Gawo 15
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri kwa John Whitmer, ku Fayette, New York, Juni 1829 (onani mutu wa gawoĀ 14). Uthengawu ndi wapamtima ndi opatsa chidwi waumwini mwakuti Ambuye akunena zodziwika kwa John Whitmer yekha ndi Iye mwini. David Whitmer pambuyo pake adakhala māmodzi mwa Mboni Zisanu ndi Zitatu za Buku la Mormoni.
1ā2, Mkono wa Ambuye uli pa dziko lonse lapansi; 3ā6, Kulalikira uthenga wabwino ndi kupulumutsa miyoyo ndi chinthu chofunika kwambiri.
1 Mvetsera, mtumiki wanga John, ndipo mvera ku mawu a Yesu Khristu, Ambuye wako ndi Muwomboli wako.
2 Pakuti taona, ndikuyankhula kwa iwe mwa kuthwa ndi mwa mphamvu, pakuti mkono wanga uli pa dziko lonse lapansi.
3 Ndipo ndidzakuuza iwe chimene palibe munthu amadziwa kupatula ine ndi iwe wekhaā
4 Pakuti nthawi zambiri iwe udafuna kwa ine kuti udziwe chimene chingakhale chofunikira kwambiri kwa iwe.
5 Taona, ndiwe wodala chifukwa cha chinthu ichi, ndi pakuyankhula mawu anga amene ndikupatsa iwe molingana ndi malamulo anga.
6 Ndipo tsopano, taona, ndinena kwa iwe, kuti chinthu chimene chidzakhale chofunikira kwambiri kwa iwe chidzakhala kulengeza kulapa kwa anthu awa, kuti ukathe kubweretsa miyoyo kwa ine, kuti ukathe kupumula nawo mu ufumu wa Atate anga. Ameni.