Gawo 57
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Ziyoni, dera la Jackson, Missouri, Juni 20, 1831. Mogwirizana ndi Lamulo la Ambuye kuti apite ku Missouri, kumene Iye akavumbulutse “dziko la cholowa chanu” (gawo 52), akulu adayenda kuchokera ku Ohio kupita ku malire a kumadzulo kwa Missouri. Joseph Smith adalingalira makhalidwe a Alamani ndipo anadabwa: “Kodi ndi liti limene chipululu chidzaphukira ngati duwa? Ndi liti limene Ziyoni adzamangidwe mu ulemelero wake, ndipo ndikuti kumene kachisi Wanu adzaima, ndi kuti kumene maiko onse adzabwera mu masiku otsiriza?” Zotsatira zake iye adalandira vumbulutso ili.
1–3, Independence, Missouri, ndi malo a mzinda wa Ziyoni ndi kachisi; 4–7, Oyera Mtima akuyenera kugula malo ndi kulandira zolowa zawo mu dera limenero; 8–16, Sidney Gilbert akuyenera kukhazikitsa sitolo, William W. Phelps akuyenera kukhala wosindikiza, ndipo Oliver Cowdery akuyenera kukonzanso zolemba kuti zitsindikizidwe.
1 Mvetserani, O inu akulu a mpingo wanga, atero Ambuye Mulungu wanu, amene mwadzisonkhanitsa nokha pamodzi, molingana ndi malamulo anga, mu dziko lino, limene ndi dziko la Missouri, limene lili dziko limene ndalisankha ndi kulipatula pa kusonkhana kwa oyera mtima.
2 Kotero, ili ndi dziko la lonjezo, ndi malo a mzinda wa Ziyoni.
3 Ndipo akutero Ambuye Mulungu wanu, ngati mungalandire nzeru nayi nzeru. Taonani, malo amene tsopano akutchedwa Independence ndi malo apakatikati; ndipo ndi malo a kachisi akhala chakumadzulo, pa malo amene sali patali ndi nyumba yamalamulo,
4 Kotero, ndi nzeru kuti malowa agulidwe ndi oyera mtima, ndiponso kagawo kalikonse kali chakumadzulo, ngakhale mzere wothamangira molunjika pakati pa Myuda ndi Mmitundu;
5 Ndiponso kagawo kalikonse ka kumalire a kumapiri, pamene aphunzira anga ali ndikuthekera kogula malo. Taonani, iyi ndi nzeru, kuti iwo akathe kulipeza ilo ku cholowa chosatha.
6 Ndipo mloleni mtumiki wanga Sidney Gilbert aime mu udindo umene ine ndamusankhira iye, kuti adzilandira ndalama, kuti akhale othandizira kwa mpingo, kugula malo mu madera onse ozungulira, pamene zingachitike mu chilungamo, ndi m’mene nzeru ingatsogolere.
7 Ndipo mloleni mtumiki wanga Edward Partridge aime mu udindo umene ine ndamusankhira iye, ndi kugawira kwa oyera mtima cholowa chawo, ngakhale monga ine ndalamulira; ndiponso iwo amene iye wasankha kuti amuthandizire iye.
8 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, mloleni mtumiki wanga Sidney Gilbert adzimangire yekha mu malo ano, ndi kukhazikitsa sitolo, kuti iye akathe kugulitsa zinthu popanda chinyengo, kuti iye akathe kupeza zinthu zilizonse zimene ophunzira angafune kuti amangire cholowa chawo.
9 Ndiponso mloleni mtumiki wanga Sidney Gilbert atenge chilolezo—taonani iyi ndi nzeru, ndiponso aliyense amene amawerenga mlekeni amvetse—kuti iye akathenso kutumiza zinthu kwa anthu, ngakhale kudzera mwa yemwe iye angafune ngati kalaliki olembedwa mu ntchito yake;
10 Ndipo potero kusamalira oyera mtima anga, kuti uthenga wanga wabwino ukathe kulalikidwa kwa iwo amene akhala mumdima ndi mu dera ndi mthunzi wa imfa.
11 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, mloleni mtumiki wanga William W. Phelps adzalidwe mu malo ano, ndipo akhazikitsidwe ngati otsindikiza kwa mpingo.
12 Ndipo onani, ngati dziko lirandira zolemba zake—taonani apa pali nzeru—mloleni iye atenge chilichonse angathe kutenga mu chilungamo, pa ubwino wa oyera mtima.
13 Ndipo mloleni mtumiki wanga Oliver Cowdery amuthandize iye, ngakhale momwe ine ndalamulira, mu malo ena aliwonse amene ine ndidzasankhira kwa iye, kuti akopele, ndi kukonza, ndi kusankha, kuti zinthu zonse zikathe kukhala zolondola pamaso panga, monga zidzatsimikiziridwa ndi Mzimu wanga kudzera mwa iye.
14 Ndipo motero aloleni iwo amene ndayankhulapo adzalidwe mu malo a Ziyoni, mwachangu momwe zingakhalire, ndi mabanja awo, kuchita zinthu izo ngakhale monga momwe ine ndayankhulira.
15 Ndipo tsopano zokhudzana ndi kusonkhana—Lolani bishopu ndi mtumiki apanga zokonzekera kwa mabanja amene alamulidwa kuti abwere ku malo ano, mwachangu momwe zingachitikire, ndi kuwakhazika iwo mu cholowa chawo.
16 Ndipo kwa otsala mwa onse akulu ndi mamembala chitsogozo china chidzaperekedwa pambuyo pake. Ngakhale choncho. Ameni.