Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 98


Gawo 98

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Ogasiti 6, 1833. Vumbulutso ili lidabwera motsatira mazunzo a Oyera mtima mu Missouri amene adali kukumana nawo Kuchulukana kwa mamembala mu Missiouri kudasokoneza anthu ena okhalako, amene adamva kuopsezedwa ndi chiwerengero cha Oyera mtima, ndale, ndi chikoka pazachuma, komanso kusiyana kwa chikhalidwe ndi chipembedzo. Pa Julayi 20, 1833, gulu lidawononga katundu wa Mpingo, kuthira phula ndi nthenga mamembala awiri a Mpingo, ndi kulamula kuti Oyera mtima achoke ku Dera la Jackson. Patatha masiku atatu, atsogoleri a Mpingo adasainira mgwirizano kuti atero. Ngakhale nkhani zina za mavuto ku Missouri zidali mosakaikitsa zitafika kwa Mneneri ku Kirtland (mtunda wautali kwambiri), kukula kwa zinthu kukadadziwika kwa iye pa tsiku limeneli kudzera mu vumbulutso lokha.

1–3. Masautso a Oyera mtima adzakhala pa ubwino wawo; 4–8, Oyera mtima akuyenera kuchita ubwenzi ndi lamulo lalikulu la dzikolo; 9–10, Oona mtima, anzeru, ndi anthu abwino akuyenera kuthandizidwa ku ulamuliro wa dziko; 11–15, Iwo amene ataya miyoyo yawo mu chifukwa cha Ambuye adzakhala ndi moyo wamuyaya; 16–18, Kanani nkhondo ndi kulengeza mtendere; 19–22, Oyera mtima ku Kirtland adzudzulidwa ndi kulamulidwa kuti alape; 23–32, Ambuye aulura malamulo Ake otsogolera za mazunzo ndi masautso ochitiridwa pa anthu Ake; 33–38, Nkhondo imalungamitsidwa pokhapokha pamene Ambuye ailamula; 39–48, Oyera mtima akuyenera kukhululukira adani awo, amene, ngati iwo alapa, adzathanso kubwenzera kwa Ambuye.

1 Indetu ndikunena kwa inu abwenzi anga, musaope, mitima yanu itonthole; inde, kondwerani nthawi zonse, ndipo muzonse yamikani;

2 Kuyembekezera modekha pa Ambuye, pakuti mapemphero anu alowa mu makutu a Ambuye wa Makamu, ndipo alembedwa ndi chisindikizo ndi chipangano ichi—Ambuye walumbira ndi kulengeza kuti iwo adzayankhidwa.

3 Kotero, iye amapereka lonjezo ili kwa inu, ndi pangano losasinthika kuti iwo adzakwaniritsidwa; ndipo zinthu zonse zimene inu mwasautsidwa nazo zidzagwira limodzi pa ubwino wanu, ndi ku ulemelero wa dzina langa, atero Ambuye.

4 Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa inu zokhudzana ndi malamulo a dziko, ndi chifuniro changa kuti anthu anga adzisunga kuchita zinthu zonse zimene ine ndawalamula.

5 Ndipo kuti lamulo la dziko limene ndi lalikulu, lothandizira mfundo yofunika ya ufulu mu kusunga maufulu ndi mwayi, ndi la anthu onse, ndipo ndi lolungamitsidwa pamaso panga.

6 Kotero, ine, Ambuye, ndakulungamitsani inu, ndi abale anu a mpingo, mu kukhala paubwezi ndi lamulo limenero limene lili lamulo loyendetsera dziko;

7 Ndipo monga zokhudza lamulo la munthu, chilichonse choposera kapena kuchepera pa ili, chimadza mwa woipayo.

8 Ine, Ambuye Mulungu, ndakumasulani, kotero ndinu afulu ndithu; ndipo lamulonso lakupangani inu afulu.

9 Komabe, pamene woipa alamulira, anthu amalira.

10 Kotero, anthu oona mtima ndi anzeru akuyenera kufunidwa mwakhama, ndipo anthu abwino ndi anthu anzeru mukuyenera kuwathandizira; apo ayi aliyense amene ali ochepera koposa izi amadza moipa.

11 Ndipo ndikupereka kwa inu lamulo, kuti musiye zoipa zonse ndi kukangamira ku zabwino zonse, kuti mukakhale mwa mawu aliwonse amene akuchokera mkamwa mwa Mulungu.

