Gawo 99
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa John Murdock, Ogasiti 29, 1832, ku Hiram, Ohio. Kopitilira chaka, John Murdock adali akulalikira uthenga wabwino pamene ana ake—opanda mayi potsatira kumwalira kwa mkazi wake, Julia Clapp, mu Epulo 1831—ankakhala ndi mabanja ena ku Ohio.
1–8, John Murdock aitanidwa kukalengeza uthenga wabwino, ndipo iwo amene amulandira iye alandira Ambuye ndipo adzapeza chifundo.
1 Taonani, akutero Ambuye kwa mtumiki wanga John Murdock—iwe waitanidwa kuti upite ku maiko akum’mawa kuchokera nyumba ndi nyumba, kuchokera ku mudzi ndi mudzi, ndipo kuchokera ku mzinda ndi mzinda, kukalengeza uthenga wanga wabwino wosatha kwa okhala kumeneko, mkati mwa mazunzo ndi zoipa.
2 Ndipo amene akulandira iwe walandira ine; ndipo udzakhala ndi mphamvu yolengeza mawu anga mu maonetseredwe a Mzimu wanga Woyera.
3 Ndipo amene akulandira iwe ngati kamwana kakang’ono, alandira ufumu wanga; ndipo odala ndi iwo, pakuti adzapeza chifundo.
4 Ndipo amene akukana iwe adzakanidwa ndi Atate anga ndi nyumba yake; ndipo iwe udzatsuka mapazi ako mu malo obisika mu njira ngati umboni otsutsana nawo.
5 Ndipo taona, ndipo ona, ndikubwera msanga kudzaweruza, kudzatsimikizira onse za ntchito zawo zoipa zimene iwo achita motsutsana nane, monga kwalembedwa za ine mu mabuku ambiri.
6 Ndipo tsopano, indetu ndikunena kwa iwo, kuti sikofunikira kuti iwe upite kufikira ana ako atasamalidwa, ndi kutumizidwa mwachikondi kwa bishopu wa Ziyoni.
7 Ndipo patapita zaka zochepa, ngati iwe ukhumba kwa ine, iwe ungathe kupitanso ku dziko labwino, kukalandira cholowa chako;
8 Apo ayi iwe udzapitiriza kulengeza uthenga wanga wabwino kufikira iwe utatengedwa. Ameni.