Gawo 38
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Mneneri Joseph Smith, ku Fayette, New York, Epulo 2, 1831. Mwambowu udali msonkhano wa Mpingo.
1–6, Khristu adalenga zinthu zonse; 7–8, Iye ali pakati pa Oyera Mtima Ake, amene posakhalitsa adzamuona Iye; 9–12, Chithupi chonse n’chovunda pamaso Pake; 13–22, Iye wasungira malo a lonjezo kwa Oyera Mtima Ake mu nthawi ndi muyaya; 23–27,Oyera Mtima akulamulidwa kukhala amodzi ndi kuonana wina ndi mzake ngati pachibale; 28–29, Nkhondo ziloseledwa; 30–33, Oyera Mtima akuyenera kupatsidwa mphamvu kuchokera kumwamba ndi kupita pakati pa maiko onse; 34–42, Mpingo walamulidwa kusamalira osauka ndi osowa ndi kufunafuna chuma cha muyaya.
1 Atero Ambuye Mulungu wanu, ngakhale Yesu Khristu, Wamkulukulu Ine Ndine, Alefa ndi Omega, oyamba ndi otsiriza, yemweyo amene adayang’ana pa mlengalenga waukulu wa muyaya, ndi makamu a serafi akumwamba, dziko lisadapangidwe;
2 Yemweyo amene amadziwa zinthu zonse, pakuti zinthu zonse zili pamaso panga;
3 Ndine yemweyo amene ndidayankhula, ndipo dziko lidapangidwa, ndipo zinthu zonse zidabwera ndi ine.
4 Ndine yemweyo amene ndatenga Ziyoni wa Enoki muchifuwa changa chomwe; ndipo indetu, ndikunena, ngakhale monga ambiri akhulupilira mu dzina langa, pakuti ndine Khristu, ndipo mu dzina langa lomwe, ndi mphamvu ya mwazi umene ndidakhetsa, ndawachondelera iwo pamaso pa Atate
5 Koma taonani, otsalira a oipawo ndawasunga m’maunyolo a mdima kufikira chiweruzo cha tsiku lalikululo, limene lidzabwera pa chimaliziro cha dziko lapansi;
6 Ndipo ngakhale choncho ndidzachititsa oipawo kuti asungidwe, amene sadzamva mawu anga koma kuumitsa mitima yawo, ndipo tsoka, tsoka, tsoka, ndiye mathero awo.
7 Koma taonani, indetu, indetu, ine ndinena kwa inu kuti maso anga ali pa inu, Ndili pakati panu ndipo inu simungandione ine;
8 Koma tsiku likudza msanga limene inu mudzandiona, ndi kudziwa kuti ndine; pakuti chinsalu cha mdima posachedwa chidzang’ambika, ndipo iye amene sali oyeretsedwa sadzakhala m’tsikulo.
9 Kotero, mangani lamba m’chuuno mwanu ndipo khalani okonzeka. Taonani, ufumu uli wanu, ndipo mdaniyo sadzapambana.
10 Indetu ndikunena kwa inu, ndinu oyera, koma osati nonse; ndipo palibe wina aliyense amene ndili okondwera naye;
11 Pakuti chithupi chonse n’chovunda pamaso panga; ndipo mphamvu za mdima zapambana pa dziko lapansi, pakati pa ana a anthu, pamaso pa makamu onse akumwamba—
12 Zimene zimapangitsa chete kulamulira, ndipo muyaya wonse ndiowawidwa, ndipo angelo akudikira lamulo lalikulu kuti akolole dziko lapansi, kusonkhanitsa nansongole kuti akawotchedwe; ndipo, taonani, mdaniyo waphatikizidwa.
13 Ndipo tsopano ndikuonetsani inu chinsinsi, chinthu chimene chakhala mzipinda zobisika, kuti chibweretse ngakhale chiwonongeko chanu mkati mwa nthawi, ndipo inu simudachidziwe;
14 Koma tsopano ndikuuza ichi kwa inu, ndipo ndinu odala, osati chifukwa cha mphulupulu zanu, kapena mitima yanu yosakhulupilira; pakuti indetu ena mwa inu ndinu olakwa pamaso panga, koma ndidzachitira chifundo ku kufooka kwanu.
15 Kotero, khalani amphamvu kuyambira tsopano; musaope, pakuti ufumu ndi wanu.
16 Ndipo pa chipulumutso chanu ndikupereka kwa inu lamulo, pakuti ndamva mapemphero anu, ndipo osauka adandaula kwa ine, ndipo olemera ndawapanga, ndipo anthu onse ndi anga, ndipo ine sindine watsankhol.
17 Ndipo ndalipanga dziko lapansi lolemera, ndipo taonani ndipoikapo mapazi anga, kotero, ndidzaimanso pamenepo.
18 Ndipo ndimazigwira ndi kudziletsa kupereka kwa inu chuma chochuluka, ngakhale dziko la lonjezo, dziko lodzadza mkaka ndi uchi, limene sikudzakhala thembelero pamene Ambuye adzabwera;
19 Ndipo ndidzalipereka kwa inu kukhala dziko la cholowa chanu, ngati inu mulifunafuna ndi mitima yanu yonse.
20 Ndipo ili lidzakhala pangano langa kwa inu, mudzakhala nalo ngati dziko la cholowa chanu, ndi cholowa cha ana anu kunthawi zosatha, pamene dziko lapansi lidzaima, ndipo inu mudzakhala nalonso ku muyaya, silidzathanso.
