Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 25


Gawo 25

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Harmony, Pennsylvania, July 1830 (onani mutu wa gawo 24). Vumbulutso limeneri likuonetsa chifuniro cha Ambuye kwa Emma Smith, mkazi wa Mneneri.

1–6, Emma Smith, mkazi wosankhidwa, ayitanidwa kuti athandize ndi kutonthoza mwamuna wake; 7–11, Iye adaitanidwanso kuti adzilemba, kufotokozera malemba, ndi kusankha nyimbo; 12–14, Nyimbo ya olungama ndi pemphero kwa Ambuye; 15–16, Mfundo za kumvera mu vumbulutso ili zimagwira ntchito kwa onse.

1 Mvetsera ku mawu a Ambuye Mulungu wako, pamene ine ndikuyankhula kwa iwe, Emma Smith, mwana wanga wamkazi; pakuti indetu ndinena kwa iwe, onse amene alandira uthenga wanga ali ana amuna ndi akazi mu ufumu wanga.

2 Vumbulutso ndikupereka kwa iwe lokhudzana ndi chifuniro changa; ndipo ngati uli wokhulupirika ndi kuyenda m’njira za ukoma pamaso panga; ndidzasunga moyo wako, ndipo udzalandira cholowa mu Ziyoni.

3 Taona, machimo ako akhululukidwa iwe, ndipo iwe ndiwe mkazi wosankhika, amene ndakuitana.

4 Usadandaule chifukwa cha zinthu zimene sudazione, pakuti zabisidwa kwa iwe ndi kwa dziko lapansi, zimene zili nzeru mwa ine mu nthawi ikudzayi.

5 Ndipo udindo wa mayitanidwe ako udzakhala wa chitonthozo kwa mtumiki wanga, Joseph Smith, Jun., mwamuna wako, m’masautso ake, ndi mawu otonthoza, mu mzimu wa chifatso.

6 ndipo udzapita naye pa nthawi ya kuyenda kwake, ndi kukhala kwa iye ngati mlembi, pamene palibe wina amene adzakhale mlembi wa iye, kuti ndidzathe kutumiza mtumiki wanga, Oliver Cowdery, kulikonse kumene ndikufuna.

7 Ndipo udzadzodzedwa pansi pa dzanja lake kuti ukafotokozere malembo, ndi kulimbikitsa mpingo, monga momwe kudzapatsidwira kwa iwe mwa Mzimu wanga.

8 Pakuti iye adzasanjika manja ake pa iwe, ndipo iwe udzalandira Mzimu Woyera, ndipo nthawi yako idzaperekedwa ku kulemba, ndi kuphunzira zambiri.

9 Ndipo sukuyenera kuopa, pakuti mwamuna wako adzakuthandiza iwe mu mpingo; pakuti kwa iwo kuli kuitana kwake, kuti zinthu zonse zikaululidwe kwa iwo, zomwe ndikufuna, molingana ndi chikhulupiliro chawo.

10 Ndipo indetu ine ndinena kwa iwe kuti udzaika pambali zinthu za dziko lapansi, ndi kufunafuna zinthu zabwino.

11 Ndipo kudzapatsidwa kwa iwe, komanso, kuti ukapange chisankhulo cha nyimbo zopatulika, monga kudzapatsidwa kwa iwe, zimene zimandikondweretsa ine, kuti zikhale mu mpingo wanga.

12 Pakuti moyo wanga umakondwera ndi kuyimba kwa mtima; inde, nyimbo ya olungama ndi pemphero kwa ine;ndipo lidzayankhidwa ndi mdalitso pa mitu yawo.

13 Kotero, kweza mtima wako ndi kusangalala, ndipo kangamila ku mapangano amene iwe wapanga.

14 Pitiriza mu mzimu wofatsa, ndipo chenjera ndi kudzikuza. Lola moyo wako ukondwere mwa mwamuna wako, ndi ulemerero umene udzafika pa iye.

15 Sunga malamulo anga mosalekeza, ndipo korona wa chilungamo iwe udzalandira. Ndipo ukapanda kuchita ichi, kumene ine ndili, sungathe kubwerako.

16 Ndipo indetu, indetu, ine ndinena kwa iwe, kuti awa ndi mawu anga kwa onse. Ameni.