12 Pakuti iye adzapereka kwa okhulupilira mzere ndi mzere; langizo ndi langizo; ndipo ndidzakuyesani inu ndi kukutsimikizirani inu pano.

13 Ndipo aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha ine, chifukwa cha dzina langa, adzaupezanso, ngakhale moyo wamuyaya.

14 Kotero, musaope adani anu, pakuti ndalamula mu mtima mwanga, atero Ambuye, kuti ndidzatsimikizira inu zinthu zonse, ngati inu mudzakhale mu pangano langa, ngakhale mpaka imfa, kuti inu mukathe kupezeka oyenera.

15 Pakuti ngati inu simukhala mu pangano langa simuli oyenera ine.

16 Kotero, kanani nkhondo ndi kulengeza mtendere, ndi kufunafuna mwakhama kutembenuzira mitima ya ana a anthu kwa makolo awo, ndi mitima ya makolo kwa ana awo;

17 Ndiponso, mitima ya Ayuda kwa aneneri, ndi aneneri kwa Ayuda; kuopa ndingabwere ndi kukantha dziko lonse lapansi ndi tembelero, ndipo mnofu wonse kunyeka pamaso panga.

18 Mitima yanu isavutike; pakuti mu nyumba ya Atate anga muli nyumba zambiri, ndipo ine ndakonzera malo a inu; ndipo kumene Atate anga ndi ine ndili, kumeneko inunso mudzakhala.

19 Taonani, ine, Ambuye, sindikondwera ndi ambiri amene ali mu mpingo ku Kirtland;

20 Pakuti iwo sadasiye machimo awo, ndi njira zawo zoipa, kunyada kwa mitima yawo, ndi kusilira kwawo, ndi zinthu zawo zonse zonyansa, ndi kusunga mawu a nzeru ndi moyo wamuyaya umene ine ndapereka kwa iwo.

21 Indetu ndikunena kwa inu, kuti ine, Ambuye, ndidzalanga iwo ndi kuchita chilinchonse ndifuna, ngati iwo salapa ndi kusunga zinthu zonse zimene ine ndanena kwa iwo.

22 Ndiponso ndikunena kwa inu, ngati musunga kuchita chilichonse ndakulamulani inu, ine, Ambuye, ndidzatembenuza ukali wonse ndi mkwiyo kuchokera kwa inu, ndipo zipata za gahena sizidzapambana motsutsana nanu.

23 Tsopano, ndikunena kwa inu zokhudzana ndi mabanja anu—ngati anthu akukanthani inu, kapena mabanja anu, kamodzi, ndipo inu mwapilira moleza mtima ndi kusawachitira mwano, kapena kuwabwenzera, inu mudzalandira mphotho;

24 Koma ngati inu simupilira moleza mtima, zidzawerengedwa kwa inu monga muyeso woyenelera kwa inu.

25 Ndiponso, ngati mdani wanu adzakukanthani kachiwiri, ndipo inu simudamuchitire mwano mdaniyo, ndipo mwapilira moleza mtima, mphotho yanu idzakhala yochuluka mazanamazana.

26 Ndiponso, ngati iye akukanthani inu kachitatu, ndipo inu mwapilira moleza mtima, mphotho yanu idzawonjezeredwa kwa inu kochulukira kanayi;

27 Ndipo maumboni atatu amenewa adzaima motsutsana ndi mdani wanu ngati iye salapa, ndipo sadzakhululukidwa.

28 Ndipo tsopano, indetu ndikunena kwa inu, ngati mdani wanu adzathawa kubwenzera kwanga, kuti iye asabweretsedwe kuchiweruzo pamaso panga, kenako mudzaonetsetse kuti inu mwamuchenjeza iye mu dzina langa, kuti iye asabwerenso pa inu, kapena pa banja lanu, ngakhale kwa ana a ana anu kufikira m’badwo wachitatu ndi wachinayi.

29 Ndipo kenako, ngati iye adzabwera pa inu kapena ana anu, kapena ana a ana anu kufikira m’badwo wachitatu ndi wachinayi, ndapereka m’dani wanuyo m’manja mwanu;

30 Ndipo kenako ngati inu mudzamusiya iye, mudzalandira mphotho ya chilungamo chanu; ndiponso ana anu ndi ana a ana anu kufikira m’badwo wachitatu ndi wachinayi.

