Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 4


Gawo 4

Vumbulutso loperekedwa kudzera kwa Mneneri Joseph Smith kwa abambo ake, Joseph Smith Sr., ku Harmony, Pennsylvania, Febuluwale 1829.

1–4, Kutumikira molimbika kumapulumutsa atumiki a Ambuye;5–6, Makhalidwe aumulungu amawayeneretsa iwo ku utumiki;7, Zinthu za Mulungu zikuyenera kufunidwa.

1 Tsopano taonani, ntchito yodabwitsa ili pafupi kutulukira pakati pa ana a anthu.

2 Kotero, O inu amene mwayamba mu utumiki wa Mulungu, onani kuti mukutumikira ndi mtima wanu wonse, mphamvu, nzeru ndi nyonga, kuti mukathe kuimilira opanda banga pamaso pa Mulungu pa tsiku lomaliza.

3 Kotero, ngati muli ndi zikhumbo za kutumikira Mulungu inu mwaitanidwa ku ntchitoyo;

4 Pakuti taonani, m’mundamo mwayera kale kuti mukololedwe; ndipo taonani, iye amene aponya chikwakwa chake ndi mphamvu zake, yemweyo akusunga munkhokwe kuti asawonongeke, koma amabweretsa chipulumutso ku moyo wake;

5 Ndipo chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi chikondi, ndi diso limodzi ku ulemelero wa Mulungu, zimamuyenereza iye kugwira ntchitoyo.

6 Kumbukirani chikhulupiliro, ukoma, chidziwitso, kudziletsa, chipiliro, kuleza mtima pa abale, umulungu, chikondi, kudzichepetsa, khama.

7 Pemphani, ndipo mudzalandira; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu. Ameni.