Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 7


Gawo 7

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Oliver Cowdery, ku Harmony, Pennsylvania, Epulo 1829, pamene iwo adafunsa kudzera mu Urimu ndi Tumimu ngati Yohane, ophunzira wokondedwa, adakali moyo kapena adamwalira. Vumbulutsoli ndi gawo lomasuliridwa ku zolemba zopangidwa pa chikopa ndi Yohane ndipo zidabisidwa ndi iyemwini.

1–3, Yohane Wokondedwa adzakhalabe kufikira Ambuye atabwera; 4–8, Petulo, Yakobo, ndi Yohane ali ndi mafungulo a uthenga wabwino.

1 Ndipo Ambuye adati kwa ine: Yohane, wokondedwa wanga, iwe ukukhumba chiyani? Pakuti ngati iwe udzapempha chimene ufuna, chidzapatsidwa kwa iwe.

2 Ndipo ine ndidati kwa iye: Ambuye, perekani kwa ine mphamvu pa imfa, kuti ndikakhale moyo ndi kubweretsa miyoyo kwa inu.

3 Ndipo Ambuye adati kwa ine: Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, chifukwa iwe wakhumba ichi iwe udzakhalabe kufikira ine nditabwera mu ulemelero wanga, ndipo iwe udzanenera pamaso pa maiko, mitundu, malilime ndi anthu.

4 Ndipo pachifukwa ichi Ambuye adati kwa Petulo: ngati nditafuna kuti iye akhalebe kufikira ine nditabwera, ndi chiyani ichi kwa iwe? Pakuti iye adakhumba kwa ine kuti akathe kubweretsa miyoyo kwa ine, koma iwe wakhumba kuti uthe kubwera mwachangu kwa ine mu ufumu wanga.

5 Ndikunena kwa iwe, Petulo, ili ndi khumbo labwino; koma wokondedwa wanga wakhumba kuti achitebe zambiri, kapena agwirebe ntchito yaikulu pakati pa anthu koposa zomwe iye wachita kale.

6 Inde, iye wayamba ntchito yaikulu; kotero ndidzamupanga iye ngati moto wamalawi ndi mngelo wotumikira; iye adzatumikira kwa iwo amene adzakhale olandira chipulumutso amene amakhala pa dziko lapansi.

7 Ndipo ndidzakupanga iwe mtumiki wa iye ndi wa m’bale wako Yakobo; ndipo kwa inu atatu ndidzapereka mphamvu izi, ndi mafungulo a utumiki uwu kufikira nditabwera.

8 Indetu ndinena ndi inu, nonsenu mudzakhala molingana ndi zokhumba zanu, pakuti inu nonse mukondwera mu chimene mwakhumbiracho.