Gawo 110
Masomphenya oonetseredwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Oliver Cowdery mu kachisi ku Kirtland, Ohio, Epulo 3, 1836. Chochitikacho chidali cha msonkhano wa tsiku la Sabata pa Lamulungu la Isitala. Mbiri ya Joseph Smith imati: “Mu masana, ndidathandiza Atsogoleri ena mu kuperekera Mgonero wa Ambuye ku Mpingo, kuulandira kuchokera kwa khumi ndi Awiri, amene mwayi wawo udali wotumikira pa gome lopatulika tsiku limeneli. Nditamaliza kuchita utumiki umenewu kwa abale anga, ndidabwelera ku guwa, nsalu yotchinga yamukachisi ikugwetsedwa, ndipo ndidawerama, ndi Oliver Cowdery, mu pemphero laulemu ndi lachete. Titadzuka mupemphero, masomphenya otsatirawa adatsegulidwa kwa tonsefe.”
1–10, Ambuye Yehova aonekera mu ulemelero ndi kuvomeleza Kachisi wa Kirtland ngati nyumba Yake; 11–12, Mose ndi Eliya aliyense aonekera ndi kupereka mafungulo awo ndi nyengo; 13–16, Eliya abwelera ndikupereka mafungulo a nyengo yake monga adalonjezedwa ndi Malaki.
1 Chophimbacho chidachotsedwa m’malingaliro mwathu, ndipo maso a kumvetsetsa kwathu adatsegulidwa.
2 Ife tidawaona Ambuye ataima chapatsogolo pa guwa, patsogolo pathu; ndipo pansi pa mapazi ake padali zomangidwa zagolide weniweni, za mtundu wonyezimira.
3 Maso ake adali ngati lawi la moto; tsitsi la pamutu pake lidali loyera ngati matalala; nkhope yake idawala kuposa kuwala kwa dzuwa; ndipo mawu ake adali ngati mkokomo wa madzi aakulu, ngakhale mawu a Yehova, nati:
4 Ine ndine woyamba ndi wotsiriza; Ine ndine wamoyo, Ine ndine amene adaphedwa; Ine ndine Nkhoswe wanu kwa Atate.
5 Taonani, machimo anu akhululukidwa; ndinu oyera pamaso panga; kotero, kwezani mitu yanu ndi kusangalala.
6 Mitima ya abale anu ikondwere, ndipo mitima ya anthu anga onse ikondwere, amene, ndi mphamvu zawo, amangira dzina langa nyumba iyi.
7 Pakuti taonani, ndalandira nyumba iyi, ndipo dzina langa lidzakhala pano; ndipo ndidzadzionetsera kwa anthu anga mwachifundo mu nyumba muno.
8 Inde, ndidzaonekera kwa atumiki anga, ndi kuyankhula nawo ndi mawu anga, ngati anthu anga asunga malamulo anga, ndipo sadzaipitsa nyumba yopatulika iyi.
9 Inde mitima ya zikwi ndipo zikwi khumi idzakondwera kwakukulu mu zotsatira za madalitso amene adzatsanuliridwa, ndi mphatso imene atumiki anga apatsidwa m’nyumba muno.
10 Ndipo mbiri ya nyumba iyi idzafalikira ku mayiko akunja; ndipo ichi ndi chiyambi cha mdalitso umene udzatsanuliridwa pamitu ya anthu anga. Ngakhale choncho. Ameni.
11 Masomphenya awa atatsekedwa, kumwamba kudatsegulidwanso kwa ife; ndipo Mose adaonekera pamaso pathu, ndipo adapereka kwa ife mafungulo a kusonkhanitsa kwa Israeli kuchokera ku magawo anayi a dziko lapansi, ndi utsogoleri wa mafuko khumi ochokera ku dziko la kumpoto.
12 Zitatha izi, Eliya adaonekera, ndipo adapereka nyengo ya uthenga wabwino wa Abrahamu, ponena kuti mwa ife ndi mbewu yathu mibadwo yonse ya pambuyo pathu idzadalitsidwa.
13 Atatha masomphenya awa, masomphenya ena aakulu ndi aulemelero adatumphukira pa ife; pakuti Eliya mneneri, amene adatengedwa kupita kumwamba popanda kulawa imfa, adaima pamaso pathu, ndipo adati:
14 Taonani, nthawi yafika ndithu, imene idanenedwa ndi pakamwa pa Malaki—kuchitira umboni kuti iye [Eliya] akuyenera kutumizidwa, lisadadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye—
15 Kudzatembenuzira mitima ya atate kwa ana, ndi ana kwa atate, kuopa kuti dziko lonse lingakanthidwe ndi thembelero—
16 Kotero, mafungulo a nyengo iyi aperekedwa m’manja mwanu; ndipo mwa ichi mudzatha kudziwa kuti tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye lili pafupi, ngakhale pa makomo.