Gawo 75
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Amherst, Ohio, Januwale 25, 1832. Gawoli lili ndi mavumbulutso awiri osiyana (loyamba mu ndime 1 mpaka 22 ndi lachiwiri mu ndime 23 mpaka 36) loperekedwa mu tsiku lomwelo. Chochitikacho chidali msonkhano umene Joseph Smith adachirikizidwa ndi kudzodzedwa kukhala Mtsogoleri wa Unsembe Waukulu. Akulu ena adafuna kudziwa zambiri ponena za ntchito zawo zanthawi yomweyo. Mavumbulutso awa adatsatira.
1–5, Akulu okhulupirika amene amalalikira uthenga wabwino adzapeza moyo wosatha; 6–12, Pempherani kuti mulandire Mtonthozi, amene amaphunzitsa zinthu zonse; 13–22, Akulu adzakhala mu chiweruzo pa iwo amene akana uthenga wawo; 23–36, Mabanja a atumiki akuyenera kulandira thandizo kuchokera ku Mpingo.
1 Indetu, indetu, ndikunena kwa inu, ine amene ndikuyankhula ngakhale ndi mawu a Mzimu wanga, ngakhale Alefa ndi Omega, Ambuye wanu ndi Mulungu wanu—
2Â Mvetserani, O inu amene mwapereka maina anu kuti mupite kukalalikira uthenga wanga wabwino, ndi kukadulira munda wanga wampesa.
3 Taonani, ndikunena kwa inu kuti ndi chifuniro changa kuti inu mupite chitsogolo ndipo musachedwe, kapena kukhala aulesi koma kugwira ntchito ndi mphamvu zanu—
4Â Kukweza mawu anu ngati kulira kwa lipenga, kulengeza choonadi molingana ndi mavumbulutso ndi malamulo amene ine ndakupatsani inu.
5Â Ndipo kotero, ngati muli okhulupirika mudzalemedwa ndi mitolo yambiri, ndi kuvekedwa korona wa ulemu, ndi ulemelero, ndi chisavundi, ndi moyo wamuyaya.
6 Kotero, indetu ndikunena kwa mtumiki wanga William E. McLellin, ndikuchotsa ntchito yomwe ndidamupatsa kuti apite kumayiko akum’mawa;
7 Ndipo ndikupereka kwa iye ntchito yatsopano ndi lamulo latsopano, m’mene ine, Ambuye, ndimulanga iye chifukwa cha kung’ung’udza kwa mtima wake;
8 Ndipo adachimwa; komabe, ndimukhululukira, ndikunena kwa iye kachiwiri, Pita ku mayiko a kum’mwera.
9 Ndipo lolani mtumiki wanga Luke Johnson apite naye, ndipo akalalikire zinthu zimene ndidawalamulira iwo—
10 Kuitanira pa dzina la Ambuye kwa Mtonthozi, amene adzawaphunzitsa zinthu zonse zimene zili zofunika kwa iwo—
11Â Kupemphera nthawi zonse kuti asafooke; ndipo pamene iwo achita ichi, ine ndidzakhala nawo ngakhale kufikira chimaliziro.
12Â Taonani, ichi ndi chifuniro cha Ambuye Mulungu wanu pa zokhudzana ndi inu. Ngakhale choncho. Ameni.
13 Ndiponso, indetu akutero Ambuye, lolani mtumiki wanga Orson Hyde ndi mtumiki wanga Samuel H. Smith ayambe ulendo wawo ku mayiko akum’mawa, ndipo alalikire zinthu zimene ine ndidawalamula iwo; ndipo pamene ali okhulupirika, taonani, ine ndidzakhala nawo ngakhale kufikira chimaliziro.
14 Ndiponso, indetu ndinena kwa mtumiki wanga Lyman Johnson, ndi kwa mtumiki wanga Orson Pratt, iwonso adzayamba ulendo wawo kulowa m’maiko akum’mawa; ndipo taonani, ndipo onani, ine ndili nawonso, ngakhale kufikira chimaliziro.
15Â Ndiponso, ndikunena kwa mtumiki wanga Asa Dodds, ndi kwa mtumiki wanga Calves Wilson, kuti iwonso adzayamba ulendo wawo kupita ku maiko a kumadzulo, ndi kulengeza uthenga wanga wabwino, inde monga ndidawalamulira iwo.
