Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 23


Gawo23

Mndandanda wa mavumbulutso asanu operekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Manchester, New York, Epulo 1830, kwa Oliver Cowdery,Hyrum Smith, Samuel H. Smith, Joseph Smith Sr., ndi Joseph Knight Sr. Chifukwa cha chikhumbo chenicheni cha anthu asanu otchulidwawo kuti adziwe za ntchito zawo, Mneneri adafunsa kwa Ambuye ndipo adalandira vumbulutso la munthu aliyense.

1–7, Ophunzira oyambilirawa akuitanidwa kukalalikira, kukalimbikitsa, ndi kukalimbitsa Mpingo.

1 Taona, ndikuyankhula kwa iwe, Oliver, mawu ochepa. Taona, iwe ndi wodalitsidwa, ndipo suli pansi pa kutsutsidwa. Koma chenjera ndi kudzikuza, kuti ungalowe m’kuyesedwa.

2 Dziwitsa maitanidwe ako kwa mpingo, ndiponso pamaso pa dziko lapansi, ndipo mtima wako udzatsegulidwa kuti ulalikire choonadi kuyambira pano mpaka muyaya. Ameni.

3 Taona, ndikuyankhula kwa iwe, Hyrum, mawu ochepa; pakuti iwenso suli wotsutsidwa, ndipo mtima wako watseguka, ndi lilime lako lamasulidwa; ndipo maitanidwe ako ndi ku chilimbikitso, ndi kulimbikitsa mpingo mosalekeza. Kotero ntchito yako ili kwa mpingo kwanthawi zonse, ndipo izi chifukwa cha banja lako. Ameni.

4 Taona, ndikuyankhula mawu ochepa kwa iwe, Samueli; pakuti iwenso suli pansi pa kutsutsidwa, ndipo maitanidwe ako ndi a chilimbikitso, ndi kulimbikitsa mpingo; ndipo sudaitanidwe kaye kukalalikira pamaso pa dziko. Ameni.

5 Taona, ndikuyankhula mawu ochepa kwa iwe, Joseph; pakuti iwenso suli pansi pa kutsutsidwa, ndipo maitanidwe ako alinso a chilimbikitso, ndi kulimbikitsa mpingo; ndipo iyi ndi ntchito yako kuyambira pano mpaka muyaya. Ameni.

6 Taona, ine ndikuonetsera kwa iwe, Joseph Knight, mwa mawu awa, kuti ukuyenera kunyamula mtanda wako, momwe iwe uyenelera kupemphera mofuula pamaso pa dziko lapansi komanso mwachinsinsi, ndi mu banja lako, ndi pakati pa abwenzi ako, ndi mu malo onse.

7 Ndipo, taona, ndi udindo wako kuti ugwirizane ndi mpingo woona, ndi kupereka chiyankhulidwe chako ku chilimbikiso mosalekeza, kuti ukathe kulandira mphotho ya wantchito. Ameni.