Gawo 114
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Far West, Missouri, Epulo 11, 1838.
1–2, maudindo a Mpingo amene adali ndi iwo amene ndi osakhulupirika adzaperekedwa kwa ena.
1 Indetu akutero Ambuye: Ndi chanzeru mwa mtumiki wanga David W. Patten, kuti iye alongosole za malonda ake onse mwachangu m’mene angathere, ndi kugulitsa malonda ake, kuti iye achite utumiki kwa ine masiku akudzawa, mothandizana ndi ena, ngakhale khumi ndi awiri kuphatikizirapo iyemwini, kukachitira umboni wa dzina langa ndi kunyamula uthenga wachimwemwe ku dziko lonse lapansi.
2 Pakuti indetu akutero Ambuye, kuti pamene pali iwo pakati panu amene akukana dzina langa, ena adzabyalidwapo m’malo mwawo ndi kulandira ubishopu wawo. Ameni.