongoka pamaso pa Ambuye.
29 Ndipo okhala mu Ziyoni adzasunga tsiku la Sabata kulipatula.
30 Ndi okhalamo a Ziyoni nawonso adzakumbukira ntchito zawo, pamene iwo asankhidwa kuti agwire ntchito, mu kukhulupirika konse; pakuti waulesi adzakumbukiridwa pamaso pa Ambuye.
31 Tsopano, ine, Ambuye, sindili wokondwa ndi anthu okhala mu Ziyoni, pakuti pali aulesi pakati pawo; ndipo ana awonso akukula mu zoipa; iwo safunanso ndi mtima wonse chuma chamuyaya, koma maso awo ali odzala ndi umbombo.
32 Zinthu izi sizikuyenera kukhala, ndipo zikuyenera kuchotsedwa pakati pawo; kotero, lolani mtumiki wanga Oliver Cowdery atengere mawu awa ku dziko la Ziyoni.
33 Ndipo lamulo ndikupereka kwa iwo—kuti iye amene sasunga mapemphero ake pamaso pa Ambuye m’nyengo yake, lolani iye akumbukiridwe pamaso pa woweruza wa anthu anga.
34 Mawu awa ali oona ndi okhulupirika; kotero, musawalakwire, kapena kuchotserako.
35 Taonani, Ine ndine Alefa ndi Omega, ndipo ndidza msanga. Ameni.