16Â Ndipo iye amene ali wokhulupirika adzagonjetsa zinthu zonse, ndipo adzakwezedwa patsiku lotsiriza.
17 Ndiponso, ndikunena kwa mtumiki wanga Major N. Ashley, ndi mtumiki wanga Burr Riggs, aloleni iwo ayambe ulendo wawonso ku dziko la kum’mwera.
18Â Inde, aloleni onsewo apite, monga ndidawalamula iwo, apite kunyumba ndi nyumba, ndi mudzi ndi mudzi, ndi mzinda ndi mzinda.
19 Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowamo, ndipo adzalandira inu, siyani mdalitso wanu pa nyumbayo.
20 Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowamo, ndipo iwo sakulandirani inu, mudzachoka msanga m’nyumbayo, ndi kusasa fumbi la kumapazi anu ngati umboni wotsutsana nawo.
21Â Ndipo mudzadzazidwa ndi chimwemwe ndi chikondwelero; ndipo dziwani ichi, kuti tsiku la chiweruzo mudzakhala oweruza a nyumbayo, ndi kuwaweruza;
22 Ndipo kudzakhala kopilirika kwa achikunja pa tsiku la chiweruzo, koposa nyumbayo; kotero, dzimangeni lamba m’chiuno mwanu ndipo khalani okhulupirika, ndipo mudzagonjetsa zinthu zonse, ndi kukwezedwa m’mwamba patsiku lotsiriza. Ngakhale choncho. Ameni.
23 Ndiponso, akutero Ambuye kwa inu, O inu akulu a mpingo wanga, amene mwapereka maina anu kuti mukathe kudziwa chifuniro chake chokhudzana ndi inu—
24Â Taonani, ndinena kwa inu, kuti ndi ntchito ya mpingo kuthandiza pothandizira mabanja a iwo, ndiponso kuthandiza mabanja a iwo amene aitanidwa ndipo akuyenera kutumizidwa ku dziko kuti akalengeze uthenga wabwino ku dziko lapansi.
25Â Kotero, ine, Ambuye, ndikupereka kwa inu lamulo ili, kuti mupeze malo a mabanja anu, pamene abale anu ali ofunitsitsa kutsegula mitima yawo.
26 Ndipo mulole onse otere amene angathe kupeza malo a mabanja awo, ndi chithandizo cha mpingo kwa iwo, asalephere kupita ku dziko, kaya kum’mawa kapena kumadzulo, kapena kumpoto, kapena kum’mwera.
27Â Aloleni iwo apemphe ndipo adzalandira, agogode ndipo chidzatsegulidwa kwa iwo, ndi kudziwitsidwa kuchokera kumwamba, ngakhale ndi Mtonthozi, kumene iwo adzapita.
28Â Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, kuti munthu aliyense amene akuyenera kusamalira banja lake la iye yekha, muloleni adzisamalira, ndipo munjira iliyonse iye sadzataya korona wake; ndipo muloleni agwire ntchito mu Mpingo.
29Â Aliyense akhale wakhama mu zinthu zonse. Ndipo mulesi sadzakhala ndi malo mu mpingo, pokhapokha iye atalapa ndi kukonza njira zake.
30Â Kotero, lolani mtumiki wanga Simeon Carter ndi mtumiki wanga Emer Harris akhale ogwirizana mu utumiki;
31 Ndiponso mtumiki wanga Ezra Thayre ndi mtumiki wanga Thomas B. Marsh;
32Â Ndiponso mtumiki wanga Hyrum Smith ndi mtumiki wanga Reynolds Cahoon;
33Â Ndiponso mtumiki wanga Daniel Stanton ndi mtumiki wanga Seymour Brunson;
34Â Ndiponso mtumiki wanga Sylvester Smith ndi mtumiki wanga Gideon Carter;
35Â Ndiponso mtumiki wanga Ruggles Eames ndi mtumiki wanga Stephen Burnett;
36 Ndiponso mtumiki wanga Micah B. Welton ndiponso mtumiki wanga Eden Smith. Ngakhale choncho. Ameni.