Gawo 69
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, Novembela 11, 1831 Kusonkhanitsa kwa mavumbulutso amene cholinga chake chidali kuti afalitsidwe koyambilira kudaperekedwa pamsonkhano wapadera wa Novembala 1–2. Pa Novembala 3, vumbulutso lomwe likuoneka pano ngati gawo 133, lomwe pambuyo pake lidatchedwa Zowonjezera, lidawonjezedwa Oliver Cowdery adali atasankhidwa kale kunyamula zolembedwa za mavumbulutso ndi malamulo ophatikizidwa ku Independence, Missouri, kuti asindikizidwe. Adayeneranso kutenga ndalama zimene zidaperekedwa kuti amange Mpingo ku Missouri. Vumbulutso ili likulangiza John Whitmer kuti atsagane ndi Oliver Cowdery ndipo likutsogoleranso Whitmer kuti ayende ndi kusonkhanitsa zinthu za mbiriyakale mu maitanidwe ake monga wolemba mbiri yakale ndi wolemba mbiri ya Mpingo.
1–2, John Whitmer akuyenera kuperekeza Oliver Cowdery ku Missouri; 3–8, Akuyeneranso kulalikira ndi kusonkhanitsa, kulemba, ndi kulemba zinthu za mbiriyakale.
1 Mvetserani kwa ine, atero Ambuye Mulungu wanu, chifukwa cha mtumiki wanga Oliver Cowdery. Si nzeru mwa ine kuti waikizidwa ndi malamulo ndi ndalama zimene iye adzanyamula kupita ku dziko la Ziyoni, kupatula mmodzi kupita ndi iye amene adzakhala woona ndi wokhulupirika.
2 Kotero, ine, Ambuye, ndikufuna kuti mtumiki wanga, John Whitmer, apite ndi mtumiki wanga Oliver Cowdery;
3 Ndiponso kuti adzapitirize mu kulemba ndi kupanga mbiri ya zinthu zonse zofunika zimene adzazione ndi kuzidziwa zokhudzana ndi mpingo wanga;
4 Ndiponso kuti alandire uphungu ndi chithandizo kuchokera kwa mtumiki wanga Oliver Cowdery ndi ena.
5 Ndiponso, atumiki anga amene ali kunja kwa dziko lapansi akatumize mbiri za ukapitawo wawo ku dziko la Ziyoni;
6 Pakuti dziko la Ziyoni lidzakhala mpando ndi malo olandilira ndi kuchita zinthu zonsezi.
7 Komabe, mulekeni mtumiki wanga John Whitmer ayende nthawi zambiri kuchokera kumalo kupita ku malo, ndi kuchokera ku mpingo kupita ku mpingo, kuti akathe kupeza chidziwitso mosavuta—
8 Kulalikira ndi kufotokozera, kulemba, kukopera, kusankha, ndi kupeza zinthu zonse zimene zidzakhala za ubwino wa mpingo, ndi kwa mibadwo ya achinyamata imene idzakulira pa dziko la Ziyoni, kulitenga ku mibadwomibadwo, kwamuyaya ndi nthawizonse. Ameni.