Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 95


Gawo 95

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Juni 1, 1833. Vumbulutso ili ndi kupitiliza kwa chitsogozo cha umulungu kumanga nyumba yopembedzera ndi malangizo, nyumba ya Ambuye (onani gawo 88:119–136).

1–6, Oyera mtima alangidwa chifukwa chakulephera kumanga nyumba ya Ambuye; 7–10, Ambuye akhumbira kugwiritsa nthito nyumba Yake kudalitsa anthu Ake ndi mphamvu yochokera kumwamba; 11–17, Nyumba ikuyenera kupatulidwa ngati malo opembedzera ndi ya sukulu ya Atumwi.

Indetu, akutero Ambuye kwa inu amene ndimakukondani, ndipo amene ndimawakonda ndimawalanga kuti machimo awo akathe kukhululukidwa, pakuti ndi chilango ndimakonzera njira ya chipulumutso mu zinthu zonse zotulukira kumayesero, ndipo ine ndakukondani—

Kotero, mukufunikira kulangidwa ndi kuima odzudzulidwa pamaso panga;

Pakuti inu mwandichimwira ine tchimo lalikulu, moteromo simudalingalire za lamulo lalikulu mu zinthu zonse, limene ine ndapereka kwa inu lokhudzana ndi kumanga kwa nyumba yanga;

Pa kukonzekera kumene ine ndapanga kukonzekeretsa atumwi anga kuti akadulire munda wanga wampesa kwa nthawi yomaliza, kuti ndikathe kubweretsa ntchito yanga yachilendo, kuti ndikathe kutsanulira Mzimu wanga pa mnofu wonse—

Koma taonani, indetu ndikunena kwa inu, kuti alipo ambiri amene adzodzedwa pakati panu, amene ndawaitana koma ochepa mwa iwo asankhidwa.

Iwo amene sadasankhidwe achimwa tchimo lalikulu, mwakuti iwo akuyenda mu mdima pakati pa tsiku.

Ndipo pachifukwa ichi ndapereka kwa inu lamulo kuti muitanitse msonkhano wapadera, kuti kusala kwanu ndi kulira kuthe kufika ku makutu a Ambuye Wamakamu, limene tanthauzo lake, wolenga wa tsiku loyamba, oyamba ndi otsiriza.

Inde, indetu ndinena kwa inu, ndidapereka kwa inu lamulo kuti mumange nyumba, mumene ine ndaipanga kuti ndidalitsiremo iwo amene ndawasankha ndi mphamvu yochokera kumwamba;

Pakuti ili ndi lonjezo la Atate kwa inu; kotero ndikukulamulani kuti muyembekeze, monga ngati Atumwi ku Yerusalemu.

10 Komabe, atumiki anga achimwa tchimo lalikulu; ndipo mikangano yabuka mu sukulu ya Aneneri; imene idali yokhumudwitsa kwa ine, atero Ambuye; kotero ndawatumiza kuti akalangidwe.

11 Indetu, ndikunena kwa inu, ndi chifuniro changa kuti inu mumange nyumba. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala ndi mphamvu zoimanga.

12 Ngati simusunga malamulo anga, chikondi cha Atate sichidzapitilira nanu, kotero mudzayenda mu mdima.

13 Tsopano nayi nzeru, ndi malingaliro a Ambuye—lolani nyumba imangidwe, osati potsatira njira ya dziko, pakuti ine sindidapereke kwa inu kuti mukhale potengera njira za dziko;

14 Kotero, lolani iyo imangidwe potsatira njira imene ine ndidzaonetsera kwa atatu mwa inu, amene mudzawasankhe ndi kuwadzodza ku mphamvu imeneyi.

15 Ndipo kukula kwake kudzakhala kutalika kwa mapazi makumi asanu ndi asanu mu lifupi, ndipo ikhale mapazi asanu ndi limodzi mphambu zisanu mu litali, mu mkati mwa bwalo lake.

16 Ndipo lolani mbali ya m’musi mwa bwalo la mkati mupatulidwe kwa ine poperekera mgonero ndi pa ulaliki wanu, ndi kusala kwanu, ndi kupemphera kwanu, ndi zopereka zokhumba zanu zoyera kwa ine, atero Ambuye wanu.

17 Ndipo lolani mbali yapamwamba pa bwalo la mkati mupatulidwe kwa ine pa sukulu ya atumwi anga, atero Mwana Ahmani; kapena, mu mawu ena, Alufasi; kapena, mu mawu ena, Omegasi, ngakhale Yesu Khristu ambuye wanu. Ameni.