Gawo 26
Vumbulutso loperekedwa kwa Mneneri Joseph Smith,Oliver Cowdery, ndi John Whitmer, ku Harmony, Pennsylvania, July 1830 (onani mutu wa gawo 24.)
1, Alangizidwa kuti akaphunzire malemba ndi kukalalikira; 2, Lamulo la kuvomeleza kwa onse litsimikiziridwa.
1 Taonani, ine ndinena kwa inu kuti inu mudzalola nthawi yanu kukhala yoperekedwa ku maphunziro a malemba, ndi kulalikira, ndi kutsimikizira mpingo wa ku Colesville, ndi kuchita ntchito zanu pa dziko, monga zikufunikira, mpaka mutatha kudzapita kumadzulo kukachita msonkhano wotsatira; ndipo pamenepo chidzadziwika chimene mudzachite.
2 Ndipo zinthu zonse zidzachitidwa ndi chilolezo cha onse mu mpingo, mwa pemphero lalikuru ndi chikhulupiliro, pakuti zinthu zonse inu mudzalandira mwa chikhulupiliro. Ameni.