21 Koma, indetu ndikunena kwa inu kuti munthawiyo simudzakhala ndi mfumu kapena wolamulira, pakuti ndidzakhala mfumu yanu ndi kukuyang’anirani inu.
22 Kotero, mverani mawu anga ndi kunditsata ine, ndipo mudzakhala anthu aufulu, ndipo simudzakhala ndi malamulo koma malamulo anga pamene ndidzabwera, pakuti ndine wokupatsani lamulo, ndipo ndi chani chingaletse dzanja langa?
23 Koma, indetu ndinena kwa inu, phunzitsanani wina ndi mzake molingana ndi udindo umene ndakusankhilani inu;
24 Ndipo lolani munthu aliyense amuone m’bale wake ngati iyemwini, ndi kuchita ukoma ndi chiyero pamaso panga.
25 Ndiponso ndikunena kwa inu, lolani munthu aliyense amuone m’bale wake ngati iyemweni.
26 Pakuti ndani munthu mwa inu atakhala ndi ana aamuna khumi ndi awiri, ndipo alibe nawo tsankho, ndipo iwo amamutumikira iye momvera, ndi kunena ndi mmodziyo: vala iwe mwinjiro, ndipo khala pano; ndi kwa wina: Vala iwe nsanza ndipo khala apo—ndi kumayang’ana kwa ana akewo ndipo nkumati ndine wachilungamo?
27 Taonani, ichi ndikupereka kwa inu ngati fanizo, ndipo zili ngakhale ngati ine. Ndikunena kwa inu, khalani amodzi; ndipo ngati simuli amodzi simuli anga.
28 Ndiponso, ine ndinena kwa inu kuti mdani ali mu zipinda zobisika kufunafuna moyo wanu.
29 Mumamva za nkhondo mu maiko akutali, ndipo inu mumati posakhalitsa kudzakhala nkhondo zazikulu ku maiko akutali, koma simukudziwa mitima ya anthu mudziko lanu lomwe.
30 Ndikukuuzani zinthu izi chifukwa cha mapepmhero anu; kotero, sungani nzeru mkati mwanu, kuopa kuipa kwa anthu kungaulule zinthu zimenezi kwa inu mwa kuipa kwawo, mu njira imene idzayankhula m’makutu anu ndi mawu ofuula kwambiri kuposa iwo amene adzagwedeze dziko lapansi; koma ngati inu muli okonzeka simudzaopa.
31 Ndipo kuti inu mukathawe mphamvu ya mdaniyo, ndi kusonkhanitsidwa kwa ine anthu olungama, opanda banga ndipo osalakwa—
32 Kotero, pachifukwa ichi ndikupereka kwa inu lamulo kuti mupite ku Ohio; ndipo kumeneko ndidzapereka kwa inu lamulo langa; ndipo kumeneko mudzapatsidwa mphamvu kuchokera kumwamba;
33 Ndipo kuchokera kumeneko, aliyense amene ndidzafuna adzapita pakati pa maiko onse, ndipo chidzauzidwa kwa iwo chimene iwo adzachite; pakuti ndili ndi ntchito yaikulu yosungidwa, pakuti Israeli adzapulumutsidwa, ndipo ndidzawatsogolera iwo kwinakulikonse ndingafune, ndipo palibe mphamvu ingadzaletse dzanja langa.
34 Ndipo tsopano, ndikupereka kwa mpingo mu zigawo izi lamulo, kuti amuna ena pakati pawo adzasankhidwa, ndipo adzasankhidwa ndi mawu a mpingo;
35 Ndipo iwo adzayang’anira osauka ndi osowa, ndi kutumikira ku thandizo lawo kuti iwo asavutike; ndi kuwatumiza iwo ku malo amene ine ndawalamula iwo;
36 Ndipo iyi idzakhala ntchito yawo, kulamulira zochitika za chuma cha mpingowu.
37 Ndipo iwo amene ali ndi minda imene siingagulitsidwe, aisiye kapena kubwereketsa monga momwe akufunira.
38 Onani kuti zinthu zonsezi zasungidwa; ndipo pamene amuna apatsidwa mphamvu kuchokera kumwamba ndi kutumizidwa, zinthu zonsezi zidzasonkhanitsidwa mchifuwa cha mpingo.
39 Ndipo ngati mufuna chuma chimene chili chifuniro cha Atate kuchipereka kwa inu, mudzakhala olemeletsetsa a anthu onse, pakuti mudzakhala ndi chuma chamuyaya; ndipo n’kofunikira kuti chuma cha dziko lapansi ndi chaine kuchipereka; koma chenjerani ndi kunyada, kuopa mungakhale ngati Anefi akale.
40 Ndiponso, ndikunena kwa inu, ndikupereka kwa inu lamulo, kuti munthu aliyense, onse mkulu, wansembe, mphunzitsi, ndiponso membala, apite ndi mphamvu zake kukagwira ntchito ndi manja ake, kukonzekera ndi kukwanilitsa zinthu zimene ine ndalamula.
41 Ndipo lolani kulalika kwanu kukhale liwu la chenjezo, munthu aliyense kwa mnasi wake, modekha ndi mofatsa.
42 Ndipo chokani pakati pa oipawo. Dzipulumutseni nokha. Khalani oyera inu amene mwanyamula zotengera za Ambuye. Ngakhale zili choncho. Ameni.