Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 112


Gawo 112

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Thomas B. Marsh, Mtsogoleri wa Gulu la Atumwi Khumi ndi Awiri, ku Kirtland, Ohio, Julaye 23, 1837. Panthawiyi padali kusagwirizana kwakukulu mu Mpingo pa utsogoleri wa Joseph Smith, kuphatikizapo ena mwa Atumwi. M’miyezi ingapo vumbulutsoli lisadaperekedwe, Thomas B. Marsh adayesetsa kuthetsa mkangano pakati pa atsogoleri a Mpingo ndikugwirizanitsa Atumwi.

1–10, Khumi ndi Awiriwo akuyenera kutumiza uthenga wabwino ndi kukweza mawu ochenjeza ku maiko onse ndi anthu; 11–15, Iwo akuyenera kunyamula mtanda wawo, kutsatira Yesu, ndi kudyetsa nkhosa Zake; 16–20, Iwo amene amalandira Atsogoleri Oyamba amalandira Ambuye; 21–29, Mdima uphimba dziko lapansi, ndipo okhawo amene amakhulupilira ndi kubatizidwa adzapulumutsidwa; 30–34, Atsogoleri Oyamba ndi Makumi ndi Awiri ali ndi mafungulo a nyengo ya chidzalo cha nthawi.

1 Indetu akutero Ambuye kwa iwe mtumiki wanga Thomas: Ndamva mapemphero ako; ndipo zachifundo zako zakwera monga chikumbutso pamaso panga, m’malo mwa iwo, abale ako, amene adasankhidwa kuchita umboni wa dzina langa ndi kulitumiza ilo pakati pa maiko onse, mafuko, manenedwe, ndi anthu, ndi kudzodzedwa kudzera mwa chida cha atumiki anga.

2 Indetu ndikunena kwa iwe, pakhala pali zinthu zina zochepa mu mtima mwako ndi iwe zimene ine, Ambuye, sindidakondwere nazo.

3 Komabe, chifukwa iwe wadzichepetsa wekha udzakwezedwa; kotero, machimo ako onse akhululukidwa kwa iwe.

4 Lola mtima wako ukondwere pamaso panga; ndipo udzachitira umboni za dzina langa, osati kwa Amitundu okha, komanso kwa Ayuda; ndipo udzatumiza mawu anga ku malekezero a dziko lapansi.

5 Tsutsa iwe, kotero, m’mawa ndi m’mawa; ndipo tsiku ndi tsiku lola liwu lako lochenjeza lipite patsogolo; ndipo usiku ukadzafika, usadzalole anthu a padziko lapansi awodzele, chifukwa chakuyankhula kwako.

6 Lola pokhala pako padziwike mu Ziyoni, ndipo usachotse nyumba yako; pakuti ine, Ambuye, ndili ndi ntchito yaikulu kwa iwe kuti uyichite, mu kufalitsa dzina langa pakati pa ana a anthu.

7 Kotero, dzimangilire m’chuuno mwako ku ntchitoyo. Lola mapazi akonso avale nsapato, pakuti wasankhidwa, ndipo njira yako ili pakati pa mapiri, ndi pakati pa mitundu yambiri ya anthu.

8 Ndipo kudzera mu mawu ako ambiri odzikuza adzatsitsidwa, ndipo kudzera mu mawu ako ambiri odzichepetsa adzakwezedwa.

9 Mawu ako adzakhala chidzudzulo kwa wolakwira; ndi pa kudzudzula kwako lilime la wosinjilira lileka chinyengo chake.

10 Khala odzichepetsa; ndipo Ambuye Mulungu wako adzakutsogolera iwe ndi dzanja, ndi kukupatsa yankho ku mapemphero ako.

11 Ndikudziwa mtima wako, ndipo ndamva mapemphero ako okhudzana ndi abale ako. Usakhale watsankho pa iwo mu chikondi choposa ambiri, koma chikondi chako chikhale kwa iwo monga cha iwe mwini; ndipo lola chikondi chako chisefukire kwa anthu onse, ndi kwa onse amene amakonda dzina langa.

12 Ndipo pemphelera abale ako a Khumi ndi Awiriwo. Uwachenjeze mwamphamvu chifukwa cha dzina langa, ndipo adzudzulidwe chifukwa cha machimo awo onse, ndipo khala okhulupirika pamaso panga ku dzina langa.

13 Ndipo pambuyo pa mayesero awo, ndi chisautso chachikulu, taona, ine, Ambuye, ndidzakhudzika, ndipo ngati iwo saumitsa mitima yawo, ndi kusaumitsa makosi awo motsutsana ndi ine, iwo adzatembenuka, ndipo ndidzawachiritsa iwo.

14 Tsopano, ndikunena kwa iwe, ndipo chimene ine ndikunena kwa iwe, ndikunena kwa onse Khumi ndi Awiriwo: Nyamuka ndipo udzimangilire lamba m’chiuno mwako, nyamula mtanda wako, nditsatireni ine, ndipo dyetsa nkhosa zanga.

