Gawo 113
Mayankho ku mafunso ena pazolemba za Yesaya, operekedwa ndi Joseph Smith Mneneri, pafupi ndi Far West, Missouri, Malitchi 1838.
1–6, Tsinde la Jese, ndodo yochokera pamenepo, ndi muzu wa Jese zidzadziwika; 7–10, Otsalira obalalitsidwa a Ziyoni ali ndi ufulu wa unsembe ndipo akuitanidwa kuti abwelere kwa Ambuye.
1Â Kodi tsinde la Jese likunenedwa mu ndime 1, 2, 3, 4 ndi 5 ya mutu 11 wa Yesaya ndi chiyani?
2Â Indetu akutero Ambuye: Ndi Khristu.
3Â Kodi ndodo ikunenedwa mu ndime yoyamba ya mutu 11 wa Yesaya, imene ikuyenera kudzachokera ku tsinde la Jese ndi chiyani?
4Â Taonani, akutero Ambuye: ndi mtumiki mu manja a Khristu, amene mbali ina ali mbadwa ya Jese komanso ya Efraimu, kapena wa nyumba ya Yosefe, amene mwa iye mwaikidwa mphamvu zambiri.
5Â Kodi muzu wa Jese wonenedwa mu ndime 10 ya Mutu 11 ndi chiyani?
6Â Taonani, akutero Ambuye, ndi mbadwa ya Jese, komanso ya Yosefe, kwa imene kuli koyenera unsembe, ndi mafungulo a ufumu, ngati mbendera, ndi pa kusonkhanitsa kwa anthu anga mu masiku otsiriza.
7 Mafunso a Elias Higbee: Kodi chikutanthauzanji za lamulo mu Yesaya, mutu 52, ndime 1, imene ikuti: Vala mphamvu zako, O Ziyoni—ndi anthu ati amene Yesaya adali kunena?
8Â Iye adafanizira kwa iwo amene Mulungu akuyenera kuwaitana mu masiku otsiriza, amene akuyenera kukhala ndi mphamvu ya unsembe yakubweretsanso Ziyoni, ndi chiwombolo cha Israeli; ndipo kuvala mphamvu yake ndi kuvala ulamuliro wa unsembe, umene iye, Ziyoni, ali ndi ufulu wake mwa umbadwa; komanso kubwelera ku mphamvu iyo imene iye adaitaya.
9Â Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za Ziyoni kudzimasula yekha ku maunyolo apakhosi lake; ndime 2?
10Â Tikuyenera kumvetsa kuti otsalira obalalitsidwa akulimbikitsidwa kubwelera kwa Ambuye kuchokera kumene iwo adagwera; zimene ngati angachite, lonjezo la Ambuye ndilakuti iye adzayankhula kwa iwo, kapena kuwapatsa iwo vumbulutso. Onani ndime 6, 7 ndi 8. Maunyolo apakhosi lake ndi matembelero a Mulungu pa iye, kapena otsalira a Israeli mu kubalalitsidwa kwawo pakati pa Amitundu.