Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 58


Gawo 58

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, mu Ziyoni, Jackson County, Missouri, Ogasiti 1, 1831. M’mbuyomo, pa Sabata loyamba pambuyo pa kufika kwa Mneneri ndi gulu lake ku dera la Jackson, Missouri, msonkhano wachipembedzo udachitidwa, ndipo mamembala awiri adalandiridwa mwa ubatizo. Mu sabata imeneyo, ena mwa Oyera mtima a Colesville ochokera ku Nthambi ya Thompson ndi ena adafika (onani gawo 54). Ambiri adali ofunitsitsa kuphunzira chifuniro cha Ambuye zokhudzana ndi iwo mu malo atsopano osonkhanira.

1–5, Iwo amene amapilira masautso adzavekedwa korona wa ulemerero; 6–12, Oyera mtima akuyenera kukonzekera ukwati wa Mwanawankhosa ndi m’gonero wa Ambuye; 13–18, Mabishopu, ndi oweruza mu Israeli; 19–23, Oyera mtima akuyenera kumvera malamulo a dziko; 24–29, Anthu akuyenera kugwiritsa ntchito ufulu wawo wosankha kuchita zabwino; 30–33, Ambuye amalamulira ndi kubweza; 34–43, Kuti alape, anthu akuyenera kuulula ndi kusiya machimo awo; 44–58, Oyera mtima akuyenera kugula cholowa chawo ndi kusonkhana mu Missouri; 59–65, Uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa cholengedwa chilichonse.

1 Mvetserani, O inu akulu a mpingo wanga, ndipo tcherani khutu ku mawu anga, ndipo phunzirani za ine chimene ndifuna zokhudzana ndi inu, ndiponso zokhudzana ndi dziko ili limene ndakutumizaniko.

2 Pakuti indetu ndinena kwa inu, wodala ndi iye amene asunga malamulo anga, kaya m’moyo kapena mu imfa; ndipo iye amene ali wokhulupirika mu masautso, mphotho yake yemweyo ndi yaikulu mu Ufumu wa Kumwamba.

3 Simungathe kuona ndi maso anu achibadwidwe, kwa nthawi ino, makonzedwe a Mulungu wanu zokhudzana ndi zinthu zimene zidzabwera pambuyo pake, ndi ulemerero umene udzatsatira pambuyo pa masautso ambiri.

4 Pakuti pambuyo pa masautso ambiri pamabwera madalitso. kotero tsiku likudza limene mudzavekedwa korona wa ulemerero wochuluka; ola silidafike, koma lili pafupi.

5 Kumbukirani ichi, chimene ndikukuuzani kale, kuti mukathe kuchiika mumtima, ndi kulandira chimene chilikutsatira.

6 Taonani, indetu ndinena kwa inu, chifukwa cha ichi ndakutumizani—kuti mukathe kukhala omvera, ndi kuti mitima yanu ikathe kukonzekera kuchitira umboni wa zinthu zimene zilinkudza;

7 Ndiponso kuti inu mukathe kulemekezedwa mu kuyala maziko, ndi mu kuchitira umboni wa dziko limene Ziyoni wa Mulungu adzaima;

8 Ndiponso kuti phwando la zinthu zonona likathe kukonzeredwa kwa osauka; inde, phwando la zinthu zonona, za vinyo wa pansenga woyengeka bwino, kuti dziko lapansi likathe kuzindikira kuti pakamwa pa aneneri sipadzalephera;

9 Inde, mgonero wa nyumba ya Ambuye, wokonzedwa bwino, kumene maiko onse adzaitanidwa.

10 Koyamba, olemera ndi ophunzira, anzeru ndi olemekezeka;

11 Ndipo pambuyo pake likudza tsiku la mphamvu yanga; pamenepo aumphawi, olumala, ndi akhungu, ndi ogontha, adzalowa ku ukwati wa Mwana wankhosa, ndi kudzadya nawo mgonero wa Ambuye, wokonzedwera tsiku lalikulu lirinkudza.

12 Taonani, ine, Ambuye, ndanena ichi.

13 Ndipo kuti umboni ukathe kupita kuchokera ku Ziyoni, inde, kuchokera mkamwa mwa mzinda wa cholowa cha Mulungu—

14 Inde, chifukwa cha ichi ndakutumizani kuno, ndipo ndasankha mtumiki wanga Edward Partridge, ndipo ndamuikira ntchito yake m’dziko lino.

15 Koma ngati salapa machimo ake, amene ali kusakhulupilira ndi khungu la mtima, muloleni asamale kuopa kuti angagwe.

16 Taonani ntchito yake yaperekedwa kwa iye, ndipo iyo sidzaperekedwanso.

17 Ndipo iye amene aimilira pa ntchito imeneyi asankhidwa kukhala woweruza mu Israeli, monga m’mene zidalili masiku akale, kugawira ana ake maiko a cholowa cha Mulungu;

18 Ndi kuweruza anthu ake ndi umboni wa olungama, ndi mothandizidwa ndi alangizi ake, molingana ndi malamulo a ufumu amene adaperekedwa ndi aneneri a Mulungu.

