Gawo 24
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Oliver Cowdery, ku Harmony, Pennsylvania, July 1830. Ngakhale kuti pasadathe miyezi inayi kuchokera pamene Mpingo udakhazikitsidwa, chizunzo chidakula kwambiri, ndipo atsogoleri amayenera kufunafuna chitetezo mwapadera. Mavumbulutso atatu otsatirawa adaperekedwa panthawiyi kuti awapatse nyonga, awalimbikitse, ndi kuwalangiza.
1–9, Joseph Smith ayitanidwa kuti amasulire, kulalikira, ndi kufotokozera malembo; 10–12, Oliver Cowdery ayitanidwa kukalalikira uthenga wabwino; 13–19, Lamulo liwululidwa mokhudzana ndi zozizwitsa, matembelero, kusasa fumbi la mapazi a munthu, ndi kupita wopanda chikwama cha ndalama kapena thumba la kamba.
1 Taona, waitanidwa ndi kusankhidwa kuti ulembe Buku la Mormoni, ndi ku utumiki wanga; ndipo ndakukweza iwe kutuluka ku masautso ako, ndi kukulangiza iwe, kuti udapulumutsidwa kwa adani ako onse, ndipo udapulumutsidwa ku mphamvu za Satana ndi ku mdima!
2 Komabe, sikuti ndiwe osakhululukidwa mu zolakwa zako; komabe, pita njira yako ndipo usachimwenso.
3 Kuza udindo wako; ndipo ukatha kufesa minda yako ndi kuisunga, pita mofulumira kwa mpingo umene uli mu Colesville, Fayette, ndi Manchester, ndipo iwo adzakuthandiza iwe; ndipo ndidzawadalitsa iwo onse muuzimu ndi kuthupi;
4 Koma ngati sakulandira, Ndidzawatumizira pa iwo matembelero m’malo mwa madalitso.
5 Ndipo iwe udzapitilira mu kuitanira pa Mulungu m’dzina langa, ndi kulemba zinthu zimene zidzapatsidwa kwa iwe ndi Mtonthozi, ndi kufotokozera malemba onse kwa mpingo.
6 Ndipo zidzapatsidwa kwa iwe nthawi yomweyo zimene udzayankhule ndi kulemba, ndipo adzazimva, kapena ndidzawatumizira matembelero m’malo mwa madalitso.
7 Pakuti udzapereka utumiki wako wonse mu Ziyoni; ndipo m’menemu udzakhala nayo mphamvu.
8 Khala opilira mu masautso, pakuti udzakhala nawo ambiri; koma apilire, pakuti taona, ine ndili ndi iwe, ngakhale kufikira ku chimaliziro cha masiku ako.
9 Ndipo mu ntchito zakuthupi iwe sudzakhala nazo mphamvu, pakuti awa si mayitanidwe ako. Samalira mayitanidwe ako ndipo udzakhala nako kuthekera kokulitsa udindo wako, ndi kufotokozera malemba onse, ndi kupitiriza mu kusanjika kwa manja ndi kutsimikizira mipingo.
10 Ndipo m’bale wako Oliver adzapitiriza kunyamula dzina langa pamaso pa dziko, ndiponso ku mpingo. Ndipo iye sadzaganiza kuti anganene zokwanira pa cholinga changa; ndipo taona, ine ndili ndi iye kufikira chimaliziro.
11 Mwa ine iye adzakhala nawo ulemelero, ndipo osati wa iye mwini, kaya mu kufowoka kapena mu mphamvu, kapena mu nsinga kapena mu ufulu;
12 Ndipo mu nthawi zonse, ndi pa malo onse, adzatsegula pakamwa pake ndi kulengeza uthenga wanga ngati ndi liwu la lipenga, onse usana ndi usiku. Ndipo ndidzampatsa iye mphamvu yosadziwika pakati pa anthu.
13 Musafune zozizwitsa, pokhapokha ne nditadzakulamulani inu, pokhapokha kutulutsa ziwanda, kuchiritsa odwala, ndi kutsutsana ndi njoka za chiphe, ndi kutsutsana ndi ziphe zakupha;
14 Ndipo zinthu izi inu simudzachita, kupatula ngati izo zikufunidwa kwa inu mwa iwo amene akufuna izo, kuti malembo akathe kukwaniritsidwa; pakuti mudzachita molingana ndi izo zimene zalembedwa.
15 Ndipo m’malo aliwonse inu mudzalowa, ndipo iwo sadzakulandirani inu m’dzina langa, inu mudzasiya thembelero m’malo mwa dalitso, pa kusasa fumbi la mapazi anu motsutsa iwo monga umboni, ndi kuyeretsa mapazi anu m’mbali mwa njira.
16 Ndipo zidzachitika kuti aliyense amene adzaika manja ake pa inu mwa ndewu, inu mudzalamula kuti akanthidwe mu dzina langa; ndipo, taonani, ndidzawakantha monga mwa mawu anu, mu nthawi yanga yoikika.
17 Ndipo aliyense amene adzapita nawe kumulandu adzakhala wotembeleredwa ndi lamulo.
18 Ndipo musadzatenge thumba la ndalama, kapena thumba la kamba, kapena ndodo; kapena malaya awiri; pakuti Mpingo udzakupatsani inu mu ola lomwelo chimene mudzasowa,chakudya ndi chobvala, ndi nsapato, ndi ndalama, ndi thumba.
19 Pakuti mwaitaniwa kuti mudulilire munda wanga wa mpesa ndi kudulira kwakukulu, inde, ngakhale kwa nthawi yotsiriza; inde, ndiponso onse amene mudawadzodza, ndipo adzachita molingana ndi chitsanzo ichi. Ameni.