Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 21


Gawo 21

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Fayette, New York, Epulo 6, 1830. Vumbulutso ili lidaperekedwa pokhazikitsa Mpingo, pa tsiku latchedwali, mnyumba ya Peter Whitmer Sr. Amuna asanu ndi mmodzi, omwe adali atabatizidwa kale, adachita nawo. Mwa chisankho chogwirizana anthuwa adaonetsa chikhumbo chawo ndi kutsimikiza mtima kukhazikitsa, molingana ndi lamulo la Mulungu (onani gawo 20). Iwo adasankhanso kuti avomereze ndi kuchirikiza Joseph Smith Jr. ndi Oliver Cowdery ngati atsogoleri a Mpingo. Ndi kusanjika kwa manja, Joseph pamenepo adadzodza Oliver kukhala mkulu wa Mpingo, ndipo Oliver chimodzimodzi adadzodza Joseph. Atatha kupereka m’gonero, Joseph ndi Oliver adaika manja pa otenga nawo mbali payekhapayekha popereka Mzimu Woyera ndi kutsimikizira aliyense ngati membala wa Mpingo.

1–3, Joseph Smith aitanidwa kukhala mulosi, womasulira, mneneri, mtumwi, ndi mkulu; 4–8, Mawu ake adzatsogolera cholinga cha Ziyoni; 9–12, Oyera mtima adzakhulupilira mawu ake pamene ayankhula kudzera mwa Mtonthozi.

1 Taonani, padzakhala zolemba zosungidwa pakati panu; ndipo m’menemo udzatchedwa mulosi, womasulira, mneneri, mtumwi wa Yesu Khristu, mkulu wa Mpingo, kudzera mwa chifuniro cha Mulungu Atate, ndi chisomo cha Ambuye wako Yesu Khristu;

2 Powuziridwa ndi Mzimu Woyera kuti akhazikitse maziko ake, ndi kuumangilira ku chikhulupiliro choyera kwambiri.

3 Mpingo umene udakonzedwa ndi kukhazikitsidwa m’chaka cha Ambuye wanu mazana khumi ndi asanu ndi atatu kudza makumi atatu, m’mwezi wachinayi, ndi pa tsiku lachisanu ndi chimodzi la mwezi umene ukutchedwa Apulo.

4 Kotero, kutanthauza mpingo, mudzimvetsera ku mawu ake onse ndi malamulo amene iye adzapereka kwa inu pamene iye walandira iwo, kuyenda mu chiyero chonse pamaso panga;

5 Pakuti mawu ake mudzalandira, monga ngati akuchokera mkamwa mwanga, mu chipiliro chonse ndi chikhulupiliro.

6 Pakuti pakuchita izi zipata za gahena sizidzapambana motsutsana ndi inu; inde, ndipo Ambuye Mulungu adzabalalitsa mphamvu zamdima pamaso panu, ndi kupangitsa kumwamba kugwedele chifukwa cha ubwino wanu, ndi ulemerero wa dzina lake.

7 Pakuti atero Ambuye Mulungu: Iyeyo ndamuuzira kuti akayendetse cholinga cha Ziyoni ndi mphamvu zazikulu pa zabwino, ndipo khama lake ndikudziwa, ndipo pemphero lake ndalimva.

8 Inde, kulira kwake kwa Ziyoni ndakuona, ndipo ndidzachititsa kuti asadzamulilirenso; pakutimasiku ake a chimwemwe afika ku chikhululukiro cha machimo ake, ndi maonetseredwe a madalitso anga pa ntchito zake.

9 Pakuti, taona, ndidzadalitsa onse amene akugwira ntchito m’munda wanga wa mpesa ndi dalitso lalikulu, ndipo adzakhulupilira m’mawu ake, amene amaperekedwa kwa iye kudzera mwa ine ndi Mtonthozi, amene amaonetsa kuti Yesu adapachikidwa ndi anthu ochimwa chifukwa cha machimo adziko lapansi,inde, kwa chikhululukiro cha machimo kwa mtima wolapa.

10 Kotero ndikofunikira kuti akuyenera kudzodzedwa ndi iwe, Oliver Cowdery mtumwi wanga;

11 Ili kukhala lamulo kwa iwe, kuti ndiwe mkulu pansi pa dzanja lake, inde kukhala woyamba kwa iwe, kuti ukathe kukhala mkulu wa mpingo uwu wa Khristu, wonyamula dzina langa—

12 Ndi mlaliki woyamba wa mpingo uwu ku mpingo, ndi pamaso pa dziko, inde, pamaso pa Amitundu; inde, ndi motero akutero Ambuye Mulungu, taonani, taonani! kwa Ayudanso. Ameni.