19 Pakuti indetu ndinena kwa inu, lamulo langa lidzasungidwa pa dziko lino.

20 Munthu asaganize kuti ndi wolamulira; koma lolani Mulungu alamulire iye amene aweruza, monga mwa uphungu wa chifuniro cha iye mwini, kapena, m’mawu ena, iye amene alangiza kapena akhala pa mpando wa chiweruzo.

21 Munthu asaphwanye malamulo a dziko, pakuti iye amene amasunga malamulo a Mulungu safunikira kuphwanya malamulo a dziko.

22 Kotero, mverani maulamuliro amene alipo, kufikira adzalamulire iye amene ali ndi ufulu wa kulamulira, ndi kugonjetsa adani onse pansi pa mapazi ake.

23 Taonani, malamulo amene inu mudalandira kuchokera m’dzanja langa ndi malamulo a mpingo, ndipo mu kuunika uku mudzawasunga iwo. Taonani, apa pali nzeru.

24 Ndipo tsopano, monga ndidanena zokhudzana ndi mtumiki wanga Edward Partridge, dziko ili ndi dziko la kukhala kwake, ndi iwo amene iye wasankha kukhala alangizi ake; ndiponso dziko la mokhalamo iye amene ndamuika kuti asunge nkhokwe yanga;

25 Kotero, aloleni iwo abweretse mabanja awo ku dziko lino, monga iwo adzachitira uphungu pakati pa iwo eni ndi ine.

26 Pakuti taonani, sikoyenera kuti ndilamulire mu zinthu zonse; pakuti iye amene akakamizidwa mu zinthu zonse, yemweyo ali waulesi ndipo osati mtumiki wanzeru; kotero iye samalandira mphotho.

27 Indetu ndinena, anthu akuyenera kutanganidwa ndi cholinga chabwino, ndi kuchita zinthu zambiri mwa kufuna kwawo, ndi kubweretsa chilungamo chochuluka;

28 Pakuti mphamvu ili mwa iwo, momwe ali atumwi kwa iwo okha. Ndipo monga momwe anthu akuchitira zabwino, iwo sadzataya malipiro awo.

29 Koma iye amene sachita kanthu kufikira atalamulidwa, ndi kulandira lamulo ndi mtima wokayika, ndi kulisunga ndi ulesi, yemweyu adzaweruzidwa.

30 Ine ndine ndani amene ndidapanga munthu, atero Ambuye, amene ndidzamuyesa wosalakwa amene samvera malamulo anga?

31 Ine ndine ndani, atero Ambuye, amene ndalonjeza ndipo sindidakwaniritse?

32 Ndimalamula ndipo anthu samvera; Ndimabweza ndipo salandira madalitso.

33 Kenako amati m’mitima mwawo: “Iyi si ntchito ya Ambuye, chifukwa malonjezo ake sakwaniritsidwa. Koma tsoka kwa otere, pakuti mphotho yawo ibisalira pansi, ndipo simachokera kumwamba.

34 Ndipo tsopano ndikukupatsani malangizo ena okhudzana ndi dziko lino.

35 Ndi cha nzeru mwa ine kuti mtumiki wanga Martin Harris akhale chitsanzo kwa mpingo, pakuika ndalama zake pamaso pa bishopu wa mpingo.

36 Ndiponso, ili ndi lamulo kwa munthu aliyense amene adza ku dziko lino kudzalandira cholowa; ndipo azichita ndi ndalama zake molingana ndi monga lamulo likunenera.

37 Ndipo ndi cha nzeru komanso kuti pakuyenera kukhala malo ogulidwa ku Independence, mu nkhokwe, ndiponso nyumba yosindikizira.

38 Ndi malangizo ena okhudzana ndi mtumiki wanga Martin Harris adzapatsidwa kwa iye ndi Mzimu, kuti iye alandire cholowa chake monga chimukomera iye;

39 Ndipo muloleni alape machimo ake, pakuti akufunafuna matamando a dziko.

40 Ndiponso mulole mtumiki wanga William W. Phelps aimilire mu udindo umene ndamusankhira iye, ndi kulandira cholowa chake m’dzikoli;

41 Ndiponso akuyenera kulapa, pakuti ine, Ambuye, sindili wokondweretsedwa naye, pakuti iye amafuna kupambana; ndipo sali wofatsa mokwanira pamaso panga.

42 Taonani, iye amene walapa machimo ake, yemweyo wakhululukidwa, ndipo ine, Ambuye, sindindimaakumbukiranso iwo.

43 Mwa ichi mungadziwe ngati munthu walapa machimo ake—taonani, adzawavomereza ndi kuwasiya.

44 Ndipo tsopano, indetu, ndinena zokhudzana ndi otsala a akulu a mpingo wanga, nthawi siidafike, kwa zaka zambiri, kuti iwo alandire cholowa chawo m’dziko lino, kupatula ngati atachikhumba kudzera mu pemphero la chikhulupiliro, pokhapokha ngati chidzaikidwa kwa iwo ndi Ambuye.

