Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 62


Gawo 62

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, m’mphepete mwa Mtsinje wa Missouri ku Chariton, Missouri, Ogasiti 13, 1831. Pa tsiku limeneli Mneneri ndi gulu lake, amene adali mu njira yawo kuchokera ku Independence kupita ku Kirtland, adakumana ndi akulu ambiri amene adali pa ulendo wawo kupita ku malo a Ziyoni, ndipo, atatha kupatsana malonje achisangalalo, adalandira vumbulutso ili.

1–3, Maumboni amalembedwa kumwamba; 4–9, Akulu akuyenera kupita ndi kukalalikira molingana ndi chiweruzo ndi momwe atsogozedwera ndi Mzimu.

1 Taonani, ndi kumvetsera, O inu akulu ampingo wanga, atero Ambuye Mulungu wanu, ngakhale Yesu Khristu, nkhoswe yanu, amene amadziwa zofooka za munthu ndi m’mene angathandizire iwo amene ayesedwa,

2 Ndipo indetu maso anga ali pa iwo amene sadapitebe ku dziko la Ziyoni; potero utumiki wanu siudakwanirebe.

3 Komabe, ndinu odala, chifukwa umboni womwe inu mwapereka walembedwa kumwamba kuti angelo adziuyang’ana; ndipo iwo amakondwera mwa inu, ndipo machimo anu akhululukidwa.

4 Ndipo tsopano pitilizani ulendo wanu. Dzisonkhanitseni nokha pa dziko la Ziyoni; ndipo mukhale ndi msonkhano ndi kukondwera limodzi, ndi kupereka sakramenti kwa Wam’mwambamwamba.

5 Ndipo kenako mukhonza kubwelera kukachitira umboni, inde, ngakhale pamodzi, kapena awiri-awiri, momwe mwaonera bwino, zilibe kanthu kwa ine; mungokhala okhulupirika basi, ndi kulengeza uthenga wabwino kwa okhala pa dziko lapansi, kapena pakati pa misonkhano ya oipa.

6 Taonani, ine, Ambuye, ndakubweretsani inu pamodzi kuti lonjezo likathe kukwaniritsidwa, kuti okhulupirika pakati panu asungidwe ndi kukondwera limodzi mu dziko la Missouri. Ine, Ambuye, ndalonjeza okhulupirika ndipo sindinganame.

7 Ine, Ambuye, ndili ofuna, ngati wina pakati panu akhumba kukwera pa akavalo, kapena abulu, kapena mu magaleta, iye adzalandira dalitso limeneli, ngati iye alilandira kuchokera mu dzanja la Ambuye, ndi mtima wothokoza mu zinthu zonse.

8 Zinthu izi zikhale ndi inu kuchita molingana ndi chiweruzo ndi chitsogozo cha Mzimu.

9 Taonani, ufumu ndi wanu. Ndipo taonani, ndipo onani, Ine ndili ndi wokhulupirika nthawi zonse. Ngakhale choncho. Ameni.