31 Komabe, mdani wanuyo ali m’manja mwanu; ndipo ngati inu mumchitira iye molingana ndi ntchito zake inu mwalungamitsidwa; ndipo ngati iye afuna moyo wanu, ndipo moyo wanu uli pa chiopsezo ndi iye, mdani wanuyo ali m’manja mwanu ndipo inu mwalungamitsidwa.

32 Taonani, ili ndi lamulo limene ndidapereka kwa mtumiki wanga Nefi, ndi makolo anu, Yosefe, ndi Yakobo, ndi Isaki, ndi Abrahamu, ndi aneneri anga onse akale ndi atumwi.

33 Ndiponso, ili ndi lamulo limene ine ndidapereka kwa akale anga, kuti iwo asapite ku nkhondo motsutsana ndi dziko lonse, fuko, lilime, kapena anthu, kupatula ine, Ambuye nditawalamula iwo.

34 Ndipo ngati dziko, lilime, kapena anthu angalengeze nkhondo motsutsana nawo, akuyenera choyamba kuimika mbendera ya mtendere kwa anthu amenewo, dziko, kapena lilime;

35 Ndipo ngati anthuwo sadavomeleze chopereka cha mtenderecho, ngakhale kachiwiri kapena nthawi yachitatu, iwo akuyenera kubweretsa maumboni amenewa pamaso pa Ambuye;

36 Kenako, ine, Ambuye, ndidzapereka kwa iwo lamulo, ndi kulungamitsa iwo pakupita ku nkhondo motsutsana ndi dziko limenelo, lilime, kapena anthu.

37 Ndipo ine, Ambuye, ndidzawamenyera nkhondo zawo, ndi nkhondo za ana awo, ndi nkhondo za ana a ana awo, kufikira iwo atabwenzera okha pa adani awo onse, kufikira m’badwo wachitatu ndi wachinayi.

38 Taonani, ichi ndi chitsanzo kwa anthu onse, atero Ambuye Mulungu wanu, cha chilungamitso pamaso panga.

39 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, ngati atatha adani anu kubwera pa inu koyamba, iye walapa ndi kubwera kwa inu kupempha chikhululukiro, inu mudzamukhululukira iye, ndipo simudzamuimikanso ngati umboni motsutsana ndi mdani wanu—

40 Ndipo moteromo kufikira nthawi yachiwiri ndi yachitatu; ndipo mowirikiza momwe mdani wanu walapa pa kulakwitsa kumene iye wakulakwirani inu, mudzamukhululukira iye, kufikira makumi asanu ndi awiri kuwirikiza kasanu ndi kawiri.

41 Ndipo ngati iye wakulakwirani inu ndipo sadalape kunthawi yoyamba, komabe inu mudzamukhululukira iye.

42 Ndipo ngati iye wakulakwirani kwa nthawi yachiwiri, ndipo sadalape, komabe inu mudzamukhululukira iye.

43 Ndipo ngati iye wakulakwirani kwa nthawi yachitatu, ndipo sadalape, inu mudzamukhululukiranso iye.

44 Koma ngati akulakwirani kwanthawi yachinayi inu simudzamukhululukira iye, koma mudzabweretsa maumboni amenewa pamaso pa Ambuye; ndipo sadzakhululukidwa kufikira iye atalapa ndi kukulipirani inu kochuluka kanayi mu zinthu zonse zimene iye adakulakwirani inu.

45 Ndipo ngati iye achita ichi, inu mudzamukhululukira iye ndi mtima wanu wonse; ndipo ngati inu muchita ichi, ine, Ambuye, ndidzabwenzera adani anu kochuluka mazanamazana;

46 Ndi pa ana ake, ndi pa ana a ana ake a onse amene amadana nane, kufikira m’badwo wachitatu ndi wachinayi.

47 Koma ngati anawo alapa, kapena ana a ana ndi kutembenukira kwa Ambuye Mulungu wawo, ndi mitima yawo yonse, ndi mphamvu zawo zonse, ndi malingaliro ndi nyonga, ndi ku bwenzeretsa kochuluka kanayi ka zolakwa zawo zonse zimene iwo adalakwira, kapena zimene makolo awo adalakwira, kapena makolo a makolo awo, kenako mkwiyo wanu udzatembenukira kutali;

48 Ndipo kubwenzera sikudzabweranso pa iwo, atero Ambuye Mulungu wanu, ndipo zolakwa zawo sizidzabweretsedwanso ngati umboni pamaso pa Ambuye motsutsana nawo. Ameni.