45 Pakuti, taonani, adzakankhira anthu pamodzi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

46 Kotero, sonkhanani inu nokha pamodzi; ndipo iwo amene sadasankhidwe kukhala m’dziko lino, alalikire uthenga wabwino m’madera ozungulira; ndipo pambuyo pake aloleni abwelere kwawo.

47 Aloleni alalikire m’njira, ndi kuchitira umboni za choonadi m’malo onse, ndi kuitana olemera, apamwamba ndi onyozeka, ndi osauka kuti alape.

48 Ndipo aloleni amange mipingo, pamene anthu okhala padziko lapansi adzalapa.

49 Ndipo lolani pakhale mthumwi wosankhidwa ndi mawu a mpingo, kwa mpingo mu Ohio, kuti alandire ndalama zogulira malo mu Ziyoni.

50 Ndipo ine ndikupereka kwa mtumiki wanga Sidney Rigdon lamulo, kuti adzalemba kafotokozedwe ka dziko la Ziyoni, ndi chiganizo cha chifuniro cha Mulungu, monga chidzadziwikire ndi Mzimu kwa iye;

51 Ndi kalata ndi kulembetsa, kukaperekedwa kwa mipingo yonse kuti alandire ndalama, kuti zikayikidwe m’manja mwa bishopu, kwa iye mwini kapena mtumiki, monga akuwonera kuti ndi zabwino kapena momwe angatsogolere, kuti agule malo a cholowa cha ana a Mulungu.

52 Pakuti, taonani, indetu ndinena kwa inu, Ambuye akufuna kuti ophunzira ndi ana a anthu atsegule mitima yawo, ngakhale kugula chigawo chonse cha dziko lino, mwamsanga pamene nthawi ilola.

53 Taonani, apa pali nzeru. Aloleni achite izi kuopa kuti sangalandire cholowa;kupatula mwa kukhetsa mwazi.

54 Ndiponso, pamene papezeka malo, lolani pamenepo patumizidwe antchito osiyanasiyana pa malowa, kuti agwire ntchito kwa oyera mtima a Mulungu.

55 Izi zonse zichitike mwadongosolo; ndipo lolani mwayi wa malowo udziwike ku nthawi ndi nthawi, ndi bishopu kapena nthumwi ya mpingo.

56 Ndipo ntchito ya kusonkhanitsa isakhale yachangu, kapena yochita mothawa; koma iloleni ichitidwe monga idzalangizidwire ndi akulu a mpingo pa misokhano yaikulu, molingana ndi chidziwitso chomwe amalandira nthawi ndi nthawi.

57 Ndipo ulole mtumiki wanga Sidney Rigdon apereke ndi kupatulira malo awa, ndi malo a kachisi, kwa Ambuye.

58 Ndipo lolani msonkhano waukulu uitanidwe; ndipo pambuyo pake lolani atumiki anga Sidney Rigdon ndi Joseph Smith, Jun., abwelere, ndiponso Oliver Cowdery ndi iwo, kuti akwaniritse yotsala ya ntchito imene ndaika kwa iwo m’dziko lawo lomwe, ndi yotsalayo monga adzalamuliridwa ndi misonkhano yaikulu.

59 Ndipo asabwelere munthu m’dziko lino, pokhapokha aikire umboni munjira pazimene akudziwa, ndi kuzikhulupilira.

60 Chimene chidaperekedwa kwa Ziba Peterson chichotsedwe kwa iye; ndipo muloleni aime monga membala wa Mpingo; ndi kugwira ntchito ndi manja ake omwe, ndi abale, mpaka iye atalangidwa mokwanira chifukwa cha machimo ake onse; pakuti samawavomereza, ndipo akuganiza zakuwabisa.

61 Lolani otsala a akulu a mpingo uno, amene akubwera ku dziko lino, ena mwa iwo ali odalitsidwa mopambana ngakhale moposa muyeso, achitenso nawo msonkhano waukulu pa dziko lino.

62 Ndipo mulole mtumiki wanga Edward Partridge atsogolere msonkhano waukuluwo umene udzachitike ndi iwo.

63 Ndipo aloleni abwelere nawonso, kulalikira uthenga wabwino munjira, kuchitira umboni wa zinthu zimene zaululidwa kwa iwo.

64 Pakuti, indetu, phokoso likuyenera kupita kuchokera kumalo ano kupita ku dziko lonse lapansi, ndi mpaka kumalekezero a dziko lapansi—uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa cholengedwa chilichonse, ndi zizindikiro zowatsatira iwo amene akhulupilira.

65 Ndipo onani Mwana wa Munthu akudza. Ameni.