15 Usadzikweze; usapandukire mtumiki wanga Joseph; pakuti indetu ndinena kwa iwe, ine ndili ndi iye, ndipo dzanja langa lidzakhala pa iye; ndipo mafungulo amene ndapereka kwa iye, ndiponso kwa iwe, sadzachotsedwa kwa iye kufikira ndidzabwera.

16 Indetu ndinena kwa iwe, mtumiki wanga Thomas, iwe ndiwe munthu amene ndamusankha kunyamula mafungulo a ufumu wanga, monga akukhudzana ndi Khumi ndi Awiriwo, kunja kwa maiko onse—

17 Kuti iwe ukathe kukhala mtumiki wanga kuti ukatsegulire chitseko cha ufumu m’malo onse kumene mtumiki wanga Joseph, ndi mtumiki wanga Sidney, ndi mtumiki wanga Hyrum, sangathe kubwera;

18 Pakuti pa iwo ndasenzetsa zolemetsa za mipingo yonse kwa kanthawi.

19 Kotero, kulikonse kumene adzakutumiza iwe, pita, ndipo ndidzakhala ndi iwe; ndipo kulikonse kumene udzalalikira dzina langa khomo lakuthekera lidzatsegulidwa kwa iwe, kuti iwo akathe kulandira mawu anga.

20 Pakuti aliyense amene amalandira mawu anga amandilandira ine, ndipo aliyense amene amandilandira ine, amalandira iwo, Atsogoleri Oyambawo, amene ine ndidawatuma, amene ndawapanga aphungu chifukwa cha dzina langa kwa iwe.

21 Ndiponso, ndikunena kwa iwe, kuti aliyense amene udzamutuma mu dzina langa, ndi liwu la abale ako, Khumi ndi Awiriwo, ovomerezedwa moyenelera ndi ololedwa ndi iwe, adzakhala ndi mphamvu yotsegulira khomo la ufumu wanga kwa mtundu uli wonse umene udzawatumize iwo—

22 Ngati iwo adzadzichepetsa pamaso panga, ndi kukhala m’mawu anga, ndi kumvetsera liwu la Mzimu wanga.

23 Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, mdima waphimba dziko lapansi, ndi mdima wandiweyani mmaganizo a anthu, ndipo matupi onse avunda pamaso panga.

24 Taona, kubwezera kudzafika msanga pa okhala pa dziko lapansi, tsiku la mkwiyo, tsiku lakupsya, tsiku la kupululutsa, la kulira, la maliro, ndi la chisoni; ndipo ngati kamvuluvulu lidzafika pamaso pa dziko lonse lapansi, atero Ambuye.

25 Ndipo pa nyumba yanga ilo lidzayamba, ndipo kuchokera kunyumba yanga ilo lidzatuluka, atero Ambuye;

26 Woyamba mwa iwo pakati panu, atero Ambuye, amene amadzinenera kuti amadziwa dzina langa, ndipo sadandidziwe ine, ndipo adandichitira mwano m’kati mwa nyumba yanga, atero Ambuye.

27 Kotero, ona kuti usadzivutitse wekha zokhudzana ndi zochitika za mpingo wanga m’malo ano, atero Ambuye.

28 Koma yeretsani mitima yanu pamaso panga; ndipo kenako pitani ku dziko lonse lapansi, ndipo lalikirani uthenga wanga wabwino kwa cholengedwa chilichonse chimene sichidaulandire;

29 Ndipo iye amene akakhulupilire ndi kubatizidwa adzapulumuka, ndipo iye amene sakakhulupilira, ndikusabatizidwa, adzaweruzidwa;

30 Pakuti kwa inu, Khumi ndi Awiri, ndi iwo, Atsogoleri Oyamba, amene asankhidwa ndi inu kuti akhale aphungu anu ndi atsogoleri anu, ndi mphamvu ya unsembe uwu woperekedwa, kwa masiku otsiriza ndi kwa nthawi yotsiriza, m’mene muli nyengo ya chidzalo cha nthawi,

31 Mphamvu yake muli nayo, mogwirizana ndi onse amene alandira nyengo pa nthawi iliyonse kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe;

32 Pakuti indetu ndikunena kwa inu, mafungulo a nyengo, imene mudalandira, adatsika kuchokera kwa makolo, ndipo potsiriza pa onse, adatsitsidwa kwa inu kuchokera kumwamba.

33 Indetu ndinena kwa inu, taonani kodi mayitanidwe anu ndi aakulu bwanji. Yeretsani mitima yanu ndi zovala zanu, kuopera kuti mwazi wa m’badwo uno ungafunidwe pa manja anu.

34 Khala okhulupirika kufikira ndidzabwere, pakuti ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndili nayo ya kubwenzera munthu aliyense molingana ndi ntchito yake itadzakhalire. Ndine Alefa ndi Omega. Ameni.