Gawo 94
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Mneneri Joseph Smith, ku Kirtland, Ohio, Ogasiti 2, 1833, kufotokoza kamangidwe ka Kirtland, siteki ya Ziyoni, ndi kusankha Hyrum Smith, Reynolds Cahoon, ndi Jared Carter ngati a bungwe la zomangamanga la Mpingo.
1–9, Ambuye apereka lamulo lokhudzana ndi kumangidwa kwa nyumba ya ntchito za atsogoleri; 10–12, Nyumba yosindikizira ikuyenera kumangidwa; 13–17, Zolowa zina ziperekedwa.
1Â Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, abwenzi anga, lamulo ndikupereka kwa inu, kuti mukayambe ntchito yoika ndi kukonzekera kuyamba ndi maziko a mzinda wa siteki ya Ziyoni, kuno ku dziko la Kirtland, kuyambira pa nyumba yanga.
2Â Ndipo taonani, ikuyenera kuchitidwa molingana ndi chitsanzo chimene ndapereka kwa inu.
3 Ndipo lolani mbali yoyamba yakum’mwera ipatulidwe kwa ine kuti pamangidwe nyumba ya utsogoleri, ya ntchito za utsogoleri, polandira mavumbulutso; ndi ya ntchito za utumiki wa utsogoleri, mu zinthu zonse zokhudzana ndi mpingo ndi ufumu.
4 Indetu ndikunena kwa inu, kuti idzamangidwe mu lifupi lake lotalika mapazi makumi asanu ndi asanu ndi makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu m’lifupi mwake ndi m’litali tali mwake, mubwalo la mkati mwake.
5 Ndipo kudzakhale bwalo la m’musi ndi bwalo la pamwamba, molingana ndi maonekedwe amene adzaperekedwe kwa inu pambuyo pake.
6Â Ndipo idzapatulidwa kwa Ambuye kuchokera ku maziko ake, molingana ndi dongosolo la unsembe, molingana ndi machitidwe amene adzaperekedwe kwa inu pambuyo pake.
7Â Ndipo idzapatulidwa yonse kwa Ambuye ku ntchito ya atsogoleri.
8 Ndipo simudzalola chodetsedwa chilichonse kubwera m’menemo; ndipo ulemelero wanga udzakhala kumeneko, ndi kupezeka kwanga kudzakhalako.
9Â Koma ngati kudzabwerako chodetsedwa chilichonse, ulemelero wanga sudzakhalako; ndi kupezeka kwanga sikudzabweramo.
10 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, mbali yachiwiri yakum’mwera idzapatulidwa kwa ine pa kumangidwa kwa nyumba kwa ine, ya ntchito zosindikizira zomasulira za malemba, ndi zinthu zonse zimene ndidzakulamulireni inu.
11 Ndipo idzakhala lifupi lake lotalika mapazi makumi asanu ndi asanu ndi makuni asanu ndi limodzi mphambu zisanu m’lifupi mwake, ndi m’litali mwake, mu bwalo la nkati; ndipo kudzakhala bwalo la m’musi ndi bwalo lapamwamba.
12Â Ndipo nyumba imeneyi idzapatulidwa yonse kwa Ambuye kuchokera ku maziko ake, pa ntchito yosindikiza, mu zinthu zonse zimene ine ndidzakulamulani inu, kukhala yoyera, yosadetsedwa, molingana ndi machitidwe a zinthu zonse monga zidzaperekedwe kwa inu.
13Â Ndipo pa malo achitatu mtumiki wanga Hyrum Smith adzalandire cholowa chake.
14 Ndipo pa malo oyamba ndi achiwiri akumpoto atumiki anga Reynolds Cahoon ndi Jared Carter adzalandirapo zolowa zawo—
15Â Kuti iwo agwire ntchito imene inde ndawasankhira iwo, kukhala bungwe lomanga nyumba zanga, molingana ndi lamulo, limene ine, Ambuye Mulungu, ndapereka kwa inu.
16Â Nyumba ziwiri zimenezi sizikuyenera kumangidwa kufikira nditapereka kwa inu lamulo lokhudza izo.
17Â Ndipo tsopano sindikupereka zina pa nthawi ino. Ameni.