Gawo 55
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa William W. Phelps, ku Kirtland, Ohio, Juni 14, 1831 William W. Phelps, otsindikiza, ndi banja lake adangofika kumene ku Kirtland, ndipo Mneneri adafunsa Ambuye mbiri yokhudza iye.
1–3, William W. Phelps waitanidwa ndi kusankhidwa kuti abatizidwe, ndi kudzodzedwa kukhala mkulu, ndi kukalalikira uthenga wabwino; 4, Iye akuyeneranso kulemba mabuku a ana amu sukulu za Mpingo; 5–6, Iye akuyenera kupita ku Missouri, kumene kudzakhale dera la ntchito zake.
1 Taona, akutero Ambuye kw iwe, mtumiki wanga William, inde, ngakhale Ambuye wa dziko lonse lapansi, iwe waitanidwa ndi kusankhidwa; ndipo pambuyo pa kubatizidwa kwako ndi madzi, zimene ngati ungachite ndi diso limodzi ku ulemelero wanga, udzakhala ndi chikhululukiro cha machimo ako ndi kulandira kwa Mzimu Woyera mwa kusanjikidwa manja;
2 Ndipo kenano iwo udzadzodzedwa ndi dzanja la mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., kukhala mkulu kwa mpingo uwu, kukalalikira kulapa ndi chikhululukiro cha machimo mwa njira ya ubatizo mu dzina la Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu wa moyo.
3 Ndipo pa wina aliyense amene iwe udzasanjika manja, ngati iwo ali wolapa pamaso panga, udzakhala ndi mphamvu yakupereka Mzimu Woyera.
4 Ndiponso, udzadzodzedwa kukhala wothandizira mtumiki wanga Oliver Cowdery kugwira ntchito yosindikiza, ndi yakusankha ndi ndikulemba mabuku a masukulu a mpingo uwu, kuti ana aang’ono athenso kulandira malangizo pamaso panga monga zili zokondweretsa kwa ine.
5 Ndiponso, indetu ndikunena kwa iwe, pachifukwa ichi iwe uyambe ulendo wako ndi mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon, kuti ukathe kudzalidwa mu dziko la cholowa chako kukachita ntchito iyi.
6 Ndiponso, lolani mtumiki wanga Joseph Coe nayenso ayambe ulendo wake ndi iwo. Zotsalirazo zidzadziwitsidwa pambuyo pake, ngakhale momwe ndifunira. Ameni.